Mlaliki 10:1-20

  • Uchitsiru pangʼono umawononga mbiri ya munthu wanzeru  (1)

  • Kuopsa kokhala munthu wosadalirika (2-11)

  • Zinthu zomvetsa chisoni zimene zimachitikira munthu wopusa (12-15)

  • Zinthu zopusa zimene olamulira amachita (16-20)

    • Mbalame ikhoza kukaulula zimene wanena (20)

10  Ntchentche zakufa nʼzimene zimachititsa kuti mafuta a munthu wopanga mafuta onunkhira awole nʼkuyamba kununkha. Mofanana ndi zimenezi uchitsiru pangʼono umawononga mbiri ya munthu amene amaoneka kuti ndi wanzeru komanso wolemekezeka.+ 2  Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera njira yoyenera,* koma mtima wa munthu wopusa umamutsogolera njira yolakwika.*+ 3  Mʼnjira iliyonse imene munthu wopusa amayenda, amachita zinthu mopanda nzeru,*+ ndipo amaonetsetsa kuti aliyense adziwe kuti iye ndi wopusa.+ 4  Mkwiyo* wa mtsogoleri ukakuyakira, usachoke pamalo ako,+ chifukwa kudekha kumachepetsa machimo aakulu.+ 5  Pali chinthu china chomvetsa chisoni chimene ndaona padziko lapansi pano, zinthu zimene olamulira amalakwitsa:+ 6  Zitsiru zaikidwa pamaudindo ambiri akuluakulu, koma anthu oyenerera* amangokhala pamalo otsika. 7  Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi, koma akalonga akuyenda wapansi ngati antchito.+ 8  Amene akukumba dzenje angathe kugweramo+ ndipo amene akugumula mpanda wamiyala angathe kulumidwa ndi njoka. 9  Amene akuphwanya miyala, akhoza kudzipweteka nayo ndipo amene akuwaza nkhuni akhoza kuvulazidwa nazo.* 10  Ngati nkhwangwa yabunthwa ndipo munthu sanainole, adzafunika kugwiritsa ntchito mphamvu zambiri. Koma nzeru zimathandiza kuti zinthu ziyende bwino. 11  Njoka ikaluma munthu asanainyengerere bwinobwino kuti aiseweretse, ndiye kuti luso la katswiri woseweretsa njokayo lilibe phindu. 12  Mawu otuluka mʼkamwa mwa munthu wanzeru amakhala osangalatsa,+ koma milomo ya munthu wopusa imamubweretsera mavuto.+ 13  Mawu oyamba otuluka mʼkamwa mwake amakhala opusa+ ndipo mawu ake omaliza amakhala misala yobweretsa chiwonongeko. 14  Ngakhale zili choncho, munthu wopusa amangolankhulabe.+ Munthu sadziwa chimene chidzachitike. Ndi ndani amene angamuuze zimene zidzachitike iye atafa?+ 15  Ntchito imene munthu wopusa amagwira mwakhama imamutopetsa, chifukwa sadziwa nʼkomwe njira yopitira mumzinda. 16  Zimakhala zomvetsa chisoni ngati mfumu imene ikulamulira mʼdziko ndi mnyamata+ ndipo ngati akalonga ake amayamba mʼmawa kuchita madyerero. 17  Zimakhala zosangalatsa ngati mfumu imene ikulamulira mʼdziko ndi mwana wochokera kubanja lachifumu ndipo akalonga amadya pa nthawi yake kuti apeze mphamvu, osati nʼcholinga choti aledzere.+ 18  Chifukwa cha ulesi waukulu denga limaloshoka, ndipo chifukwa cha kuchita manja lende nyumba imadontha.+ 19  Chakudya chimachititsa kuti anthu aziseka, ndipo vinyo amachititsa kuti moyo ukhale wosangalatsa,+ koma ndalama zimathandiza munthu kupeza chilichonse chimene akufuna.+ 20  Ngakhale mʼmaganizo mwako,* usatemberere* mfumu+ ndipo usatemberere munthu wolemera kuchipinda kwako. Chifukwa mbalame* ikhoza kutenga mawu ako* kapena cholengedwa chokhala ndi mapiko chikhoza kukaulula zimene wanenazo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “uli kudzanja lake lamanja.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “uli kudzanja lake lamanzere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wake ulibe nzeru.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu; Mpweya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu olemera.”
Mabaibulo ena amati, “aziwaza mosamala.”
Mabaibulo ena amati, “Ngakhale pamene uli pabedi pako.”
Kapena kuti, “usafunire zoipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “cholengedwa chouluka chamumlengalenga.”
Kapena kuti, “uthenga wako.”