Oweruza 21:1-25

  • Fuko la Benjamini linapulumutsidwa (1-25)

21  Tsopano amuna a Isiraeli analumbira ku Mizipa+ kuti: “Aliyense wa ife sadzapereka mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.”+ 2  Ndiyeno anthuwo anapita ku Beteli+ nʼkukhala pansi pamaso pa Mulungu woona mpaka madzulo. Iwo ankalira kwambiri mofuula. 3  Iwo ankanena kuti: “Nʼchifukwa chiyani zimenezi zachitika mu Isiraeli, inu Yehova Mulungu wa Isiraeli? Nʼchifukwa chiyani lero fuko limodzi lasowa mu Isiraeli?” 4  Ndiyeno tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka mʼmawa nʼkumanga guwa lansembe ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano.+ 5  Kenako Aisiraeli anati: “Pa mafuko onse a Isiraeli ndi ndani sanabwere kudzasonkhana pamaso pa Yehova?” Popeza anali atalumbira kuti aliyense amene sabwera kwa Yehova ku Mizipa, aphedwe ndithu. 6  Aisiraeli anayamba kumva chisoni chifukwa cha zimene zinachitikira mchimwene wawo Benjamini. Iwo anati: “Lero fuko limodzi ladulidwa ndi kuchotsedwa mu Isiraeli. 7  Titani kuti tiwapezere akazi anthu amene atsalawa, popeza tinalumbira pamaso pa Yehova+ kuti sitiwapatsa ana athu aakazi kuti akhale akazi awo?”+ 8  Anayamba kufunsana kuti: “Pa mafuko onse a Isiraeli ndi ndani sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?”+ Ndiyeno anaona kuti panalibe aliyense wochokera ku Yabesi-giliyadi amene anabwera kumsasa kumene kunali mpingowo. 9  Atawerenga anthuwo, anaona kuti panalibe aliyense wochokera ku Yabesi-giliyadi. 10  Choncho gulu la Aisiraelilo linatumiza amuna amphamvu kwambiri okwana 12,000. Anawalamula kuti: “Pitani, mukaphe ndi lupanga anthu a ku Yabesi-giliyadi ndipo mukaphenso akazi ndi ana omwe.+ 11  Zoti mukachite ndi izi: Mukaphe mwamuna aliyense komanso mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna.” 12  Ku Yabesi-giliyadi anapezako atsikana 400, amene anali anamwali oti sanagonepo ndi mwamuna. Atsikanawa anabwera nawo kumsasa ku Silo,+ mʼdziko la Kanani. 13  Ndiyeno gululo linatumiza uthenga kwa anthu a fuko la Benjamini amene anali kuthanthwe la Rimoni+ aja ndipo anawalonjeza mtendere. 14  Choncho, anthu a fuko la Benjaminiwo anabwerera ndipo anawapatsa akazi a ku Yabesi-giliyadi amene sanawaphe aja.+ Koma akaziwo anali osakwanira. 15  Anthuwo anamva chisoni ndi zimene zinachitikira fuko la Benjamini,+ chifukwa Yehova anachititsa kuti mafuko a Isiraeli agawanike. 16  Ndiyeno akulu a Isiraeli ananena kuti: “Popeza akazi onse a fuko la Benjamini anaphedwa, titani kuti tiwapezere akazi amuna amene atsalawa?” 17  Ndiyeno ena anayankha kuti: “Payenera kukhala cholowa kwa anthu a fuko la Benjamini amene apulumuka kuti pasakhale fuko limene lafafanizidwa mu Isiraeli. 18  Koma ife sitikuloledwa kuwapatsa ana athu aakazi kuti akhale akazi awo, chifukwa Aisiraeli analumbira kuti, ‘Aliyense wopereka mkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini ndi wotembereredwa.’”+ 19  Kenako anati: “Pajatu ku Silo+ kumachitika chikondwerero cha Yehova chaka chilichonse. Mzinda wa Silo uli kumpoto kwa Beteli, chakumʼmawa kwa msewu waukulu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kumʼmwera kwa Lebona.” 20  Choncho analamula anthu a fuko la Benjamini kuti: “Pitani, mukabisale mʼminda ya mpesa. 21  Ndiyeno mukakaona atsikana a ku Silo akubwera kudzavina magule awo ovina mozungulira, aliyense akatuluke mʼminda ya mpesayo, nʼkugwira mtsikana pakati pa atsikana a ku Silo, ndipo akapite naye kudera la Benjamini kuti akakhale mkazi wake. 22  Abambo awo kapena azichimwene awo akabwera kudzadandaula, tidzawauza kuti, ‘Tikomereni mtima, tiyeni tiwathandize, chifukwa pa nthawi ya nkhondo, sitinakwanitse kugwira akazi okwanira amuna onse a fuko la Benjamini.+ Ndipo inunso simukanawapatsa akazi popanda kukhala ndi mlandu.’”+ 23  Choncho anthu a fuko la Benjamini anachitadi zimenezo. Ndipo aliyense anatenga mkazi pa akazi amene ankavina. Atatero, anabwerera kumalo awo ndipo anamanganso mizinda+ ija nʼkumakhalamo. 24  Aisiraeli anayamba kubalalika kuchoka kumeneko ndipo aliyense anapita ku fuko lake ndi ku banja lake. Iwo anachoka kumeneko moti aliyense anapita ku cholowa chake. 25  Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Aliyense ankangochita zimene akuona kuti nʼzoyenera.

Mawu a M'munsi