Mlaliki 11:1-10
11 Ponya* mkate wako pamadzi+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+
2 Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7 kapena 8+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.
3 Mitambo ikadzaza madzi, imakhuthulira mvula yochuluka padziko lapansi, ndipo mtengo ukagwera kumʼmwera kapena kumpoto, pamene wagwerapo udzakhala pomwepo.
4 Munthu amene amayangʼana mphepo sadzadzala mbewu ndipo amene amayangʼana mitambo sadzakolola.+
5 Iwe sudziwa mmene mzimu umachititsira kuti mafupa a mwana amene ali mʼmimba mwa mayi ake akule.+ Mofanana ndi zimenezi sudziwanso ntchito ya Mulungu woona, amene amachita zinthu zonse.+
6 Dzala mbewu zako mʼmawa ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo,+ chifukwa sukudziwa zimene zidzachite bwino, kaya izi kapena zinazo, kapenanso ngati zonse zidzachite bwino.
7 Kuwala nʼkokoma ndipo ndi bwino kuti maso aone dzuwa.
8 Ngati munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, azisangalala pa zaka zonsezo.+ Koma azikumbukira kuti masiku a mdima akhoza kukhala ambiri. Zonse zimene zikubwera nʼzachabechabe.+
9 Mnyamata iwe, sangalala pa nthawi imene uli wachinyamata, ndipo mtima wako usangalale masiku a unyamata wako. Uzichita zimene mtima wako ukufuna ndipo uzipita kumene maso ako akukutsogolera. Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza* pa zinthu zonsezi.+
10 Choncho chotsa zinthu zobweretsa mavuto mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku zinthu zimene zingakuvulaze, chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo nʼzachabechabe.+