Miyambo 11:1-31
11 Yehova amanyasidwa ndi masikelo achinyengo,Koma sikelo imene imayeza molondola imamusangalatsa.*+
2 Kudzikweza kukafika manyazi amafikanso,+Koma anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.+
3 Kukhulupirika kwa anthu owongoka mtima nʼkumene kumawatsogolera,+Koma wochita zinthu mwachinyengo adzawonongedwa chifukwa cha mabodza ake.+
4 Chuma chidzakhala chopanda* phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+Koma chilungamo nʼchimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+
5 Chilungamo cha munthu wopanda cholakwa chimawongola njira yake,Koma woipa adzagwa chifukwa cha kuipa kwake komwe.+
6 Chilungamo cha anthu owongoka mtima chidzawapulumutsa,+Koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+
7 Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimathera pomwepo,Ndipo zonse zimene amayembekezera kuchita ndi mphamvu zake zimalephereka.+
8 Wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,Ndipo mʼmalo mwake woipa ndi amene amakumana ndi mavutowo.+
9 Wampatuko* amawononga mnzake ndi pakamwa pake,Koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+
10 Mzinda umasangalala chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,Ndipo anthu oipa akawonongedwa anthu amafuula mosangalala.+
11 Mzinda umakhala wapamwamba chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+Koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+
12 Aliyense wopanda nzeru amasonyeza kuti akuipidwa ndi* mnzake,Koma munthu amene alidi wozindikira amakhala chete.+
13 Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi za anzake,+Koma munthu wokhulupirika* amasunga chinsinsi.*
14 Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.Koma zinthu zimayenda bwino* ngati pali alangizi* ambiri.+
15 Munthu amene amalonjeza kuti adzapereka ngongole ya munthu wachilendo mwiniwakeyo akadzalephera kubweza, zinthu sizidzamuyendera bwino.+Koma amene amapewa* kugwirana dzanja pochita mgwirizano adzakhala wotetezeka.
16 Mkazi wachikoka amapeza ulemu.+Koma anthu ankhanza amalanda chuma cha ena.
17 Munthu wokoma mtima* zinthu zimamuyendera bwino,*+Koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.*+
18 Munthu woipa amapeza malipiro achinyengo,+Koma wofesa chilungamo amalandira mphoto yeniyeni.+
19 Munthu wosasunthika pachilungamo adzapeza moyo,+Koma munthu wofunafuna zoipa adzafa.
20 Anthu amtima wopotoka, Yehova amanyasidwa nawo,+Koma amene amachita zinthu mosalakwitsa kanthu amamusangalatsa.+
21 Musakaikire mfundo yakuti:* Munthu woipa sadzalephera kulangidwa,+Koma ana a anthu olungama adzapulumuka.
22 Mofanana ndi ndolo yagolide imene ili pamphuno ya nkhumba,Ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola amene amakana nzeru.
23 Zimene munthu wolungama amalakalaka zimakhala ndi zotsatira zabwino.+Koma zimene oipa amayembekezera zimabweretsa mkwiyo woopsa.
24 Munthu amapereka mowolowa manja* ndipo pamapeto pake amakhala ndi zinthu zochuluka.+Munthu wina amaumira zimene amafunika kupatsa anthu ena, koma amasauka.+
25 Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino,*+Ndipo amene amatsitsimula ena* nayenso adzatsitsimulidwa.+
26 Wokana kugulitsa mbewu zake, anthu adzamʼtemberera.Koma wolola kuzigulitsa adzamudalitsa.
27 Munthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino, adzakomeredwa mtima.+Koma wofunitsitsa kuchita zoipa, zoipazo zidzamʼbwerera.+
28 Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto,+Koma anthu olungama adzasangalala ngati mtengo wa masamba obiriwira.+
29 Aliyense wobweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake cholowa chake chidzakhala mphepo,+Ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wanzeru.
30 Zotsatira za zimene munthu wolungama amachita zili ngati mtengo wa moyo,+Ndipo munthu amene amalimbikitsa ena kuchita zabwino ndi wanzeru.+
31 Ngati wolungama padziko lapansi amapatsidwa mphoto,Ndiye kuli bwanji woipa ndi wochimwa?+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mwala woyezera wolemera mokwanira umamusangalatsa.”
^ Kapena kuti, “Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda.”
^ Kapena kuti, “Munthu wosaopa Mulungu.”
^ Kapena kuti, “amanyoza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “wa mzimu wokhulupirika.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amabisa nkhani.”
^ Kapena kuti, “Koma munthu amapulumuka.”
^ Kapena kuti, “aphungu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amadana ndi.”
^ Kapena kuti, “wachikondi chokhulupirika.”
^ Kapena kuti, “amachitira zabwino moyo wake.”
^ Kapena kuti, “manyazi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amamwaza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepetsedwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amathirira ena mosaumira.”
^ Kapena kuti, “manyazi.”