Wolembedwa ndi Mateyu 18:1-35
18 Pa nthawi imeneyo, ophunzira anabwera pafupi ndi Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ndi ndani kwenikweni amene adzakhale wamkulu kwambiri mu Ufumu wakumwamba?”+
2 Choncho iye anaitana mwana wamngʼono nʼkumuimika pakati pawo.
3 Kenako anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mukapanda kutembenuka*+ nʼkukhala ngati ana aangʼono, simudzalowa mu Ufumu wakumwamba.+
4 Choncho aliyense amene adzadzichepetse ngati mwana wamngʼonoyu ndi amene adzakhale wamkulu kwambiri mu Ufumu wakumwamba.+
5 Ndiponso aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati ameneyu mʼdzina langa walandiranso ine.
6 Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana iti timene timandikhulupirira, zingamukhalire bwino kwambiri kumumangirira chimwala cha mphero mʼkhosi mwake chimene bulu amayendetsa, nʼkumuponyera mʼnyanja yakuya.+
7 Tsoka kwa dzikoli chifukwa cha zopunthwitsa! Inde sitingachitire mwina, zopunthwitsazo ziyenera kubwera ndithu, koma tsoka kwa munthu wobweretsa chopunthwitsa!
8 Choncho ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule nʼkulitaya kutali.+ Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi kapena uli wolumala kusiyana nʼkuti uponyedwe mʼmoto wosatha uli ndi manja onse awiri kapena mapazi onse awiri.+
9 Komanso ngati diso lako limakuchimwitsa* ulikolowole nʼkulitaya kutali. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli ndi diso limodzi kusiyana nʼkuti uponyedwe mu Gehena* wamoto uli ndi maso onse awiri.+
10 Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.+
11 *——
12 Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo nʼkusochera,+ kodi sangasiye nkhosa 99 zija mʼphiri nʼkupita kukafunafuna yosocherayo?+
13 Akaipeza, ndithu ndikukuuzani, amasangalala kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zimene sizinasochere zija.
14 Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga* wakumwamba sakufuna kuti ngakhale mmodzi wa tiana timeneti awonongeke.+
15 Komanso ngati mʼbale wako wachimwa, upite kukamufotokozera zimene walakwitsazo* panokha, iwe ndi iyeyo.+ Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza mʼbale wakoyo.+
16 Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi umboni wa mboni* ziwiri kapena zitatu.+
17 Amenewanso akapanda kuwamvera, uuze mpingo. Ndipo mpingowo akapandanso kuumvera, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera kumtundu wina+ komanso ngati wokhometsa msonkho.+
18 Ndithu ndikukuuzani, zilizonse zimene mudzamange padziko lapansi zidzakhala zoti zamangidwa kale kumwamba. Ndipo zilizonse zimene mudzamasule padziko lapansi zidzakhala zoti zamasulidwa kale kumwamba.
19 Ndiponso ndikukuuzani kuti, ngati awiri mwa inu padziko lapansi pano mutagwirizana kuti mupemphe chinthu chilichonse chofunika, Atate wanga wakumwamba adzakuchitirani.+
20 Chifukwa kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana mʼdzina langa,+ ine ndidzakhala pakati pawo.”
21 Kenako Petulo anabwera nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, kodi mʼbale wanga ndizimukhululukira kangati akamandichimwira? Mpaka maulendo 7 kodi?”
22 Yesu anamuyankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati maulendo 7 okha ayi, koma mpaka maulendo 77.+
23 Nʼchifukwa chake Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi mfumu imene inkafuna kuti akapolo ake abweze ngongole.
24 Mfumuyo itayamba kulandira ngongolezo, atumiki ake anabweretsa munthu amene anali ndi ngongole ya matalente 10,000.*
25 Koma chifukwa choti sakanakwanitsa kubweza ngongoleyo, mbuye wake analamula kuti mwamuna ameneyu, mkazi wake, ana ake komanso zonse zimene anali nazo zigulitsidwe nʼkumubwezera ndalama zake.+
26 Ndiyeno kapoloyu anagwada pansi nʼkumuweramira ndipo ananena kuti, ‘Ndilezereni mtima chonde, ndidzakubwezerani zonse.’
27 Mbuyeyo anamva chisoni ndi zimenezi ndipo anamusiya kapoloyo nʼkumukhululukira ngongole yake ija.+
28 Koma kapolo ameneyu atatuluka anakumana ndi kapolo mnzake amene anali ndi ngongole yake yokwana madinari 100.* Choncho anamugwira nʼkuyamba kumukanyanga pakhosi, akunena kuti, ‘Bweza ngongole ija mwamsanga.’
29 Kapolo mnzakeyo anagwada pansi nʼkuyamba kumudandaulira kuti, ‘Ndilezereni mtima chonde, ndidzakubwezerani.’
30 Koma iye sanalole ndipo anapita naye kundende kuti akamutsekere mpaka atamaliza kubweza ngongoleyo.
31 Akapolo anzake ataona zimene zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita kwa mbuye wawo nʼkukamufotokozera zonse zimene zinachitika.
32 Ndiyeno mbuye wakeyo anamuitanitsa nʼkumuuza kuti: ‘Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukira ngongole yonse ija utandidandaulira.
33 Kodi sukanamuchitira chifundo kapolo mnzako, ngati mmene ine ndachitira kwa iwe?’+
34 Choncho mbuye wakeyo anakwiya kwambiri ndipo anapita naye kwa oyangʼanira ndende kuti amutsekere mpaka atamaliza kubweza ngongole yonse ija.
35 Atate wanga wakumwamba adzakuchitiraninso zofanana ndi zimenezi+ ngati aliyense wa inu sakhululukira mʼbale wake ndi mtima wonse.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “kusintha.”
^ Kapena kuti, “limakupunthwitsa.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Zakumapeto A3.
^ Mabaibulo ena amati, “wanu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “upite ukamudzudzule.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi pakamwa pa mboni.”
^ Matalente 10,000 asiliva anali ofanana ndi madinari 60 miliyoni. Onani Zakumapeto B14.
^ Onani Zakumapeto B14.