Miyambo 14:1-35
14 Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+Koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.
2 Munthu amene amachita zabwino amaopa Yehova,Koma amene amachita zinthu mwachinyengo* amanyoza Mulungu.
3 Mawu odzikuza a munthu wopusa ali ngati chikwapu cholangira munthu,Koma milomo ya anthu anzeru idzawateteza.
4 Ngati palibe ngʼombe, chodyeramo chimakhala choyera.Koma zokolola zimachuluka ngati pali ngʼombe yamphongo yamphamvu.
5 Mboni yokhulupirika sinama,Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha.+
6 Munthu wonyoza amafunafuna nzeru koma sazipeza,Koma munthu womvetsa zinthu amaphunzira zinthu mosavuta.+
7 Usayandikire munthu wopusa,Chifukwa suphunzira chilichonse mʼmawu otuluka pakamwa pake.+
8 Nzeru zimathandiza munthu wochenjera kuzindikira njira imene akuyenda,Koma anthu opusa amapusitsika* ndi kupusa kwawo komwe.+
9 Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,*+Koma anthu owongoka mtima amakhala ofunitsitsa kugwirizananso.
10 Ngati munthu mtima ukumupweteka amadziwa yekha,Ndipo munthu wina sangamvetse mmene mnzake akusangalalira mumtima mwake.
11 Nyumba ya munthu woipa idzawonongedwa,+Koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.*
12 Pali njira imene imaoneka ngati yabwino kwa munthu,+Koma pamapeto pake imabweretsa imfa.+
13 Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kumamupweteka.Ndipo kusangalala kungathere mʼchisoni.
14 Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakumana ndi zotsatira za zochita zake,+Koma munthu wabwino amapeza mphoto chifukwa cha zochita zake.+
15 Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse,Koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.+
16 Munthu wanzeru amachita zinthu mosamala ndipo amapewa zoipa,Koma wopusa amachita zinthu mosasamala* ndipo amakhala wodzidalira.
17 Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+Koma munthu amene amaganiza bwino amadedwa.
18 Anthu osadziwa zambiri adzakhala opusa,Koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chisoti chachifumu.+
19 Anthu oipa adzagwadira anthu abwino,Ndipo oipa adzagwada pamageti a anthu olungama.
20 Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi anzake,+Koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+
21 Munthu amene amanyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,Koma wosangalala ndi munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+
22 Anthu okonza chiwembu amasochera,
Koma amene ali ndi mtima wofunitsitsa kuchita zabwino amawachitira zinthu mokhulupirika komanso kuwasonyeza chikondi chokhulupirika.+
23 Kugwira ntchito iliyonse mwakhama kumapindulitsa,Koma kungolankhula chabe kumasaukitsa.+
24 Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo.Koma kupusa kumapangitsa kuti anthu opusa apitirizebe kukhala opusa.+
25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo ya anthu,Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha.
26 Munthu woopa Yehova amamukhulupirira pa chilichonse,+Ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+
27 Kuopa Yehova kuli ngati kasupe wa moyo,Chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa.
28 Kuchuluka kwa anthu kumabweretsa ulemerero kwa mfumu,+Koma wolamulira amene alibe anthu oti aziwalamulira ulamuliro wake umatha.
29 Munthu amene sakwiya msanga ndi wozindikira zinthu kwambiri,+Koma wosaugwira mtima amasonyeza uchitsiru wake.+
30 Mtima wodekha umapangitsa kuti thupi likhale lathanzi,Koma nsanje imawoletsa mafupa.+
31 Amene amabera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+Koma amene amakomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+
32 Woipa adzagwetsedwa ndi kuipa kwakeko,Koma kukhulupirika kwa munthu wolungama kudzakhala malo ake othawirako.+
33 Munthu womvetsa zinthu salankhula modzitama kuti ali ndi nzeru,+Koma munthu wopusa, nthawi zonse amalengeza zimene akudziwa.
34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,+Koma tchimo limachititsa manyazi mitundu ya anthu.
35 Mfumu imasangalala ndi wantchito amene amachita zinthu mozindikira,+Koma imakwiya ndi wantchito wochita zinthu zochititsa manyazi.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “zopotoka.”
^ Mabaibulo ena amati, “anthu opusa amapusitsa anzawo.”
^ Kapena kuti, “Anthu opusa akapalamula mlandu zoti akonze zinthu zimangowaseketsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “idzalemera.”
^ Kapena kuti, “amakhala wokwiya.”