Salimo 96:1-13

  • “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano”

    • Yehova ndi woyenera kutamandidwa kwambiri (4)

    • Milungu ya anthu a mitundu ina ndi yopanda pake (5)

    • Lambirani Mulungu mutavala zovala zokongola komanso zopatulika (9)

96  Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+ Dziko lonse lapansi liimbire Yehova.+  2  Imbirani Yehova, tamandani dzina lake. Tsiku ndi tsiku muzilengeza uthenga wabwino wa chipulumutso chake.+  3  Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,Lengezani ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+  4  Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri. Iye ndi wochititsa mantha kwambiri kuposa milungu ina yonse.  5  Milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+Koma Yehova ndi amene anapanga kumwamba.+  6  Pamene amakhala pali ulemu ndi ulemerero.+Mphamvu ndi kukongola zili mʼnyumba yake yopatulika.+  7  Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu mabanja a mitundu ya anthu,Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.+  8  Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+Bweretsani mphatso ndi kulowa mʼmabwalo ake.  9  Gwadirani* Yehova mutavala zovala zokongola komanso zopatulika.*Dziko lonse lapansi linjenjemere pamaso pake. 10  Lengezani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: “Yehova wakhala Mfumu.+ Dziko lapansi lakhazikika moti silingasunthidwe.* Iye adzaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo.”*+ 11  Kumwamba kukondwere ndipo dziko lapansi lisangalale.Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo.+ 12  Mtunda ndi zonse zimene zili pamenepo zikondwere.+ Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo yonse yamʼnkhalango ifuule mosangalala+ 13  Pamaso pa Yehova, chifukwa iye akubwera,*Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo+Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Lambirani.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake.”
Kapena kuti, “moti silingagwedezeke.”
Kapena kuti, “Iye adzateteza anthu pa mlandu wawo mwachilungamo.”
Kapena kuti, “wabwera.”