Salimo 98:1-9
-
Yehova ndi Mpulumutsi komanso Woweruza wolungama
-
Chipulumutso cha Yehova chadziwika (2, 3)
-
Nyimbo.
98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+Chifukwa wachita zinthu zodabwitsa.+
Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.*+
2 Yehova wachititsa kuti chipulumutso chake chidziwike.+Wachititsa kuti anthu a mitundu yonse aone chilungamo chake.+
3 Iye wakumbukira chikondi chake chokhulupirika komanso kukhulupirika kumene analonjeza nyumba ya Isiraeli.+
Anthu onse padziko lapansi aona mmene Mulungu wathu wapulumutsira anthu ake.*+
4 Dziko lonse lapansi lifuulire Yehova mosangalala chifukwa wapambana.
Kondwerani ndipo fuulani mosangalala komanso imbani nyimbo zomutamanda.+
5 Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze,Mutamandeni ndi nyimbo zosangalatsa pogwiritsa ntchito zeze.
6 Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova,Poimba malipenga komanso lipenga la nyanga ya nkhosa chifukwa wapambana.+
7 Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,Chimodzimodzinso dziko lapansi komanso amene akukhala mmenemo.
8 Mitsinje iwombe mʼmanja,Mapiri afuule pamodzi mosangalala+
9 Pamaso pa Yehova chifukwa iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
Adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo+Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “zamuchititsa kuti apambane.”
^ Kapena kuti, “aona kupambana kwa Mulungu wathu.”