Miyambo 28:1-28
28 Anthu oipa amathawa popanda wowathamangitsa,Koma olungama amakhala olimba mtima ngati mkango.*+
2 Anthu okhala mʼdziko akamachimwa,* dzikolo limasintha akalonga pafupipafupi,+Koma kalonga akamathandizidwa ndi munthu wozindikira komanso wodziwa zinthu, amakhala nthawi yaitali.+
3 Munthu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+Ali ngati mvula imene imakokolola chakudya chonse.
4 Anthu amene asiya chilamulo amatamanda munthu woipa,Koma amene amasunga chilamulo amakwiyira anthu amene asiya chilamulowo.+
5 Anthu oipa sangamvetse chilungamo,Koma amene akufunafuna Yehova angathe kumvetsa chilichonse.+
6 Munthu wosauka amene amachita zinthu mokhulupirika,Ali bwino kuposa munthu wolemera amene amachita zachinyengo.+
7 Mwana womvetsa zinthu amatsatira malamulo,Koma amene amakonda kucheza ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+
8 Munthu amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja+ ndi katapira,Chuma chakecho chidzapita kwa munthu amene amakomera mtima anthu osauka.+
9 Munthu amene amakana kumvera chilamulo,Ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+
10 Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima kuti azichita zinthu zoipa, adzagwera mʼdzenje lake lomwe,+Koma anthu osalakwa adzalandira zinthu zabwino.+
11 Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru,+Koma munthu wosauka amene ndi wozindikira amamufufuza nʼkudziwa zoona zake.+
12 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, anthu amasangalala kwambiri,*Koma anthu oipa akayamba kulamulira, anthu amabisala.+
13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+Koma amene amawaulula nʼkuwasiya adzachitiridwa chifundo.+
14 Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake,*Koma amene amaumitsa mtima wake adzakumana ndi tsoka.+
15 Mtsogoleri woipa amene akulamulira anthu onyozeka+Ali ngati mkango wobangula komanso chimbalangondo chimene chakonzekera kugwira nyama.
16 Mtsogoleri wosazindikira amagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika,+Koma amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo adzatalikitsa moyo wake.+
17 Munthu amene ali ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu, adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.*+
Aliyense asamuthandize.
18 Amene amayenda mosalakwitsa kanthu adzapulumutsidwa,+Koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mwadzidzidzi.+
19 Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chambiri,Koma amene akutanganidwa ndi zinthu zopanda phindu adzakhala pa umphawi waukulu.+
20 Munthu wokhulupirika adzalandira madalitso ambiri,+Koma amene akufuna kulemera mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+
21 Si bwino kukondera.+Koma munthu akhoza kuchita zinthu zolakwika pofuna kupeza kachidutswa ka chakudya.
22 Munthu wadyera amayesetsa kuti apeze chuma,Osadziwa kuti umphawi udzamugwira.
23 Amene amadzudzula munthu,+ pambuyo pake adzakondedwa kwambiri+Kuposa munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamaso.
24 Wobera bambo ake ndi mayi ake nʼkumanena kuti, “Si kulakwa,”+
Amakhala ngati mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+
25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,Koma aliyense amene amadalira Yehova zinthu zidzamuyendera bwino.*+
26 Aliyense amene amadalira mtima wake ndi wopusa,+Koma amene amachita zinthu mwanzeru adzapulumuka.+
27 Aliyense amene amapereka zinthu zake kwa anthu osauka sadzasowa kanthu,+Koma amene amatseka maso ake kuti asaone osaukawo adzalandira matemberero ambiri.
28 Munthu woipa akayamba kulamulira, munthu amabisala,Koma oipawo akatha anthu olungama amachuluka.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mkango wamphamvu.”
^ Kapena kuti, “akamachita zinthu zoukira.”
^ Kapena kuti, “pamakhala ulemerero wochuluka.”
^ Kapena kuti, “amene sachita mantha.”
^ Kapena kuti, “mʼdzenje.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepa.”