Miyambo 13:1-25

  • Anthu amene amapempha malangizo amakhala ndi nzeru (10)

  • Chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala (12)

  • Nthumwi yokhulupirika imachiritsa (17)

  • Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru (20)

  • Chilango chimasonyeza chikondi (24)

13  Mwana wanzeru amalandira malangizo* ochokera kwa bambo ake,+Koma wonyoza samvera akadzudzulidwa.*+  2  Munthu adzadya zinthu zabwino kuchokera pa zipatso zapakamwa pake,+Koma anthu achinyengo amalakalaka kuchita zachiwawa.  3  Amene amayangʼanira pakamwa pake* amateteza moyo wake,+Koma amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+  4  Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho alibe chilichonse.+Koma munthu wakhama zinthu zidzamuyendera bwino.*+  5  Wolungama amadana ndi mabodza,+Koma zochita za munthu woipa zimabweretsa manyazi ndi kunyozeka.  6  Chilungamo chimateteza munthu wosalakwa,+Koma kuchita zoipa kumachititsa kuti wochimwa awonongeke.  7  Pali munthu amene amadzionetsa ngati wolemera koma chonsecho alibe chilichonse.+Pali munthu winanso amene amadzionetsa ngati wosauka koma ali ndi chuma chambiri.  8  Chuma chimawombola moyo wa munthu,+Koma anthu osauka saopsezedwa* nʼkomwe.+  9  Kuwala kwa nyale ya anthu olungama kukuwonjezeka kwambiri.*+Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+ 10  Kudzikuza kumangoyambitsa mikangano basi,+Koma anthu amene amapempha malangizo* amakhala ndi nzeru.+ 11  Chuma chimene munthu amachipeza mofulumira* sichichedwa kutha,+Koma chuma cha munthu amene wachipeza pangʼonopangʼono* chidzawonjezeka. 12  Chinthu chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala.+Koma chomwe umalakalaka chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+ 13  Aliyense amene safuna kutsatira malangizo, adzakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zakezo,+Koma munthu amene amamvera malamulo adzalandira mphoto.+ 14  Zimene munthu wanzeru amaphunzitsa* zimapereka moyo,+Chifukwa zimapulumutsa munthu kumisampha ya imfa. 15  Munthu wozindikira kwambiri, anthu amamukomera mtima,Koma anthu achinyengo moyo wawo umakhala wodzaza ndi mavuto. 16  Munthu wochenjera amadziwa zimene akuchita,+Koma wopusa amaonetsa uchitsiru wake wonse.+ 17  Munthu woipa wobweretsa uthenga amakumana ndi mavuto,+Koma nthumwi yokhulupirika imachiritsa.+ 18  Aliyense amene amanyalanyaza malangizo* amasauka ndipo amanyozeka,Koma amene amamvera akadzudzulidwa adzalemekezedwa.+ 19  Zimene munthu amalakalaka zikakwaniritsidwa amasangalala.+Koma opusa amadana ndi zoti asiye zinthu zoipa.+ 20  Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+Koma amene amachita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+ 21  Tsoka limatsatira ochimwa,+Koma anthu olungama zinthu zimawayendera bwino.+ 22  Munthu wabwino amasiyira cholowa zidzukulu zake,Koma chuma cha munthu wochimwa chidzasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+ 23  Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,Koma chingathe kutengedwa* ndi anthu opanda chilungamo. 24  Munthu amene sakwapula* mwana wake ndiye kuti akudana naye,+Koma amene amamukonda salephera* kumupatsa chilango.+ 25  Wolungama amadya nʼkukhuta,+Koma mimba za anthu oipa zimakhala zopanda kanthu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “akalangizidwa.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Kapena kuti, “zimene amalankhula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzudzulidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kukusangalala.”
Kapena kuti, “amene amakhala pamodzi nʼkumakambirana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachisonkhanitsa ndi manja ake.”
Kapena kuti, “mʼnjira zachinyengo.”
Kapena kuti, “Chilamulo cha munthu wanzeru.”
Kapena kuti, “akadzudzulidwa.”
Kapena kuti, “angathe kuwonongedwa.”
Kapena kuti, “sapereka chilango kwa.”
Mabaibulo ena amati, “sazengereza.”