Oweruza 10:1-18

  • Oweruza Tola ndi Yaeli (1-5)

  • Aisiraeli anasiya Mulungu kenako nʼkulapa (6-16)

  • Aamoni anaopseza Aisiraeli (17, 18)

10  Abimeleki atafa, panabwera Tola, mwana wa Puwa amene anali mwana wa Dodo wa fuko la Isakara ndipo anapulumutsa Isiraeli.+ Iye ankakhala ku Samiri mʼdera lamapiri la Efuraimu. 2  Tola anaweruza Isiraeli zaka 23. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa ku Samiri. 3  Tola atamwalira, panabwera Yairi wa ku Giliyadi ndipo anaweruza Isiraeli zaka 22. 4  Iye anali ndi ana 30 aamuna amene ankayenda pa abulu 30, ndipo iwo anali ndi mizinda 30. Mpaka lero mizinda imeneyi imadziwikabe kuti Havoti-yairi+ ndipo ili ku Giliyadi. 5  Kenako Yairi anamwalira ndipo anaikidwa ku Kamoni. 6  Aisiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ mafano a Asitoreti, milungu ya ku Aramu,* milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya Aamoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Iwo anasiya Yehova ndipo sankamutumikira. 7  Zitatero, Yehova anakwiyira kwambiri Aisiraeli moti anawapereka* kwa Afilisiti ndi kwa Aamoni.+ 8  Choncho, anthu amenewa anazunza ndi kupondereza kwambiri Aisiraeli chaka chimenecho. Kwa zaka 18, anapondereza Aisiraeli onse amene anali kumʼmawa kwa Yorodano, mʼdziko la Aamori limene linali ku Giliyadi. 9  Aamoni ankawolokanso Yorodano kukamenyana ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndi la Efuraimu, moti Aisiraeli ankavutika kwambiri. 10  Zitatero Aisiraeli anapempha Yehova kuti awathandize.+ Iwo anati: “Takuchimwirani inu Mulungu wathu, chifukwa tinakusiyani nʼkuyamba kutumikira Abaala.”+ 11  Koma Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Kodi sindinakupulumutseni pamene Aiguputo,+ Aamori,+ Aamoni, Afilisiti,+ 12  Asidoni, Aamaleki ndi Amidiyani ankakuponderezani? Inu mutandilirira ndinakupulumutsani mʼmanja mwawo. 13  Koma munandisiya nʼkuyamba kutumikira milungu ina.+ Nʼchifukwa chake sindikupulumutsaninso.+ 14  Pitani, mukapemphe thandizo kwa milungu imene mwasankhayo.+ Milungu imeneyoyo ikupulumutseni pa nthawi imene mukuvutikayi.”+ 15  Koma Aisiraeli anauza Yehova kuti: “Tachimwa. Inuyo mutichite chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino. Koma panopa chonde tipulumutseni.” 16  Atatero, iwo anachotsa milungu yonse yachilendo imene anali nayo ndipo anayamba kutumikira Yehova,+ moti iye sanalole kuti Aisiraeli apitirize kuvutika.+ 17  Patapita nthawi, Aamoni+ anasonkhana nʼkumanga msasa wawo ku Giliyadi. Zitatero, Aisiraeli nawonso anasonkhana nʼkumanga msasa wawo ku Mizipa. 18  Ndiyeno anthu ndi akalonga a Giliyadi anayamba kufunsana kuti: “Ndani atitsogolere kukamenyana ndi Aamoni?+ Ameneyo akhale mtsogoleri wa anthu onse okhala mʼGiliyadi.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Siriya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anawagulitsa.”