Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Mlaliki

Machaputala

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12

Mitu

  • 1

    • Zinthu zonse nʼzachabechabe (1-11)

      • Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale (4)

      • Zinthu zamʼchilengedwe zimachitika mobwerezabwereza (5-7)

      • Palibe chatsopano padziko lapansi pano (9)

    • Nzeru za anthu nʼzoperewera (12-18)

      • Kuthamangitsa mphepo (14)

  • 2

    • Solomo anachita zinthu zosiyanasiyana (1-11)

    • Nzeru za anthu nʼzothandiza pangʼono (12-16)

    • Ntchito ya munthu wakhama imamubweretsera zowawa (17-23)

    • Idya, imwa ndipo sangalala ndi ntchito yako (24-26)

  • 3

    • Chilichonse chili ndi nthawi yake (1-8)

    • Kusangalala ndi moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu (9-15)

      • Anthu ali ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale (11)

    • Mulungu amaweruza anthu onse mwachilungamo (16, 17)

    • Anthu ndi nyama zonse zimafa (18-22)

      • Zonse zimabwerera kufumbi (20)

  • 4

    • Kuponderezedwa nʼkoipa kuposa imfa (1-3)

    • Kuona ntchito moyenera (4-6)

    • Ubwino wokhala ndi mnzako (7-12)

      • Awiri amaposa mmodzi (9)

    • Moyo wa wolamulira ungathe kukhala wachabechabe (13-16)

  • 5

    • Uziopa Mulungu moyenera (1-7)

    • Aliyense ali ndi amene amamuyangʼanira (8, 9)

    • Mavuto amene anthu achuma amakumana nawo (10-20)

      • Anthu okonda ndalama sakhutira (10)

      • Wantchito amagona tulo tokoma (12)

  • 6

    • Kukhala ndi zinthu koma osasangalala (1-6)

    • Muzisangalala ndi zinthu zimene muli nazo panopa (7-12)

  • 7

    • Mbiri yabwino komanso tsiku lomwalira (1-4)

    • Munthu wanzeru akamadzudzula (5-7)

    • Mapeto ndi abwino kuposa chiyambi (8-10)

    • Ubwino wa nzeru (11, 12)

    • Masiku abwino komanso masiku oipa (13-15)

    • Musamachite zinthu mopitirira muyezo (16-22)

    • Zimene wosonkhanitsa anthu anaona (23-29)

  • 8

    • Kulamulidwa ndi anthu omwe si angwiro (1-17)

      • Muzimvera zimene mfumu yalamula (2-4)

      • Munthu amapweteka munthu mnzake pomulamulira (9)

      • Chilango chikapanda kuperekedwa mwamsanga (11)

      • Idya, imwa komanso usangalale (15)

  • 9

    • Anthu onse mapeto awo ndi ofanana (1-3)

    • Uzisangalala ndi moyo ngakhale kuti udzafa (4-12)

      • Akufa sadziwa chilichonse (5)

      • Ku Manda kulibe kugwira ntchito (10)

      • Nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka (11)

    • Si nthawi zonse pamene anthu amayamikira munthu wanzeru (13-18)

  • 10

    • Uchitsiru pangʼono umawononga mbiri ya munthu wanzeru  (1)

    • Kuopsa kokhala munthu wosadalirika (2-11)

    • Zinthu zomvetsa chisoni zimene zimachitikira munthu wopusa (12-15)

    • Zinthu zopusa zimene olamulira amachita (16-20)

      • Mbalame ikhoza kukaulula zimene wanena (20)

  • 11

    • Uzigwiritsa ntchito mwayi umene uli nawo mwanzeru (1-8)

      • Ponya mkate wako pamadzi (1)

      • Dzala mbewu zako mʼmawa mpaka madzulo (6)

    • Sangalala moyenera ndi unyamata wako (9, 10)

  • 12

    • Uzikumbukira Mlengi usanakalambe (1-8)

    • Mawu omaliza a wosonkhanitsa anthu (9-14)

      • Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ngʼombe (11)

      • Opa Mulungu woona (13)