Kalata ya Yakobo 5:1-20
5 Tamverani inu anthu achuma. Lirani mofuula chifukwa cha masautso amene akubwera kwa inu.+
2 Chuma chanu chawola ndipo zovala zanu zadyedwa ndi njenjete.*+
3 Golide ndi siliva wanu wawonongeka ndi dzimbiri. Dzimbiri limenelo lidzakhala umboni wokutsutsani ndipo lidzadya mnofu wanu. Zimene mwasunga zidzakhala ngati moto mʼmasiku otsiriza.+
4 Tamverani! Malipiro amene simunapereke kwa anthu amene anagwira ntchito yokolola mʼminda yanu akufuula ndipo Yehova* wa magulu ankhondo akumwamba wamva kufuula kopempha thandizo kwa anthu okololawo.+
5 Mwakhala moyo wa mwanaalirenji ndipo dziko lapansi mwalidyerera. Mwadya ndipo mwanenepa ngati nyama pa tsiku limene ikukaphedwa.+
6 Mwaweruza ndiponso kupha munthu wolungama. Iye akukutsutsani.
7 Choncho lezani mtima abale, mpaka kukhalapo kwa Ambuye.+ Ganizirani mmene mlimi amachitira. Iye amayembekezerabe zipatso zamtengo wapatali zochokera munthaka. Amayembekezera moleza mtima mpaka mvula yoyamba komanso mvula yomaliza itagwa.+
8 Inunso khalani oleza mtima.+ Limbitsani mitima yanu, chifukwa kukhalapo kwa Ambuye kwayandikira.+
9 Musamadandaule za ena* abale, kuti musaweruzidwe.+ Taonani, Woweruza waima pakhomo.
10 Abale, pa nkhani ya kumva zowawa+ ndi kuleza mtima,+ tengerani chitsanzo cha aneneri amene analankhula mʼdzina la Yehova.*+
11 Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawaona kuti ndi odala.*+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mukudziwa madalitso amene Yehova* anamupatsa.+ Mukuona nokha kuti Yehova* ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.+
12 Koma koposa zonse abale anga, siyani kulumbira, potchula kumwamba kapena dziko lapansi kapena lumbiro lina lililonse. Koma mukati “Inde,” azikhaladi inde ndipo mukati “Ayi,” azikhaladi ayi+ kuti musakhale oyenera kuweruzidwa.
13 Kodi pali aliyense amene akukumana ndi mavuto pakati panu? Apitirize kupemphera.+ Kodi pali aliyense amene akusangalala? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.+
14 Kodi pali aliyense amene akudwala pakati panu? Aitane akulu+ a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka+ mafuta mʼdzina la Yehova.*
15 Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu amene akudwalayo* ndipo Yehova* adzamulimbitsa. Komanso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.
16 Choncho muululirane machimo anu poyera+ ndi kupemphererana, kuti muchiritsidwe. Pemphero lopembedzera la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.*+
17 Eliya anali munthu ngati ife tomwe, komabe atapemphera kuchokera pansi pamtima kuti mvula isagwe, mvula sinagwedi mʼdzikolo kwa zaka zitatu ndi miyezi 6.+
18 Kenako anapempheranso ndipo mvula inagwa kuchokera kumwamba moti nthaka inatulutsa zipatso zake.+
19 Abale anga, ngati wina pakati panu wasiya choonadi chifukwa chosocheretsedwa, ndiye munthu wina nʼkumubweza,
20 dziwani kuti amene wabweza wochimwayo panjira yake yoipa,+ wamupulumutsa ku imfa ndipo Mulungu adzakhululukira wochimwayo machimo ambiri.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “Musamangʼungʼudze za ena.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “osangalala.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mabaibulo ena amati, “amene watopayo.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “limakhala lamphamvu kwambiri pamene likugwira ntchito.”