Kalata Yopita kwa Tito 2:1-15
2 Koma iwe pitiriza kulankhula zinthu zogwirizana ndi mfundo zolondola.+
2 Amuna achikulire akhale osachita zinthu mopitirira malire, opanda chibwana, oganiza bwino, achikhulupiriro cholimba, achikondi chachikulu ndi opirira kwambiri.
3 Nawonso akazi achikulire akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche, kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino,
4 nʼcholinga choti azilangiza* akazi achitsikana kuti azikonda amuna awo, azikonda ana awo,
5 azikhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo,* abwino ndiponso ogonjera amuna awo,+ kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.
6 Komanso upitirize kulimbikitsa anyamata kuti akhale oganiza bwino.+
7 Ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino mʼnjira iliyonse. Uziphunzitsa zolondola* ndipo uzisonyeza kuti ndiwe wopanda chibwana.+
8 Mawu ako azikhala oyenera, omwe sangatsutsidwe,+ kuti otsutsa achite manyazi ndipo asapeze chifukwa chotinenera.+
9 Akapolo azigonjera ambuye awo pa zinthu zonse+ ndipo aziwakondweretsa. Asamatsutsane nawo
10 kapena kuwabera,+ koma akhale okhulupirika pa chilichonse, kuti azikometsera zimene Mpulumutsi wathu Mulungu amatiphunzitsa.+
11 Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweretsa chipulumutso kwa anthu, kaya akhale otani.+
12 Zimenezi zimatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu. Zimatiphunzitsanso kuti tisamalakelake zinthu zoipa zamʼdzikoli,+ koma kuti tikhale oganiza bwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu mʼdzikoli*+
13 pamene tikuyembekezera zinthu zosangalatsa+ ndiponso kuonekera kwaulemerero kwa Mulungu wamkulu komanso kwa Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu,
14 amene anadzipereka mʼmalo mwa ife+ kuti atilanditse*+ ku moyo wochita zinthu zosamvera malamulo za mtundu uliwonse ndiponso kuti atiyeretse, kuti tikhale anthu ake apadera, odzipereka pa ntchito zabwino.+
15 Pitiriza kulankhula zimenezi, kulimbikitsa ndi kudzudzula anthu pogwiritsa ntchito ulamuliro wonse umene wapatsidwa.+ Usalole kuti munthu aliyense akuderere.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “azikumbutsa; aziphunzitsa.”
^ Kapena kuti, “osamalira nyumba zawo.”
^ Kapena kuti, “zoyera.”
^ Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “atiperekere dipo; atiwombole.”