Miyambo 15:1-33
15 Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+
2 Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+Koma pakamwa pa zitsiru pamangolankhula mawu opusa.
3 Maso a Yehova ali paliponse,Amaona anthu oipa ndi abwino omwe.+
4 Lilime lodekha* lili ngati mtengo wa moyo,+Koma mawu achinyengo amachititsa kuti anthu ataye mtima.
5 Munthu wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+Koma munthu wochenjera amamvera ena akamudzudzula.+
6 Mʼnyumba ya munthu wolungama muli chuma chambiri,Koma zokolola za munthu woipa zimamubweretsera mavuto.+
7 Milomo ya munthu wanzeru imafalitsa zimene akudziwa,+Koma mtima wa munthu wopusa suchita zimenezo.+
8 Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa kwa Yehova,+Koma pemphero la munthu wowongoka mtima limamusangalatsa.+
9 Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+Koma amakonda munthu amene amachita chilungamo.+
10 Chilango chimaoneka choipa* kwa munthu amene wasiya njira yabwino,+Koma aliyense amene amadana ndi kudzudzulidwa adzafa.+
11 Ngati Yehova amaona bwinobwino amene ali mʼManda* ndiponso malo achiwonongeko,*+
Ndiye kuli bwanji zimene zili mʼmitima ya anthu?+
12 Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akumudzudzula.+
Iye sadzapempha malangizo kwa anthu anzeru.+
13 Mtima wachimwemwe umapangitsa kuti nkhope izioneka yosangalala,Koma munthu sasangalala ngati mtima ukumupweteka.+
14 Anthu anzeru* amayesetsa kuti adziwe zinthu,+Koma pakamwa pa anthu opusa pamasangalala ndi zinthu zopusa.+
15 Masiku onse a munthu amene akukumana ndi mavuto amakhala oipa,+Koma munthu amene ali ndi mtima wosangalala* amachita phwando nthawi zonse.+
16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+Kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri koma uli ndi nkhawa.*+
17 Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+Kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa* koma pali chidani.+
18 Munthu wosachedwa kupsa mtima amayambitsa mkangano,+Koma munthu amene sakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+
19 Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+Koma njira ya munthu wowongoka mtima ili ngati msewu wosalazidwa bwino.+
20 Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma munthu wopusa amanyoza mayi ake.+
21 Munthu wopanda nzeru amasangalala ndi uchitsiru,+Koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+
22 Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana,*Koma alangizi akachuluka zinthu zimayenda bwino.+
23 Munthu amasangalala akapereka yankho labwino,*+Ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+
24 Munthu amene ndi wozindikira ali panjira yokwezeka yopita kumoyo,+Ndipo amapewa kuyenda mʼnjira yotsikira ku Manda.*+
25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+Koma adzateteza malire a malo a mkazi wamasiye.+
26 Yehova amadana ndi ziwembu za munthu woipa,+Koma mawu osangalatsa ndi oyera kwa iye.+
27 Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake,+Koma amene amadana ndi ziphuphu adzakhalabe ndi moyo.+
28 Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+Koma pakamwa pa anthu oipa pamangolankhula zoipa.
29 Yehova ali kutali ndi anthu oipa,Koma amamva pemphero la anthu olungama.+
30 Maso owala amapangitsa* kuti mtima usangalale.Uthenga wabwino umachititsa kuti mafupa akhale amphamvu.*+
31 Munthu amene amamvetsera chidzudzulo chopatsa moyo,Amakhala pakati pa anthu anzeru.+
32 Aliyense amene amakana malangizo amanyoza moyo wake,+Koma amene amamvetsera akadzudzulidwa amakhala wozindikira.+
33 Kuopa Yehova nʼkumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+Ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “moleza mtima.”
^ Kapena kuti, “Lilime lochiritsa.”
^ Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
^ Kapena kuti, “chowawa kwambiri.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndiponso Abadoni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wanzeru.”
^ Kapena kuti, “wabwino.”
^ Kapena kuti, “koma uli wosokonezeka maganizo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “yodyetsedwa bwino.”
^ Kapena kuti, “sakambirana moona mtima.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “manyazi.”
^ Kapena kuti, “Kuyangʼana munthu ndi nkhope yachimwemwe kumapangitsa.”
^ Kapena kuti, “umanenepetsa mafupa.”