Miyambo 22:1-29
22 Ndi bwino kusankha dzina labwino* kusiyana ndi chuma chochuluka.+Kulemekezedwa* nʼkwabwino kuposa siliva ndi golide.
2 Anthu olemera ndiponso anthu osauka ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi:
Onsewo anapangidwa ndi Yehova.+
3 Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala,Koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.
4 Zotsatira za kudzichepetsa komanso kuopa YehovaNdi chuma, ulemerero ndi moyo.+
5 Minga ndi misampha zili mʼnjira ya munthu wochita zopotoka,Koma aliyense amene amaona kuti moyo wake ndi wamtengo wapatali, amakhala nazo kutali.+
6 Phunzitsa mwana kuti aziyenda mʼnjira imene akuyenera kuyendamo.+Ngakhale akadzakalamba sadzachoka mʼnjira imeneyo.+
7 Wolemera amalamulira anthu osauka,Ndipo wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsa.+
8 Wofesa zosalungama adzakolola mavuto,+Ndipo ndodo ya ukali wake idzatha.+
9 Munthu wowolowa manja* adzadalitsidwa,Chifukwa amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.+
10 Thamangitsa munthu wonyozaNdipo mikangano itha,Komanso milandu ndi kunyozana zilekeka.
11 Munthu amene mtima wake ndi woyera ndipo amalankhula mokoma mtima,Adzakhala bwenzi la mfumu.+
12 Maso a Yehova amateteza wodziwa zinthu,Koma iye amawononga mawu a munthu wochita zachinyengo.+
13 Waulesi amanena kuti: “Panja pali mkango!
Ndithu undipha pakati pa bwalo la mzinda!”+
14 Pakamwa pa akazi amakhalidwe oipa* pali ngati dzenje lakuya.+
Amene waputa mkwiyo wa Yehova adzagweramo.
15 Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.+Koma ndodo yomulangira ndi imene imauthamangitsira kutali ndi iye.+
16 Amene amabera mwachinyengo munthu wosauka kuti awonjezere chuma chake+Komanso wopereka mphatso kwa munthu wolemera,Ndithu adzasauka.
17 Tchera khutu lako ndipo umvetsere mawu a anthu anzeru,+Kuti ulandire ndi mtima wonse nzeru zochokera kwa ine.+
18 Chifukwa nʼzosangalatsa kuti uzisunge mumtima mwako,+Ukatero zidzakhazikika pamilomo yako nthawi zonse.+
19 Lero ndakudziwitsa zinthu,Nʼcholinga choti uzidalira Yehova.
20 Kodi sindinakulembereZinthu zoti zikupatse malangizo komanso kukuphunzitsa,
21 Nʼcholinga choti ndikuphunzitse mawu oona komanso odalirika,Kuti ubwerere kwa amene wakutuma nʼkukamuuza lipoti lolondola?
22 Usabere munthu wosauka chifukwa choti ndi wosauka,+Ndipo usapondereze munthu wonyozeka pageti la mzinda,+
23 Chifukwa Yehova adzawateteza pa mlandu wawo,+Ndipo adzachotsa moyo wa anthu amene akuwabera mwachinyengo.
24 Usamagwirizane ndi munthu wosachedwa kupsa mtimaKapena kuchita zinthu ndi munthu wosachedwa kukwiya,
25 Kuti usaphunzire njira zakeNʼkudzitchera wekha msampha.+
26 Usakhale mʼgulu la anthu amene akugwirana dzanja pochita mgwirizano,Amene amakhala chikole cha ngongole za anthu ena.+
27 Ukadzalephera kulipira,Adzakulanda bedi limene umagonapo.
28 Usamasunthe chizindikiro chakalekale cha malire,Chimene makolo anu anaika.+
29 Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake?
Iye adzaima pamaso pa mafumu.+Sadzaima pamaso pa anthu wamba.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Kukomeredwa mtima.”
^ Kapena kuti, “mbiri yabwino.” Mʼchilankhulo choyambirira, “dzina.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakumana pamodzi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Amene ali ndi diso labwino.”