Mika 1:1-16
1 Yehova analankhula ndi Mika*+ wa ku Morese mʼmasiku a Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda.+ Analankhula naye kudzera mʼmasomphenya ndipo anamuuza zokhudza Samariya ndi Yerusalemu kuti:
2 “Tamverani anthu nonsenu!
Mvetsera mwatcheru iwe dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo.Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa akhale mboni yokutsutsani,+Yehova akutsutseni ali mʼkachisi wake woyera.
3 Tamverani! Yehova akuchoka pamalo ake,Ndipo atsika nʼkupondaponda malo okwezeka apadziko lapansi.
4 Mapiri adzasungunuka kumapazi ake,+Ndipo zigwa zidzagawanika,Ngati phula losungunuka ndi moto.Ndipo zidzayenda ngati madzi othiridwa pamalo otsetsereka.
5 Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti Yakobo wandigalukira.Ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+
Kodi wachititsa kuti Yakobo andigalukire ndani?
Kodi si anthu a ku Samariya?+
Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+
Si anthu a ku Yerusalemu kodi?
6 Samariya ndidzamusandutsa bwinja,Malo oyenera kudzalapo mpesa.Miyala yake ndidzaiponya* mʼchigwa.Ndipo maziko ake ndidzawafukula nʼkuwasiya pamtunda.
7 Zifaniziro zake zonse zogoba zidzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswazidutswa.+Ndipo mphatso zonse zimene ankalandira ngati malipiro zidzatenthedwa pamoto.+
Mafano ake onse ndidzawawononga.
Chifukwa anawapeza kuchokera ku ndalama zimene ankalandira pochita uhule.Ndipo tsopano zinthu zimenezi zidzatengedwa kuti zikakhale malipiro a mahule kwinakwake.”
8 Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+
Ndidzalira ngati mimbulu,Ndiponso ngati nthiwatiwa.
9 Bala lake ndi losachiritsika,+Ndipo lakafika mpaka ku Yuda.+
Mliri umenewu wafalikira mpaka kukafika pageti la anthu amtundu wanga ku Yerusalemu.+
10 “Musanene zimenezi ku Gati.Ndipo musalire ngakhale pangʼono.
Gubudukani pafumbi ku Beti-afira.*
11 Inu anthu a ku Safiri, tulukani mʼdziko lanu muli maliseche ndiponso mukuchititsa manyazi.
Anthu a ku Zaanana sanachoke mʼdziko lawo.
Ku Beti-ezeli kuzingomveka kulira kokhakokha ndipo anthu ake adzasiya kukuthandizani.
12 Anthu a ku Maroti ankayembekezera zinthu zabwino,Koma zoipa zochokera kwa Yehova zafika pageti la ku Yerusalemu.
13 Inu anthu a ku Lakisi, mangirirani galeta ku gulu la mahatchi.*+
Ndinu amene munayambitsa tchimo la mwana wamkazi wa Ziyoni,*Popeza kugalukira kwa Isiraeli kunapezeka mwa inu.+
14 Choncho mudzapereka mphatso zotsanzikirana kwa Moreseti-gati.
Anthu a ku Akizibu+ anapusitsa mafumu a Isiraeli.
15 Inu anthu a ku Maresha+ ndidzakubweretserani munthu wokugonjetsani,*+
Ulemerero wa Isiraeli udzafika mpaka ku Adulamu.+
16 Muchotse tsitsi lonse ndipo mumete mpala chifukwa cha ana anu amene mumawakonda.
Metani mpala ngati wa chiwombankhanga,Chifukwa chakuti ana anuwo atengedwa kupita kudziko lina.”+
Mawu a M'munsi
^ Chidule cha dzina lakuti Mikayeli (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Mulungu”) kapena Mikaya (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Yehova”).
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzaikhuthulira.”
^ Kapena kuti, “mʼnyumba ya Afira.”
^ Ena amati “mahosi.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Kapena kuti, “wolanda zinthu za ena.”