Nyimbo ya Solomo 1:1-17
-
Nyimbo yoposa nyimbo zonse (1)
-
Mtsikana (2-7)
-
Ana aakazi a ku Yerusalemu (8)
-
Mfumu (9-11)
-
“Ife tikupangira zokongoletsa zagolide” (11)
-
-
Mtsikana (12-14)
-
‘Wachikondi wanga ali ngati kathumba konunkhira ka mule’ (13)
-
-
Mʼbusa (15)
-
“Ndiwe wokongola wokondedwa wanga”
-
-
Mtsikana (16, 17)
-
“Iwenso ndiwe wooneka bwino, wachikondi wanga” (16)
-
1 Nyimbo yoposa nyimbo zonse, nyimbo ya Solomo:+
2 “Undikise ndi milomo yako,Chifukwa chikondi chimene umandisonyeza chimaposa vinyo.+
3 Kununkhira kwa mafuta ako ndi kosangalatsa.+
Dzina lako lili ngati mafuta onunkhira amene athiridwa pamutu.+
Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda.
4 Nditenge, tiye tithawe.
Chifukwatu mfumu yandipititsa mʼzipinda zake zamkati.
Tiye tikondwere komanso kusangalalira limodzi.
Tiye titamande* chikondi chimene umandisonyeza kuposa kutamanda vinyo.
Mpake kuti atsikana amakukonda.
5 Inu ana aakazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda koma wokongola,Ngati matenti a ku Kedara+ komanso nsalu za matenti+ a Solomo.
6 Musandiyangʼanitsitse chifukwa chakuti ndada,Ndi dzuwatu landidetsali.
Ana aamuna a mayi anga anandikwiyira.Choncho anandiika kuti ndiziyangʼanira minda ya mpesaMoti sindinathe kusamalira munda wanga wa mpesa.
7 Tandiuze, iwe amene ndimakukonda kwambiri,Ndiuze kumene umakadyetsera ziweto zako,+Kumene umakagonetsa ziweto masana.
Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu kumutu*Pakati pa magulu a ziweto za anzako?”
8 “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,Tsatira mapazi a ziwetoNdipo ukadyetse mbuzi zako zingʼonozingʼono pafupi ndi matenti a abusa.”
9 “Iwe wokondedwa wanga, kwa ine uli ngati hatchi yaikazi yapamagaleta a Farao.+
10 Masaya ako amaoneka bwino ukavala zodzikongoletsera,*Ndipo khosi lako limaoneka bwino ukavala mikanda.
11 Ife tikupangira zokongoletsa* zagolideZokhala ndi mikanda yasiliva.”
12 “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira,Mafuta anga onunkhira*+ akutulutsa kafungo kosangalatsa.
13 Wachikondi wanga ali ngati kathumba konunkhira ka mule* kwa ine.+Iye amakhala pakati pa mabere anga usiku wonse.
14 Kwa ine, wachikondi wanga ali ngati maluwa a hena+Mʼminda ya mpesa ya ku Eni-gedi.”+
15 “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga.
Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+
16 “Iwenso ndiwe wooneka bwino,* wachikondi wanga komanso ndiwe wosangalatsa.+
Bedi lathu ndi lamasamba ofewa.
17 Nyumba yathu* inamangidwa ndi mitengo ya mkungudza,Ndipo kudenga kwake kuli mitengo ya junipa.”*
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Tiye tikambirane za.”
^ Kapena kuti, “nsalu yovala kumutu polira maliro.”
^ Mabaibulo ena amati, “Masaya ako ndi okongola ndi nkhata zatsitsi.”
^ Kapena kuti, “zovala kumutu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Nado wanga.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndiwe wokongola.”
^ Kapena kuti, “Nyumba yathu yabwino kwambiri.”
^ Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.