Numeri 34:1-29
34 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti:
2 “Upereke malangizo awa kwa Aisiraeli: ‘Awa ndi malire a dziko la Kanani, dziko limene ndidzakupatseni kuti likhale cholowa chanu.+
3 Malire a dziko lanu mbali yakumʼmwera adzayambire kuchipululu cha Zini, malire ndi Edomu. Malire anu akumʼmwera, mbali yakumʼmawa, adzayambire kumene Nyanja Yamchere* yathera.+
4 Malirewo adzakhota nʼkukadutsa kumʼmwera kwa chitunda cha Akirabimu+ kulowera ku Zini, nʼkukathera kumʼmwera kwa Kadesi-barinea.+ Kenako akakhotere ku Hazara-adara+ nʼkukafika ku Azimoni.
5 Ndiyeno kuchokera ku Azimoni, malirewo akalowere kuchigwa cha Iguputo* mpaka kukathera ku Nyanja Yaikulu.*+
6 Malire anu a mbali yakumadzulo akakhale gombe la Nyanja Yaikulu.* Amenewa akakhale malire anu a mbali yakumadzulo.+
7 Malire anu akumpoto akayende motere: Mukalembe malirewo kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kuphiri la Hora.+
8 Kuchokera kuphiri la Hora, mukalembe malirewo mpaka kukafika ku Lebo-hamati,*+ ndipo malirewo akathere ku Zedadi.+
9 Malirewo akafike ku Zifironi, mpaka kukathera ku Hazara-enani.+ Malire anu a mbali yakumpoto akakhale amenewa.
10 Ndiyeno mukalembe malire anu a kumʼmawa kuyambira ku Hazara-enani mpaka ku Sefamu.
11 Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kumʼmawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akadutse pamalo otsetsereka akumʼmawa kwa Nyanja ya Kinereti.*+
12 Malirewo akatsike ndithu mpaka kumtsinje wa Yorodano, ndipo akathere ku Nyanja Yamchere.+ Limeneli ndi limene lidzakhale dziko lanu+ ndi malire ake olizungulira.’”
13 Choncho Mose anauza Aisiraeli kuti: “Limeneli ndi dziko limene ligawidwe kwa inu pogwiritsa ntchito maere kuti likhale cholowa chanu.+ Lidzagawidwa kwa inu mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kuti liperekedwe kwa mafuko 9 ndi hafu.
14 Fuko la Rubeni potengera mabanja a makolo awo, fuko la Gadi potengera mabanja a makolo awo komanso hafu ya fuko la Manase, analandira kale cholowa chawo.+
15 Mafuko awiri ndi hafuwo analandira kale cholowa chawo kudera lakumʼmawa kwa Yorodano, moyangʼanizana ndi Yeriko.”+
16 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
17 “Amuna amene akakugawireni malo kuti akhale cholowa chanu, mayina awo ndi awa: Wansembe Eleazara+ ndi Yoswa+ mwana wa Nuni.
18 Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse kuti akathandize kugawa malowo kuti akhale cholowa chanu.+
19 Amunawo mayina awo ndi awa: pa fuko la Yuda,+ Kalebe+ mwana wa Yefune,
20 pa fuko la ana a Simiyoni,+ Semuyeli mwana wa Amihudi,
21 pa fuko la Benjamini,+ Elidadi mwana wa Kisiloni,
22 pa fuko la ana a Dani,+ mtsogoleri Buki mwana wa Yogili,
23 pa ana a Yosefe+ ku fuko la ana a Manase,+ mtsogoleri Hanieli mwana wa Efodi,
24 pa fuko la ana a Efuraimu,+ mtsogoleri Kemueli mwana wa Sipitana,
25 pa fuko la ana a Zebuloni,+ mtsogoleri Elizafana mwana wa Paranaki,
26 pa fuko la ana a Isakara,+ mtsogoleri Palitiyeli mwana wa Azani,
27 pa fuko la ana a Aseri,+ mtsogoleri Ahihudi mwana wa Selomi,
28 ndipo pa fuko la ana a Nafitali,+ mtsogoleri Pedaheli mwana wa Amihudi.”
29 Amenewa ndi amuna amene Yehova anawalamula kuti akagawe malo kwa Aisiraeli mʼdziko la Kanani.+
Mawu a M'munsi
^ Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
^ Kapena kuti, “kukhwawa la Iguputo.”
^ Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.
^ Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
^ Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
^ Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti, kapena kuti Nyanja ya Galileya.