Wolembedwa ndi Mateyu 17:1-27
17 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi mchimwene wake Yohane nʼkukwera nawo mʼphiri lalitali kwaokhaokha.+
2 Ndiyeno iwo anaona kuti wasintha maonekedwe ake. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo malaya ake akunja anawala* kwambiri.+
3 Kenako anaona Mose ndi Eliya akukambirana ndi Yesu.
4 Ndiye Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Ngati mukufuna, ndimanga matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.”
5 Mawu ake adakali mʼkamwa, mtambo wowala kwambiri unawaphimba ndipo panamveka mawu kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene amandisangalatsa kwambiri.+ Muzimumvera.”+
6 Ophunzirawo atamva zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi ndipo anachita mantha kwambiri.
7 Kenako Yesu anawayandikira ndipo anawagwira nʼkunena kuti: “Dzukani, musaope.”
8 Atayangʼana, anaona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha.
9 Akutsika mʼphirimo, Yesu anawalamula kuti: “Musauze wina aliyense za masomphenya amenewa mpaka Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”+
10 Koma ophunzirawo anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ayenera kubwera choyamba?”+
11 Iye anayankha kuti: “Inde, Eliya adzabweradi ndipo adzabwezeretsa zinthu zonse.+
12 Komabe, ine ndikukuuzani kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anamuchitira zilizonse zimene iwo anafuna.+ Iwo adzazunzanso Mwana wa munthu mwa njira imeneyi.”+
13 Atatero ophunzirawo anazindikira kuti akunena za Yohane Mʼbatizi.
14 Atafika kufupi ndi gulu la anthu,+ mwamuna wina anamuyandikira ndipo anamugwadira nʼkunena kuti:
15 “Ambuye, muchitire chifundo mwana wanga wamwamuna, chifukwa akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Nthawi zambiri amagwera pamoto ndiponso mʼmadzi.+
16 Ndinapita naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”
17 Yesu anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.”
18 Ndiyeno Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka. Nthawi yomweyo mnyamatayo anachira.+
19 Kenako ophunzira anapita kwa Yesu ali kwayekha nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?”
20 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhale chosatheka kwa inu.”+
21 *——
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu+
23 ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.
24 Atafika ku Kaperenao, anthu okhometsa msonkho wa madalakima awiri anapita kwa Petulo nʼkumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amapereka madalakima awiri* a msonkho?”+
25 Iye anati: “Inde amapereka.” Koma atalowa mʼnyumba, asananene chilichonse, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?”
26 Atayankha kuti: “Kuchokera kwa anthu achilendo,” Yesu anamuuza kuti: “Ndiye kuti ana sakuyenera kukhoma msonkho.
27 Koma kuti tisawakhumudwitse,+ pita kunyanja, ukaponye mbedza ndipo ukatenge nsomba yoyambirira kuwedza. Ukakaikanula kukamwa kwake, ukapezako khobidi limodzi lasiliva.* Ukalitenge nʼkukhomera msonkho wako ndi wanga.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “anayera.”
^ Onani Zakumapeto A3.
^ Onani Zakumapeto B14.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “khobidi la siteta.” Khobidi limeneli linali lofanana ndi madalakima 4. Onani Zakumapeto B14.