Mlaliki 7:1-29

  • Mbiri yabwino komanso tsiku lomwalira (1-4)

  • Munthu wanzeru akamadzudzula (5-7)

  • Mapeto ndi abwino kuposa chiyambi (8-10)

  • Ubwino wa nzeru (11, 12)

  • Masiku abwino komanso masiku oipa (13-15)

  • Musamachite zinthu mopitirira muyezo (16-22)

  • Zimene wosonkhanitsa anthu anaona (23-29)

7  Mbiri yabwino imaposa* mafuta amtengo wapatali,+ ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa. 2  Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero,+ chifukwa amenewo ndi mapeto a munthu aliyense, ndipo amene ali ndi moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake. 3  Ndi bwino kumva chisoni kusiyana ndi kuseka,+ chifukwa chisoni chimachititsa kuti munthu akhale ndi mtima wabwino.+ 4  Munthu wanzeru amene ali mʼnyumba yamaliro, amaganizira mozama za moyo ndi imfa. Koma munthu wopusa, nthawi zonse amaganizira za zisangalalo.+ 5  Ndi bwino kumvetsera munthu wanzeru akamakudzudzula,+ kusiyana ndi kumvetsera nyimbo ya zitsiru. 6  Kuseka kwa anthu opusa kuli ngati kuthetheka kwa minga zomwe zikuyaka pansi pa mphika.+ Zimenezinso nʼzachabechabe. 7  Koma kuponderezedwa kungapangitse munthu wanzeru kuchita zinthu ngati wamisala, ndipo chiphuphu chimawononga mtima wa munthu.+ 8  Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake. Ndipo kukhala woleza mtima ndi kwabwino kuposa kukhala wodzikuza.+ 9  Usamafulumire kukwiya,+ chifukwa anthu opusa ndi amene sachedwa kukwiya.*+ 10  Usanene kuti, “Nʼchifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?” chifukwa si nzeru kufunsa funso ngati limeneli.+ 11  Munthu wanzeru akalandira cholowa zimakhala bwino, ndipo nzeru zimapindulitsa anthu amene ali padziko lapansi.* 12  Chifukwa nzeru zimateteza+ mofanana ndi mmene ndalama zimatetezera.+ Koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi uwu: Nzeru zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeruzo.+ 13  Ganizira ntchito ya Mulungu woona, chifukwa ndi ndani amene angathe kuwongola zinthu zimene iye anazikhotetsa?+ 14  Pa tsiku labwino, uzichitanso zinthu zabwino.+ Koma pa tsiku latsoka uzikumbukira kuti Mulungu woona anapanga masiku onsewa+ nʼcholinga choti anthu asamadziwe chilichonse chimene chidzawachitikire mʼtsogolo.+ 15  Pa moyo wanga wopanda pakewu,+ ndaona chilichonse. Ndaona munthu wolungama amene amawonongeka akuchita zinthu zolungama,+ komanso ndaona munthu woipa amene amakhala ndi moyo wautali ngakhale kuti akuchita zoipa.+ 16  Usakhale wolungama mopitirira muyezo+ kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri.+ Nʼchifukwa chiyani ukufuna kudzibweretsera mavuto?+ 17  Usakhale woipa mopitirira muyezo kapena kukhala wopusa.+ Uferenji mwamsanga?+ 18  Ndi bwino kwambiri kuti usunge malangizo onsewa, usasiyepo ena.+ Chifukwa munthu amene amaopa Mulungu adzamvera malangizo onsewa. 19  Nzeru zimapangitsa kuti munthu wanzeru akhale wamphamvu kwambiri kuposa amuna 10 amphamvu amene ali mumzinda.+ 20  Chifukwa padziko lapansi palibe munthu wolungama amene amachita zabwino nthawi zonse ndipo sachimwa.+ 21  Komanso usamaganizire kwambiri mawu aliwonse amene anthu akulankhula.+ Ukamachita zimenezi ukhoza kumva wantchito wako akukunenera zoipa,* 22  chifukwa iweyo ukudziwa bwino mumtima mwako kuti wanenerapo anthu ena zoipa kambirimbiri.+ 23  Ndinaganizira zinthu zonsezi mwanzeru ndipo ndinati: “Ndidzakhala wanzeru.” Koma zinali zosatheka kuti ndipeze nzeruzo. 24  Zimene zinachitika kale sitingathe kuzimvetsa ndipo nʼzozama kwambiri. Ndi ndani angazimvetse?+ 25  Mumtima mwanga ndinasankha kuti ndidziwe, ndifufuze ndiponso ndifunefune nzeru komanso chifukwa chake zinthu zinazake zimachitika. Ndinafunanso kumvetsa kuti uchitsiru ndi woipa bwanji komanso makhalidwe opusa a anthu amene amachita zinthu ngati amisala.+ 26  Ndiye ndinapeza izi: Mkazi amene ali ngati ukonde wosakira nyama, amene mtima wake uli ngati khoka, komanso amene manja ake ali ngati unyolo wakundende, ndi wowawa kwambiri kuposa imfa. Munthu amene amasangalatsa Mulungu woona adzamuthawa,+ koma wochimwa amagwidwa naye.+ 27  Wosonkhanitsa anthu akunena kuti: “Taona, izi ndi zimene ndapeza.+ Ndafufuza chinthu chimodzi ndi chimodzi kuti ndidziwe zimenezi, 28  koma chimene ndinkachifufuza kwambiri sindinachipeze. Pa anthu 1,000, ndinapezapo mwamuna mmodzi yekha wolungama,* koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi wolungama. 29  Zimene ndapeza ndi izi zokha: Mulungu woona anapanga anthu owongoka mtima,+ koma anthuwo asankha kuchita zinthu zogwirizana ndi zolinga zawo.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzina limaposa.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa kukwiya ndi chizindikiro cha anthu opusa.”
Kapena kuti, “amene ali ndi moyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akukutemberera.”
Kapena kuti, “wowongoka mtima.”