Mlaliki 5:1-20
5 Uzisamala mmene ukuyendera ukapita kunyumba ya Mulungu woona.+ Ndi bwino kuti ukapita kumeneko uzikamvetsera,+ kusiyana ndi kukapereka nsembe ngati mmene anthu opusa amachitira+ chifukwa iwo sakudziwa kuti zimene akuchita nʼzoipa.
2 Usamapupulume kulankhula kapena kulola kuti mtima wako ufulumire kulankhula pamaso pa Mulungu woona,+ chifukwa Mulungu woona ali kumwamba koma iwe uli padziko lapansi. Nʼchifukwa chake suyenera kulankhula zambiri.+
3 Maloto amabwera chifukwa chochuluka zochita,*+ ndipo munthu wopusa akamalankhula zinthu zambiri, zimachititsa kuti alankhule zinthu zopanda pake.+
4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+
5 Ndi bwino kuti usalonjeze kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.+
6 Usalole kuti pakamwa pako pakuchimwitse,+ komanso usamauze mngelo* kuti unalakwitsa.+ Nʼchifukwa chiyani ukufuna kukwiyitsa Mulungu woona ndi zonena zako mpaka kufika poti awononge ntchito ya manja ako?+
7 Pajatu zochita zikachuluka zimachititsa kuti munthu azingolota.+ Mofanana ndi zimenezi, mawu akachuluka zotsatira zake zimakhala zachabechabe. Koma uziopa Mulungu woona.+
8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zopanda chilungamo zikuchitika mʼdera limene ukukhala, usadabwe nazo.+ Chifukwa munthu waudindoyo akuonedwa ndi wina waudindo waukulu kuposa iyeyo. Ndipo pali enanso amene ali ndi udindo waukulu kuposa onsewo.
9 Komanso, onsewo amapindula ndi zimene dzikoli limatulutsa. Ngakhale zimene mfumu imadya zimachokera kumunda.+
10 Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.+ Zimenezinso nʼzachabechabe.+
11 Zinthu zabwino zikachuluka ozidya amachulukanso.+ Ndipo kodi mwiniwake wa zinthuzo amapindula chiyani kuposa kumangoziyangʼana ndi maso ake?+
12 Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma, kaya adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.
13 Pali chinthu* chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndaona padziko lapansi pano: Munthu ankangosonkhanitsa chuma koma pambuyo pake chinamupweteketsa.
14 Chumacho chinatha chifukwa cha zinthu zina* zimene sizinayende bwino, ndipo atabereka mwana, analibe chilichonse choti amusiyire ngati cholowa.+
15 Monga mmene munthu anabadwira kuchokera mʼmimba mwa mayi ake, adzapitanso wamaliseche ngati mmene anabwerera.+ Ndipo sangatenge chilichonse pa ntchito yake imene anaigwira mwakhama.+
16 Palinso chinthu china chomvetsa chisoni kwambiri:* Monga mmene munthu anabwerera, adzapitanso chimodzimodzi. Ndipo kodi munthu amene amagwira ntchito mwakhama koma zonse nʼkungopita ndi mphepo amapindula chiyani?+
17 Komanso, tsiku lililonse amadya chakudya chake mumdima ndipo amakhala ndi nkhawa zambiri, amadwala komanso amakhala wokwiya.+
18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso choyenera chimene ine ndaona nʼchakuti: Munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala+ chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku ochepa a moyo wake amene Mulungu woona wamupatsa. Chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.*+
19 Komanso Mulungu woona akapatsa munthu chuma ndiponso zinthu zambiri+ zimene angathe kusangalala nazo, ayenera kulandira mphoto yake* ndi kusangalala chifukwa cha ntchito imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+
20 Adzaona kuti masiku a moyo wake akudutsa mofulumira kwambiri, chifukwa Mulungu woona adzamuchititsa kuti akhale wotanganidwa ndi zinthu zimene mtima wake umasangalala nazo.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “chifukwa cha zinthu zambiri zofunika kuzisamalira.”
^ Kapena kuti, “mthenga.”
^ Kapena kuti, “Pali tsoka lalikulu limene.”
^ Kapena kuti, “chifukwa cha ntchito.”
^ Kapena kuti, “Palinso tsoka lina lalikulu kwambiri.”
^ Kapena kuti, “Chifukwa limenelo ndi gawo lake.”
^ Kapena kuti, “kulandira gawo lake.”