Oweruza 1:1-36

  • Madera omwe Yuda ndi Simiyoni anagonjetsa (1-20)

  • Ayebusi anapitiriza kukhala ku Yerusalemu (21)

  • Yosefe anagonjetsa Beteli (22-26)

  • Akanani ena anasiyidwa (27-36)

1  Yoswa atamwalira,+ Aisiraeli* anafunsa Yehova kuti:+ “Ndani wa ife ayambe kupita kukamenyana ndi Akanani?” 2  Yehova anayankha kuti: “Ayambe Yuda,+ ndipo ndapereka* dzikolo mʼmanja mwake.” 3  Ndiyeno Yuda anauza mʼbale wake Simiyoni kuti: “Tiye tipitire limodzi mʼgawo langa+ kuti tikamenyane ndi Akanani. Kenako inenso ndidzapita nawe kugawo lako.” Choncho Simiyoni anapita naye. 4  Fuko la Yuda litapita, Yehova anapereka Akanani ndi Aperezi mʼmanja mwawo,+ moti anagonjetsa amuna 10,000 ku Bezeki. 5  Anapeza Adoni-bezeki ku Bezeki nʼkumenyana naye ndipo anagonjetsa Akanani+ ndi Aperezi.+ 6  Adoni-bezeki atayamba kuthawa, anamʼthamangitsa ndi kumʼgwira ndipo anamʼdula zala zazikulu zamʼmanja ndi zakumapazi. 7  Zitatero, Adoni-bezeki anati: “Pali mafumu 70 odulidwa zala zazikulu zamʼmanja ndi zakumapazi, amene ankatola chakudya pansi pa tebulo langa. Mulungu wandibwezera zimene ndinachita.” Kenako anamʼtengera ku Yerusalemu+ kumene anakafera. 8  Amuna a fuko la Yuda anamenyananso ndi mzinda wa Yerusalemu+ nʼkuulanda. Anapha anthu okhala mmenemo ndi lupanga, ndipo mzindawo anautentha ndi moto. 9  Kenako amuna a fuko la Yuda anapita kukamenyana ndi Akanani okhala mʼdera lamapiri, ku Negebu ndi ku Sefela.+ 10  Choncho fuko la Yuda linapita kukamenyana ndi Akanani amene ankakhala ku Heburoni, (poyamba dzina la mzinda wa Heburoni linali Kiriyati-ariba). Iwo anapha Sesai, Ahimani ndi Talimai.+ 11  Atachoka kumeneko anapita kukamenyana ndi anthu a mumzinda wa Debiri.+ (Poyamba dzina la mzinda wa Debiri linali Kiriyati-seferi.)+ 12  Kenako Kalebe+ anati: “Aliyense amene agonjetse mzinda wa Kiriyati-seferi nʼkuulanda, ndidzamʼpatsa mwana wanga Akisa, kuti akhale mkazi wake.”+ 13  Ndipo Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ mngʼono wake wa Kalebe, analanda mzindawo. Choncho Kalebe anamʼpatsa Akisa mwana wake kuti akhale mkazi wake. 14  Pamene Akisa ankapita kunyumba, anauza Otiniyeli kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo ake. Kenako Akisa anatsika pabulu.* Atatero, Kalebe anamufunsa kuti: “Ukufuna chiyani?” 15  Iye anapempha kuti: “Ndidalitseni, poti mwandipatsa malo akumʼmwera* mundipatsenso Guloti-maimu.”* Choncho Kalebe anamʼpatsa Guloti Wakumtunda ndi Guloti Wakumunsi. 16  Ndiyeno ana a munthu wamtundu wa Chikeni,+ yemwe anali mpongozi wa Mose,+ anatuluka mumzinda wa mitengo ya kanjedza+ pamodzi ndi anthu a ku Yuda nʼkukalowa mʼchipululu cha Yuda, kumʼmwera kwa Aradi.+ Ndipo iwo anayamba kukhala pamodzi ndi anthuwo.+ 17  Koma fuko la Yuda linayendabe ndi abale awo a fuko la Simiyoni, ndipo anapha Akanani okhala ku Zefati nʼkuwononga mzindawo.+ Choncho mzindawo anaupatsa dzina loti Horima.*+ 18  Kenako fuko la Yuda linalanda Gaza+ ndi madera ake, Asikeloni+ ndi madera ake ndiponso Ekironi+ ndi madera ake. 19  Yehova anali ndi fuko la Yuda moti linalanda dera lamapiri. Koma silinathe kuthamangitsa anthu okhala mʼchigwa chifukwa chakuti anthuwo anali ndi magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali komanso zakuthwa.