Salimo 95:1-11

  • Kulambira koona komanso kumvera

    • “Lero anthu inu mukamvera mawu ake” (7)

    • “Musaumitse mitima yanu” (8)

    • “Sadzalowa mumpumulo wanga” (11)

95  Bwerani, tiyeni tifuule kwa Yehova mosangalala! Tiyeni tifuule mosangalala ndipo titamande Thanthwe la chipulumutso chathu.+  2  Tiyeni tikaonekere pamaso pake moyamikira.+Tiyeni timuimbire nyimbo zomutamanda ndipo tifuule mosangalala.  3  Chifukwa Yehova ndi Mulungu wamkulu,Iye ndi Mfumu yaikulu kuposa milungu ina yonse.+  4  Malo ozama kwambiri a dziko lapansi ali mʼmanja mwake,Mapiri aatali nawonso ndi ake.+  5  Nyanja imene iye anapanga ndi yake,+Ndipo manja ake anapanganso mtunda.+  6  Bwerani, tiyeni timulambire komanso kumugwadira.Tiyeni tigwade pamaso pa Yehova amene anatipanga.+  7  Chifukwa iye ndi Mulungu wathuNdipo ife ndi anthu amene iye akuweta,Nkhosa zimene akuzisamalira.*+ Lero anthu inu mukamvera mawu ake,+  8  Musaumitse mitima yanu ngati mmene makolo anu anachitira ku Meriba,*+Ngati mmene anachitira ku Masa* mʼchipululu,+  9  Pamene makolo anu anandiyesa.+Iwo anatsutsana ndi ine ngakhale kuti anaona ntchito zanga.+ 10  Kwa zaka 40, mʼbadwo umenewo unkandinyansa ndipo ndinati: “Awa ndi anthu amene mitima yawo imasochera nthawi zonse,Njira zanga sakuzidziwa.” 11  Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti: “Sadzalowa mumpumulo wanga.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “zimene zili mʼmanja mwake.”
Kutanthauza, “Kukangana.”
Kutanthauza, “Kuyesa; Mayesero.”