Nehemiya 11:1-36
-
Anthu anayambiranso kukhala ku Yerusalemu (1-36)
11 Akalonga a anthuwo ankakhala ku Yerusalemu.+ Anthu ena onse anachita maere+ kuti apeze munthu mmodzi pa anthu 10 alionse woti akakhale ku Yerusalemu, mzinda woyera, ndipo anthu 9 otsalawo ankakhala mʼmizinda ina.
2 Komanso anthu anadalitsa amuna onse amene anadzipereka kukakhala ku Yerusalemu.
3 Otsatirawa ndi atsogoleri a chigawo cha Yuda amene ankakhala ku Yerusalemu, (Aisiraeli ena onse, ansembe, Alevi, atumiki apakachisi*+ ndiponso ana a atumiki a Solomo+ ankakhala mʼmizinda ina ya Yuda. Aliyense ankakhala pamalo ake mumzinda wake.+
4 Ku Yerusalemu kunkakhalanso anthu ena a fuko la Yuda ndi la Benjamini.) Anthu a fuko la Yudawo anali Ataya mwana wa Uziya. Uziyayo anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Sefatiya, Sefatiya anali mwana wa Mahalalele wochokera mʼbanja la Perezi.+
5 Panalinso Maaseya mwana wa Baruki amene anali mwana wa Kolihoze. Kolihoze anali mwana wa Hazaya, Hazaya anali mwana wa Adaya, Adaya anali mwana wa Yoyaribi, Yoyaribi anali mwana wa Zekariya mbadwa ya Shela.
6 Ana onse a Perezi amene ankakhala ku Yerusalemu anali amuna amphamvu okwana 468.
7 Anthu a fuko la Benjamini anali awa: Salelu+ mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Yoedi, Yoedi anali mwana wa Pedaya, Pedaya anali mwana wa Kolaya, Kolaya anali mwana wa Maaseya, Maaseya anali mwana wa Itiyeli ndipo Itiyeli anali mwana wa Yesaiya.
8 Pambuyo pa Salelu panali Gabai ndi Salai ndipo onse pamodzi analipo 928.
9 Yoweli mwana wa Zikiri anali woyangʼanira wawo ndipo Yuda mwana wa Hasenuwa anali wachiwiri kwa woyangʼanira mzinda.
10 Pagulu la ansembe panali awa: Yedaya mwana wa Yoyaribi, Yakini,+
11 Seraya mwana wa Hilikiya. Hilikiya anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Merayoti, Merayoti anali mwana wa Ahitubu,+ mtsogoleri wa panyumba* ya Mulungu woona.
12 Abale awo omwe ankagwira ntchito panyumbapo analipo 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu. Yerohamu anali mwana wa Pelaliya, Pelaliya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Pasuri+ ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya.
13 Abale ake a Adaya, atsogoleri a nyumba za makolo awo, analipo 242. Ndiyeno panalinso Amasisai mwana wa Azareli. Azareli anali mwana wa Azai, Azai anali mwana wa Mesilemoti amene anali mwana wa Imeri.
14 Amasisai pamodzi ndi abale ake, amuna amphamvu ndiponso olimba mtima, analipo okwana 128. Iwowa mtsogoleri wawo anali Zabidiyeli wochokera mʼbanja lotchuka.
15 Pagulu la Alevi panali awa: Semaya+ mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu, Azirikamu anali mwana wa Hasabiya ndipo Hasabiya anali mwana wa Buni.
16 Panalinso Sabetai+ ndi Yozabadi,+ omwe anali mʼgulu la atsogoleri a Alevi. Amenewa ankayangʼanira ntchito yapanja pa nyumba ya Mulungu woona.
17 Komanso panali Mataniya+ mwana wa Mika ndipo Mika anali mwana wa Zabidi. Zabidi anali mwana wa Asafu,+ yemwe anali mtsogoleri wa nyimbo zotamanda Mulungu. Iye ankatsogolera potamanda Mulungu pa nthawi ya pemphero.+ Bakibukiya anali wachiwiri wake poyangʼanira abale ake. Panalinso Abada mwana wa Samuwa, Samuwa anali mwana wa Galali ndipo Galali anali mwana wa Yedutuni.+
18 Alevi onse amene ankakhala mumzinda woyera analipo 284.
19 Alonda apageti anali Akubu, Talimoni+ ndi abale awo amene ankalondera mʼmageti. Onse pamodzi analipo 172.
20 Aisiraeli ena onse komanso ansembe ndi Alevi ena onse, anali mʼmizinda ina ya Yuda, aliyense pacholowa chake.
21 Atumiki apakachisi*+ ankakhala ku Ofeli+ ndipo Ziha ndi Gisipa ankayangʼanira atumiki apakachisiwo.
22 Woyangʼanira Alevi ku Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani. Bani anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Mataniya,+ Mataniya anali mwana wa Mika wa mʼbanja la Asafu ndipo a mʼbanja la Asafu anali oimba. Uzi ankayangʼanira ntchito yapanyumba ya Mulungu woona
23 Mfumu inapereka lamulo lokhudza oimba,+ ndipo panali dongosolo loti aziwapatsa thandizo tsiku lililonse mogwirizana ndi zofunikira za tsikulo.
24 Petahiya mwana wa Mesezabele, wa mʼbanja la Zera mwana wa Yuda, anali mlangizi wa mfumu pa nkhani zonse zokhudza anthu.
25 Ayuda ena ankakhala mʼmidzi ndi mʼmadera ozungulira midziyo. Ena ankakhala ku Kiriyati-ariba+ ndi midzi yake yozungulira, ku Diboni ndi midzi yake yozungulira, ku Yekabizeeli+ ndi midzi yake yozungulira,
26 ku Yesuwa, ku Molada,+ ku Beti-peleti,+
27 ku Hazara-suali,+ ku Beere-seba ndi midzi yake yozungulira,
28 ku Zikilaga,+ ku Mekona ndi midzi yake yozungulira,
29 ku Eni-rimoni,+ ku Zora,+ ku Yarimuti,
30 ku Zanowa,+ ku Adulamu ndi midzi yake yozungulira, ku Lakisi+ ndi madera ake ozungulira ndiponso ku Azeka+ ndi midzi yake yozungulira. Iwo anakhala* kuyambira ku Beere-seba mpaka kuchigwa cha Hinomu.+
31 Anthu a fuko la Benjamini anakhala ku Geba,+ ku Mikimasi, ku Aiya, ku Beteli+ ndi midzi yake yozungulira,
32 ku Anatoti,+ ku Nobu,+ ku Ananiya,
33 ku Hazori, ku Rama,+ ku Gitaimu,
34 ku Hadidi, ku Zeboyimu, ku Nebalati,
35 ku Lodi ndiponso ku Ono,+ chigwa cha amisiri.
36 Ndipo Alevi ena ochokera ku Yuda anapatsidwa malo ku Benjamini.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “wapakachisi.”
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “anamanga misasa.”