Nyimbo ya Solomo 4:1-16

  • Mʼbusa (1-5)

    • “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga” (1)

  • Mtsikana (6)

  • Mʼbusa (7-16a)

    • ‘Watenga mtima wanga, mkwatibwi wanga’ (9)

  • Mtsikana (16b)

4  “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga. Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa munsalu yako yophimba kumutuyo. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuziZimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+  2  Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe angozimeta kumene,Zimene zikuchokera kosambitsidwa,Zonse zabereka mapasa,Ndipo palibe imene ana ake afa.  3  Milomo yako ili ngati chingwe chofiira kwambiri,Ndipo ukamalankhula umasangalatsa. Masaya ako munsalu yako yophimba kumutuyoAli ngati khangaza* logamphula pakati.  4  Khosi lako+ lili ngati nsanja ya Davide,+Yomangidwa ndi miyala yokhala mʼmizeremizere,Pamene akolekapo zishango 1,000,Zishango zonse zozungulira za amuna amphamvu.+  5  Mabere ako awiri ali ngati ana awiri a insaNgati ana amapasa a insa,+Amene akudya msipu pakati pa maluwa.”  6  “Mpaka kunja kutayamba kuwomba kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka,Ndipita kuphiri la muleNdiponso kuzitunda za lubani.”+  7  “Ndiwe wokongola paliponse, wokondedwa wanga,+Ndipo ulibe chilema chilichonse.  8  Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni, iwe mkwatibwi wanga,Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni.+ Utsetsereke kuchokera pamwamba pa phiri la Amana,*Kuchokera pamwamba pa phiri la Seniri, kapena kuti pamwamba pa phiri la Herimoni.+Utsetsereke kuchokera mʼmapanga a mikango, ndiponso kuchokera kumapiri a akambuku.  9  Watenga mtima wanga,+ iwe mchemwali wanga, mkwatibwi wanga,Watenga mtima wanga utangondiyangʼana kamodzi kokha,Ndiponso ndi mkanda wa mʼkhosi mwako. 10  Chikondi chimene umandisonyeza nʼchokoma,+ iwe mchemwali wanga, mkwatibwi wanga. Chikondi chimene umandisonyeza nʼchabwino kuposa vinyo,+Ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola nʼkoposa zonunkhira zamitundu yonse.+ 11  Milomo yako imakha uchi wapachisa,+ iwe mkwatibwi wanga. Uchi ndi mkaka zili kuseri kwa lilime lako,+Ndipo kafungo konunkhira ka zovala zako kakumveka ngati kafungo konunkhira ka ku Lebanoni. 12  Mchemwali wanga, mkwatibwi wanga, ali ngati munda umene watsekedwa.Iye ali ngati munda umene watsekedwa, ndiponso ngati kasupe amene watsekedwa. 13  Uli ngati munda* wa mitengo imene nthambi zake zili ndi makangaza ambiriUmene uli ndi zipatso zabwino kwambiri, maluwa a hena ndi mitengo ya nado, 14  Nado,+ maluwa a safironi, mabango onunkhira,+ sinamoni,+Komanso mitengo yosiyanasiyana ya lubani, mule, aloye,+Ndi zonunkhira zonse zabwino kwambiri.+ 15  Uli ngati kasupe wamʼmunda, chitsime chamadzi abwino,Ndiponso timitsinje tochokera ku Lebanoni.+ 16  Dzuka, iwe mphepo yakumpoto.Bwera, iwe mphepo yakumʼmwera. Womba pamunda wanga. Kununkhira kwake kufalikire.” “Wachikondi wanga alowe mʼmunda wakeKuti adzadye zipatso zake zabwino kwambiri.”

Mawu a M'munsi

“Khangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Kapena kuti, “Anti-Lebanoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “paradaiso.”