Mika 6:1-16

  • Mulungu anaimba mlandu Aisiraeli (1-5)

  • Yehova akufuna kuti uzichita chiyani? (6-8)

    • Chilungamo, kukhulupirika, kudzichepetsa (8)

  • Aisiraeli analakwa nʼkulangidwa (9-16)

6  Imvani zimene Yehova akunena. Nyamukani mukanene mlandu wanu kwa mapiri akuluakulu,Ndipo mapiri angʼonoangʼono akamve mawu anu.+  2  Inu mapiri akuluakulu, imvani mlandu umene Yehova ali nawo pa anthu ake.Mvetserani inu maziko a dziko lapansi,+Chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake.Iye azenga mlandu Aisiraeli, kuti:+  3  “Inu anthu anga, ndakulakwirani chiyani? Kodi ndachita chiyani kuti ndikutopetseni?+ Perekani umboni wonditsutsa.  4  Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+Ndinakuwombolani mʼnyumba ya ukapolo,+Ndipo ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.+  5  Inu anthu anga, chonde kumbukirani zimene Balaki mfumu ya Mowabu ankafuna kuchita.+Ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+Kumbukirani zimenezi kuti mudziwe ntchito zolungama za Yehova.”  6  Kodi nditenge chiyani popita kwa Yehova? Ndikagwade ndi chiyani kwa Mulungu wakumwamba? Kodi ndipite nditatenga nsembe zopsereza zathunthu?Ndiponso ana a ngʼombe achaka chimodzi?+  7  Kodi Yehova adzasangalala ndi masauzande a nkhosa zamphongo?Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande ambirimbiri?+ Kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba chifukwa cha zolakwa zanga,Ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?+  8  Iye anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna kuti uzichita* chiyani? Iye akungofuna kuti uzichita chilungamo,*+ uziona kuti kukhulupirika nʼkofunika,*+Ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+  9  Mawu a Yehova akumveka mumzinda.Anthu anzeru zopindulitsa adzaopa dzina lanu. Mverani mawu a ndodo ndi a amene anaisankha.*+ 10  Kodi mʼnyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo?Ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wonyansa? 11  Kodi ndingakhale woyera* ndili ndi sikelo yachinyengo,Ndiponso thumba la miyala yachinyengo yoyezera zinthu?+ 12  Anthu olemera amumzindawo amakonda kuchita zachiwawa.Anthu ake amalankhula zabodza+Ndipo lilime lawo ndi lachinyengo.+ 13  “Choncho ine ndidzakumenyani mpaka mudzakhala ndi mabala,+Ndipo mudzasautsika chifukwa cha machimo anu. 14  Inu mudzadya, koma simudzakhuta.Ndipo mudzamvabe njala.+ Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino, koma simudzatha kuziteteza.Zimene mudzatenge, ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge. 15  Mudzadzala mbewu, koma simudzakolola. Mudzaponda maolivi, koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake.Mudzapanga vinyo watsopano, koma simudzamwa vinyo.+ 16  Mukutsatira malamulo a Omuri komanso zinthu zonse zimene anthu a mʼnyumba ya Ahabu amachita.+Ndipo mukuyendera malangizo awo. Nʼchifukwa chake ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa,Ndipo anthu amumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+Inuyo mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “uzikhala wokoma mtima ndipo chikondi chako chizikhala chokhulupirika.” Mʼchilankhulo choyambirira, “uzikonda chikondi chokhulupirika.”
Kapena kuti, “ukhale wachilungamo.”
Kapena kuti, “umubwezere.”
Kapena kuti, “Mverani chilango ndi amene akuchipereka.”
Kapena kuti, “wosalakwa.”