Miyambo 24:1-34
24 Usamasirire anthu oipa,Ndipo usamalakelake utakhala pagulu lawo,+
2 Chifukwa mtima wawo umangoganizira zochita chiwawa,Ndipo milomo yawo imangokhalira kulankhula zobweretsera ena mavuto.
3 Nzeru zimamanga nyumba ya* munthu,+Ndipo kuzindikira kumachititsa kuti ilimbe kwambiri.
4 Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda za nyumbayo zidzazeNdi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.+
5 Munthu wanzeru ndi wamphamvu,+Ndipo akakhala wodziwa zinthu amawonjezera mphamvu zake.
6 Ukamatsatira malangizo anzeru udzatha kumenya nkhondo yako,+Ndipo pakakhala alangizi* ambiri udzapambana.*+
7 Kwa munthu wopusa nʼzosatheka kupeza nzeru zenizeni.+Ndipo amakhala alibe chilichonse choti anganene pageti la mzinda.
8 Aliyense wokonzera anzake ziwembuAdzatchedwa katswiri wokonza ziwembu.+
9 Mapulani a munthu* wopusa amamupangitsa kuti achite tchimo,Ndipo anthu amanyansidwa ndi munthu wonyoza.+
10 Ukafooka pa nthawi imene ukukumana ndi mavuto,Mphamvu zako zidzachepa.
11 Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe,Ndipo amene akuyenda modzandira popita kukaphedwa uwathandize.+
12 Ukanena kuti: “Ifetu zimenezi sitimazidziwa,”
Kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimene zili mʼmaganizo mwako?+
Ndithudi, amene amakuyangʼanitsitsa adzadziwaNdipo adzabwezera munthu aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+
13 Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino.Uchi wochokera pazisa za njuchi umatsekemera.
14 Mofanana ndi zimenezi, dziwa kuti nzeru ndi zabwino kwa iwe.*+
Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwinoNdipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+
15 Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pafupi ndi nyumba yake kuti umuchitire chiwembu.Usamawononge malo ake okhala.
16 Chifukwa munthu wolungama akhoza kugwa maulendo 7 ndipo adzadzukanso,+Koma anthu oipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzagwa.+
17 Mdani wako akagwa usamasangalale,Ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere.+
18 Ukachita zimenezi Yehova adzaona ndipo zidzamuipiraMoti adzachotsa mkwiyo wake pa mdani wakoyo.+
19 Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.Usamasirire anthu oipa,
20 Chifukwa aliyense woipa alibe tsogolo,+Ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+
21 Mwana wanga uziopa Yehova komanso mfumu.+
Ndipo usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe,+
22 Chifukwa tsoka lawo lidzabwera modzidzimutsa.+
Ndipo ndi ndani amene angadziwe za tsoka limene onsewa* adzawabweretsere?+
23 Mawu awanso ndi a anthu anzeru:
Si bwino kukondera poweruza mlandu.+
24 Aliyense amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wolungama,”+
Anthu adzamutemberera ndipo mitundu ya anthu idzaitanira tsoka pa iye.
25 Koma anthu amene amamudzudzula zinthu zidzawayendera bwino.+Adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+
26 Anthu adzakisa milomo ya munthu amene amayankha moona mtima.*+
27 Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo uonetsetse kuti ntchito yonse yatheka mʼmunda wako.Ukatero ukamange nyumba yako.*
28 Usapereke umboni wotsutsana ndi mnzako ngati ulibe umboni weniweni.+
Usapusitse anthu ena ndi milomo yako.+
29 Usanene kuti: “Ndimuchitira zimene iye wandichitira.Ndimubwezera zimene anandichitira.”+
30 Ndinadutsa pamunda pa munthu waulesi,+Pamunda wa mpesa wa munthu wopanda nzeru.
31 Ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.Zitsamba zoyabwa zinali paliponse mʼmundamo,Komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+
32 Nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,Ndipo ndinaphunzirapo kuti:
33 Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume,
34 Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “banja la.”
^ Kapena kuti, “aphungu.”
^ Kapena kuti, “zinthu zidzakuyendera bwino; udzapulumuka.”
^ Kapena kuti, “Ziwembu za munthu.”
^ Kapena kuti, “nʼzotsekemera kwa iwe.”
^ Kutanthauza Yehova komanso mfumu.
^ Mabaibulo ena amati, “Kuyankha mosapita mʼmbali kuli ngati kukisa munthu.”
^ Kapena kuti, “ukalimbitse banja lako.”