Wolembedwa ndi Mateyu 23:1-39

  • Musamatsanzire alembi ndi Afarisi (1-12)

  • Tsoka kwa alembi ndi Afarisi (13-36)

  • Yesu analirira Yerusalemu (37-39)

23  Kenako Yesu anauza gulu la anthu ndi ophunzira ake kuti: 2  “Alembi ndi Afarisi adzikhazika pampando wa Mose. 3  Choncho muzichita ndi kutsatira zinthu zonse zimene angakuuzeni, koma musamachite zimene iwo amachita, chifukwa iwo amangonena koma sachita zimene amanenazo.+ 4  Iwo amamanga akatundu olemera nʼkusenzetsa anthu pamapewa,+ koma eni akewo safuna kusuntha akatunduwo ndi chala chawo.+ 5  Zonse zimene amachita, amazichita kuti anthu awaone.+ Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba timene amavala monga zodzitetezera,+ ndipo amatalikitsanso ulusi wopota wa mʼmphepete mwa zovala zawo.+ 6  Amakonda malo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo* mʼmasunagoge.+ 7  Amakondanso kupatsidwa moni mʼmisika komanso kuti anthu aziwatchula kuti Rabi.* 8  Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa Mphunzitsi+ wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. 9  Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, chifukwa Atate+ wanu ndi mmodzi Yekhayo, amene amakhala kumwamba. 10  Musamatchulidwenso kuti atsogoleri, chifukwa Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. 11  Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu.+ 12  Aliyense amene amadzikweza adzatsitsidwa,+ koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.+ 13  Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa mukutseka Ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Popeza inuyo simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe.+ 14 *⁠—— 15  Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumawoloka nyanja komanso kuyenda mitunda italiitali kuti mukatembenuze munthu mmodzi. Koma akatembenuka mumamupangitsa kuti akhale woyenera kuponyedwa mʼGehena* kuposa inuyo. 16  Tsoka kwa inu atsogoleri akhungu,+ amene mumati, ‘Ngati munthu watchula kachisi polumbira, palibe kanthu, koma ngati munthu watchula golide wa mʼkachisi, akuyenera kusunga lumbiro lake.’+ 17  Anthu opusa komanso akhungu inu! Chofunika kwambiri ndi chiti, golide kapena kachisi amene wayeretsa golideyo? 18  Komanso mumati, ‘Ngati munthu watchula guwa lansembe polumbira, palibe kanthu, koma ngati munthu watchula mphatso imene ili paguwapo polumbira, asunge lumbiro lake.’ 19  Anthu akhungu inu! Chofunika kwambiri ndi chiti, mphatso kapena guwa lansembe limene limayeretsa mphatsoyo? 20  Choncho amene watchula guwa lansembe polumbira, walumbirira guwalo ndi zinthu zonse zimene zili pamenepo, 21  ndipo amene watchula kachisi polumbira, walumbirira kachisiyo komanso Mulungu amene amakhala mmenemo.+ 22  Ndipo aliyense amene watchula kumwamba polumbira, walumbirira mpando wachifumu wa Mulungu komanso Mulungu amene wakhala pampandowo. 23  Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili ndi chitowe,+ koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za mʼChilamulo, zomwe ndi chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika. Kupereka zinthu zimenezi nʼkofunika ndithu, koma osanyalanyaza zinthu zinazo.+ 24  Atsogoleri akhungu inu,+ amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere+ koma mumameza ngamila.+ 25  Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa muli ngati kapu ndi mbale zimene zatsukidwa kunja kokha+ koma mkati mwake muli mwakuda. Mkati mwa mitima yanu mwadzaza dyera*+ ndi kusadziletsa.+ 26  Mfarisi wakhungu iwe, yeretsa mkati mwa kapu ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera. 27  Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu,+ amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zamitundu yonse. 28  Mofanana ndi zimenezi, pamaso pa anthu, inunso mumaoneka ngati olungama koma mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo.+ 29  Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumamanga manda a aneneri ndi kukongoletsa manda* a anthu olungama,+ 30  ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako mʼmasiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’ 31  Choncho mukudzichitira nokha umboni kuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneri.+ 32  Ndiyetu malizitsani ntchito imene makolo anu anayamba. 33  Njoka inu, ana a mphiri,+ mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?*+ 34  Pa chifukwa chimenechi, ndikukutumizirani aneneri,+ anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ nʼkuwapachika pamtengo ndipo ena mudzawakwapula+ mʼmasunagoge mwanu ndi kuwazunza+ mumzinda ndi mzinda, 35  kuti magazi onse a anthu olungama amene anakhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu. Kuyambira magazi a Abele wolungama+ mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe.+ 36  Ndithu ndikukuuzani kuti, mʼbadwo uwu udzayankha mlandu wa zinthu zonsezi. 37  Yerusalemu, Yerusalemu, wopha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, ngati mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake mʼmapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 38  Tsopano tamverani! Mulungu wachoka nʼkukusiyirani nyumba yanuyi.*+ 39  Ndithu ndikukuuzani, kuyambira panopa simudzandionanso mpaka pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!’”*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mipando yabwino kwambiri.”
Kapena kuti, “Mphunzitsi.”
Kapena kuti, “kulanda zinthu za eni.”
Kapena kuti, “manda achikumbutso.”
Mabaibulo ena amati, “nʼkukusiyirani nyumba yanuyi ili bwinja.”