Miyambo 18:1-24

  • Kudzipatula ndi kudzikonda komanso kupanda nzeru (1)

  • Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba (10)

  • Chuma chili ngati chitetezo mʼmaganizo mwa munthu (11)

  • Ubwino womvetsera mbali zonse (17)

  • Mnzako amakhala nawe pafupi kuposa mʼbale wako (24)

18  Munthu aliyense amene amadzipatula amangoganizira kuchita zimene amalakalaka.Iye amakana* nzeru zonse zopindulitsa.  2  Munthu wopusa sasangalala ndi kumvetsa zinthu.Iye amangokonda kuulula zimene zili mumtima mwake.+  3  Munthu woipa akabwera, pamabweranso kunyozeka,Ndipo munthu akamachita zinthu zochititsa manyazi amanyozeka.+  4  Mawu amʼkamwa mwa munthu ali ngati madzi akuya.+ Kasupe wa nzeru ali ngati mtsinje wosefukira.  5  Si bwino kukondera munthu woipa+Kapena kulephera kuchitira chilungamo munthu wolungama.+  6  Zolankhula za munthu wopusa zimayambitsa mikangano,+Ndipo pakamwa pake pamaitana zikwapu.+  7  Pakamwa pa munthu wopusa mʼpamene pamamuchititsa kuti awonongedwe,+Ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.  8  Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati chakudya chokoma,*+Akachimeza chimalowa mʼmimba.+  9  Munthu waulesi pa ntchito yakeNdi mʼbale wake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+ 10  Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+ Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.*+ 11  Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba.Ndipo mʼmaganizo mwake chili ngati mpanda umene ukumuteteza.+ 12  Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+Ndipo akadzichepetsa amapeza ulemerero.+ 13  Munthu akayankhira nkhani asanaimvetsetse,Kumakhala kupusa ndipo amachita manyazi.+ 14  Mtima wa munthu ukhoza kupirira matenda,+Koma mtima wosweka ndi ndani angaupirire?+ 15  Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu,+Ndipo khutu la munthu wanzeru limafunitsitsa kudziwa zinthu. 16  Mphatso ya munthu imamʼtsegulira njira,+Ndipo imamuthandiza kuti akafike kwa anthu olemekezeka. 17  Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola,+Mpaka mnzake atabwera nʼkudzamufunsa mafunso.*+ 18  Kuchita maere kumathetsa mikangano+Ndipo kumathetsa nkhani pakati pa* anthu amphamvu. 19  Kusangalatsa mʼbale amene walakwiridwa nʼkovuta kwambiri kuposa kulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba,+Ndipo mikangano ingathe kulekanitsa anthu ngati mageti otseka a mzinda wolimba.+ 20  Mimba ya munthu imakhuta zipatso za mawu otuluka pakamwa pake.+Iye amakhuta zokolola za milomo yake. 21  Imfa ndiponso moyo zili mumphamvu ya lilime,+Ndipo amene amakonda kuligwiritsa ntchito adzadya zipatso zake.+ 22  Munthu amene wapeza mkazi wabwino wapeza chinthu chabwino,+Ndipo Yehova amamukomera mtima.*+ 23  Munthu wosauka akamalankhula amachita kuchonderera,Koma munthu wolemera amayankha mwaukali. 24  Pali anthu ogwirizana amene ndi okonzeka kuchitirana zoipa,+Koma pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Amanyansidwa ndi.”
Kapena kuti, “ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amakwezedwa mʼmwamba,” kutanthauza kuti amaikidwa mʼmalo otetezeka.
Kapena kuti, “kudzamufufuza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumalekanitsa.”
Kapena kuti, “amamufunira zabwino.”