Miyambo 29:1-27
29 Munthu amene amaumitsa khosi lake* pambuyo podzudzulidwa mobwerezabwereza+Adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo sadzachira.+
2 Olungama akachuluka, anthu amasangalala,Koma munthu woipa akamalamulira, anthu amabuula.+
3 Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+Koma woyenda ndi mahule amawononga chuma chake.+
4 Mfumu ikamachita zinthu zachilungamo dziko limalimba,+Koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.
5 Munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamasoAkuyalira ukonde mapazi ake.+
6 Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+Koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+
7 Wolungama amafunitsitsa kuti anthu osauka aziweruzidwa mwachilungamo,+Koma woipa safuna kuchita zimenezi.+
8 Anthu odzitama ali ngati anthu amene amayatsa tauni,+Koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+
9 Munthu wanzeru akayamba kukangana ndi chitsiru,Pamangokhala phokoso ndi kunyozana, ndipo munthu wanzeruyo sapindula chilichonse.+
10 Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi munthu aliyense wosalakwa,+Ndipo amafuna kuchotsa moyo wa anthu owongoka mtima.*
11 Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse,+Koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.+
12 Wolamulira akamamvera mabodza,Antchito ake onse adzakhala oipa.+
13 Munthu wosauka komanso munthu wopondereza ena ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi:
Yehova amachititsa kuti maso a onsewa aziona kuwala.*
14 Mfumu ikamaweruza anthu osauka mwachilungamo,+Idzapitiriza kulamulira mpaka kalekale.+
15 Chikwapu* komanso kudzudzula nʼzimene zimapereka nzeru,+Koma mwana womulekerera amachititsa manyazi mayi ake.
16 Oipa akachuluka, machimo amachuluka,Koma olungama adzaona oipawo akugwa.+
17 Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumuloKomanso adzakusangalatsa kwambiri.+
18 Ngati anthu sakutsogoleredwa ndi Mulungu, amachita zinthu motayirira,+Koma osangalala ndi amene amatsatira chilamulo.+
19 Wantchito safuna kusintha ndi mawu okha,Chifukwa ngakhale atamvetsa mawuwo, safuna kuwatsatira.+
20 Kodi waona munthu amene amafulumira kulankhula asanaganize?+
Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa munthu ameneyu.+
21 Ngati munthu akusasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana,Mʼtsogolo adzakhala wosayamika.
22 Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano.+Aliyense amene sachedwa kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+
23 Kudzikuza kwa munthu kudzamutsitsa,+Koma amene ali ndi mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+
24 Amene amathandiza munthu wakuba amadzibweretsera mavuto.
Iye angamve kuitana kuti akapereke umboni,* koma osakanena chilichonse.+
25 Kuopa anthu ndi msampha,*+Koma amene amakhulupirira Yehova adzatetezedwa.+
26 Anthu ambiri amafunitsitsa kuonana ndi wolamulira,*Koma kwa Yehova nʼkumene munthu amapeza chilungamo.+
27 Munthu wopanda chilungamo ndi wonyansa kwa anthu olungama,+Koma munthu amene amachita zabwino ndi wonyansa kwa munthu woipa.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amene safuna kusintha.”
^ Mabaibulo ena amati, “Koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amakumana pamodzi.”
^ Kutanthauza kuti amawapatsa moyo.
^ Kapena kuti, “Chilango.”
^ Kapena kuti, “lumbiro limene linalinso ndi mawu otemberera.”
^ Kapena kuti, “kumatchera msampha.”
^ Mabaibulo ena amati, “amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima.”