Wolembedwa ndi Mateyu 22:1-46

  • Fanizo la phwando laukwati (1-14)

  • Mulungu komanso Kaisara (15-22)

  • Funso lokhudza kuukitsidwa kwa akufa (23-33)

  • Malamulo awiri akuluakulu (34-40)

  • Kodi Khristu ndi mwana wa Davide? (41-46)

22  Yesu anawauzanso mafanizo ena kuti: 2  “Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi mfumu imene inakonzera mwana wake wamwamuna phwando la ukwati.+ 3  Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa kuphwando laukwati, koma anthuwo sanafune kubwera.+ 4  Kenako inatumanso akapolo ena kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana, ngʼombe zanga zamphongo komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani kuphwando laukwati.”’ 5  Koma anthuwo ananyalanyaza nʼkuchoka. Wina anapita kumunda wake ndipo wina anapita kumalonda ake.+ 6  Koma enawo anagwira akapolo akewo ndipo anawachitira chipongwe nʼkuwapha. 7  Zitatero mfumu ija inakwiya kwambiri ndipo inatumiza asilikali ake kukapha anthu amene anapha akapolo akewo nʼkuwotcha mzinda wawo.+ 8  Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa, koma oitanidwa aja anali osayenera.+ 9  Choncho pitani mʼmisewu yotulukira mumzinda ndipo aliyense amene mukamupeze, mukamuitane kuti abwere kuphwando laukwatili.’+ 10  Ndiyeno akapolowo anapita mʼmisewu ndipo anasonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe. Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu amene ankadya chakudya. 11  Mfumu ija italowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati. 12  Choncho inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’ Iye anasowa chonena. 13  Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo ndipo mumuponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’ 14  Chifukwa oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.” 15  Kenako Afarisi anachoka nʼkukapangana kuti amupezere zifukwa pa zimene angalankhule.+ 16  Choncho anamutumizira ophunzira awo, limodzi ndi anthu amene ankatsatira Herode,+ ndipo iwo ananena kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu mʼchoonadi, ndiponso simuchita zinthu pongofuna kusangalatsa munthu, chifukwa simuyangʼana maonekedwe a anthu. 17  Ndiye tatiuzani, mukuganiza bwanji? Kodi nʼzololeka* kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 18  Koma Yesu anadziwa kuipa mtima kwawo ndipo ananena kuti: “Anthu achinyengo inu! Bwanji mukundiyesa? 19  Ndionetseni khobidi la msonkho.” Iwo anamubweretsera khobidi limodzi la dinari.* 20  Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi komanso mawu akewa nʼzandani?” 21  Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Choncho iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 22  Atamva zimenezi, anadabwa ndipo anangochokapo nʼkumusiya. 23  Pa tsiku limenelo Asaduki amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 24  “Mphunzitsi, Mose ananena kuti: ‘Ngati mwamuna wamwalira asanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 25  Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako nʼkumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkaziyo anakwatiwa ndi mchimwene wa mwamuna wake uja. 26  Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja. 27  Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 28  Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.” 29  Koma Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.+ 30  Chifukwa akufa akadzaukitsidwa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 31  Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti: 32  ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakoboʼ?+ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.”+ 33  Gulu la anthulo litamva zimenezo, linadabwa ndi zimene ankaphunzitsa.+ 34  Afarisi atamva kuti Yesu anawasowetsa chonena Asaduki, anasonkhana monga gulu limodzi. 35  Ndipo mmodzi wa iwo, amene ankadziwa Chilamulo, anamuyesa pomufunsa kuti: 36  “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri mʼChilamulo ndi liti?”+ 37  Iye anamuyankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi maganizo anu onse.’+ 38  Limeneli ndi lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. 39  Lachiwiri lofanana nalo ndi ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ 40  Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso zimene aneneri analemba.”+ 41  Tsopano Afarisi aja atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti:+ 42  “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+ 43  Iye anawafunsanso kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu,+ Davide anamutchula kuti Ambuye, pamene ananena kuti, 44  ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako”’?+ 45  Ndiye ngati Davide anamutchula kuti Ambuye, zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?”+ 46  Panalibe ngakhale mmodzi amene anatha kumuyankha, ndipo kuchokera tsiku limenelo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nʼzoyenera.”