+ 20  Anapereka Heburoni kwa Kalebe ngati mmene Mose analonjezera,+ ndipo Kalebe anathamangitsa ana atatu aamuna a Anaki+ amene ankakhala kumeneko. 21  Anthu a fuko la Benjamini sanathamangitse Ayebusi a ku Yerusalemu, moti Ayebusiwo akukhalabe ndi anthu a fuko la Benjamini ku Yerusalemu mpaka lero.+ 22  Pa nthawi imeneyi, ana a Yosefe+ anapita kukamenyana ndi mzinda wa Beteli ndipo Yehova anali nawo.+ 23  Ana a Yosefe anayamba kufufuza mmene angagonjetsere mzinda wa Beteli. (Poyamba dzina la mzindawu linali Luzi.)+ 24  Ndiyeno anthu amene ankafufuzawo anaona mwamuna wina akutuluka mumzindawo, ndipo anamuuza kuti: “Tiuze mmene tingalowere mumzinda, ndipo tikukomera mtima.”* 25  Iye anawauzadi mmene angalowere mumzindawo, ndipo iwo anapha anthu amumzindawo ndi lupanga, koma mwamunayo ndi anthu onse a mʼbanja lake sanawaphe.+ 26  Ndiyeno mwamunayo anapita kudziko la Ahiti ndi kumanga mzinda ndipo anaupatsa dzina loti Luzi. Limeneli ndi dzina la mzindawo mpaka lero. 27  Manase sanatenge mzinda wa Beti-seani ndi midzi yake yozungulira komanso Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira. Sanathamangitsenso anthu okhala mumzinda wa Dori ndi midzi yake yozungulira, anthu amumzinda wa Ibuleamu ndi midzi yake yozungulira ndi anthu okhala mumzinda wa Megido ndi midzi yake yozungulira.+ Akananiwo anakakamirabe kukhala mʼdziko limeneli. 28  Aisiraeli atakhala amphamvu, anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ koma sanawachotseretu onse mʼdzikolo.+ 29  Fuko la Efuraimu nalonso silinathamangitse Akanani amene ankakhala ku Gezeri, moti Akananiwo anapitiriza kukhala pakati pawo ku Gezeriko.+ 30  Fuko la Zebuloni silinathamangitse anthu okhala mumzinda wa Kitironi ndi mzinda wa Nahaloli,+ moti Akananiwo anapitiriza kukhala pakati pawo ndipo a fuko la Zebuloni anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo.+ 31  Fuko la Aseri silinathamangitse anthu okhala ku Ako ndi anthu okhala ku Sidoni,+ Alabu, Akizibu,+ Heliba, Afiki+ ndi ku Rehobu.+ 32  Choncho fuko la Aseri linapitiriza kukhala pakati pa Akanani amene ankakhala mʼdzikolo, chifukwa sanawathamangitse. 33  Fuko la Nafitali silinathamangitse anthu okhala mʼmizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati,+ koma iwo anapitiriza kukhala pakati pa Akanani akumeneko.+ Ndipo fuko la Nafitali linayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo anthu okhala mʼmizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati. 34  Aamori ankapanikizira anthu a fuko la Dani kudera lamapiri ndipo sanawalole kutsikira mʼchigwa.+ 35  Choncho Aamori anakakamira kukhala mʼphiri la Herese ndi mʼmizinda ya Aijaloni+ ndi Saalibimu.+ Koma ana a Yosefe atayamba kukula mphamvu, anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Aamoriwo. 36  Dera la Aamori linayambira kuchitunda cha Akirabimu,+ komanso ku Sela kupita chakumtunda.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Kapena kuti, “ndikupereka.”
Mabaibulo ena amati, “anawomba mʼmanja ali pabulu.”
Kapena kuti, “Negebu.”
Kutanthauza “Mabeseni a Madzi.”
Kutanthauza “Kuwononga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tikusonyeza chikondi chokhulupirika.”