Yeremiya 10:1-25
10 Inu a mʼnyumba ya Isiraeli, imvani chenjezo limene Yehova wakupatsani.
2 Yehova wanena kuti:
“Musaphunzire miyambo ya anthu a mitundu ina,+Ndipo musachite mantha ndi zizindikiro zakumwamba,Chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+
3 Miyambo ya anthu amenewa ndi yopanda pake.
Mmisiri amagwetsa mtengo munkhalango,Nʼkusema fano pogwiritsa ntchito chida chake.*+
4 Akatero amakongoletsa fanolo ndi siliva komanso golide.+Kenako amatenga hamala ndi misomali nʼkulikhomerera pansi kuti lisagwe.+
5 Mafanowo ali ngati choopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+Iwo amafunika kunyamulidwa chifukwa sangayende okha.+
Musamachite mantha ndi mafano chifukwa sangakuvulazeni,Komanso sangachite chilichonse chabwino.”+
6 Palibe aliyense amene angafanane ndi inu Yehova.+
Inu ndinu wamkulu ndipo dzina lanu ndi lalikulu komanso lamphamvu.
7 Kodi ndi ndani amene sakuyenera kukuopani, inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa.Chifukwa pakati pa anzeru onse a mʼmitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse,Palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+
8 Onse ndi opanda nzeru ndiponso opusa.+
Malangizo ochokera pamtengo amalimbikitsa anthu kuchita zachabechabe.+
9 Siliva amene anamusula kukhala mapalemapale amachokera ku Tarisi+ ndipo golide amachokera ku Ufazi.Zonsezi zimakonzedwa mwaluso ndipo ndi ntchito ya manja a mmisiri wa zitsulo.
Amawaveka zovala zaulusi wabuluu ndi ubweya wa nkhosa wapepo.
Mafano onsewo amapangidwa ndi amisiri aluso.
10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.
Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu yamuyaya.+
Dziko lapansi lidzagwedezeka chifukwa cha mkwiyo wake,+Ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzapilire mkwiyo wake.
11 * Mitunduyo ukaiuze izi:
“Milungu imene sinapange kumwamba ndi dziko lapansiIdzawonongedwa padziko lapansi komanso pansi pa thambo.”+
12 Iye ndi Mulungu amene anapanga dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake,Amene anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru zake.+Amenenso anatambasula kumwamba chifukwa cha kuzindikira kwake.+
13 Mawu ake akamveka,Madzi akumwamba amachita mkokomo,+Ndipo amachititsa mitambo* kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima,Ndipo amatulutsa mphepo mʼnyumba zake zosungira.+
14 Munthu aliyense akuchita zinthu mopanda nzeru komanso mosazindikira.
Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+Chifukwa chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonamaNdipo mafano amenewa alibe mzimu.*+
15 Iwo ndi achabechabe, oyenera kunyozedwa.+
Tsiku loti aweruzidwe likadzafika adzawonongedwa.
16 Koma Mulungu, amene ndi cholowa cha Yakobo, sali ngati mafano amenewa,Chifukwa iye ndi amene anapanga china chilichonse,Ndipo Isiraeli ndi ndodo ya cholowa chake.+
Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
17 Iwe mkazi amene wazunguliridwa ndi adani,Sonkhanitsa katundu wako.
18 Chifukwa Yehova wanena kuti:
“Pa nthawi ino ndikuthamangitsa* anthu okhala mʼdzikoli,+Ndipo ndidzachititsa kuti akumane ndi mavuto.”
19 Tsoka kwa ine chifukwa cha kuwonongedwa kwanga!*+
Bala langa ndi losachiritsika.
Ndinanena kuti: “Ndithudi amenewa ndi matenda anga ndipo ndikufunika kuwapirira.
20 Tenti yanga yawonongedwa ndipo zingwe zanga zonse zomangira tentiyo aziduladula.+
Ana anga aamuna andisiya ndipo kulibenso.+
Palibe aliyense amene watsala woti atambasule tenti yanga kapena kudzutsa nsalu za tentiyo.
21 Abusa achita zinthu mopanda nzeru,+Ndipo sanafunse malangizo kwa Yehova.+
Nʼchifukwa chake sanachite zinthu mozindikira,Ndipo ziweto zawo zonse zabalalika.”+
22 Tamvetserani, mdani akubwera!
Kukumveka kugunda kwakukulu kuchokera kudziko lakumpoto,+Kumene kudzasandutsa mizinda ya Yuda kukhala mabwinja, malo obisalamo mimbulu.+
23 Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu alibe ulamuliro wosankha yekha njira ya moyo wake.
Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.+
24 Inu Yehova, ndilangizeni pondipatsa chiweruzo,Koma osati mutakwiya+ chifukwa mungandiwononge.+
25 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene akukunyalanyazani,+Komanso pa mafuko amene saitana pa dzina lanu.
Chifukwa iwo awononga mbadwa zonse za Yakobo,+Amuwononga mpaka kufika potheratu,+Ndipo dziko lake alisandutsa bwinja.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “sompho wake.” Sompho ndi chida chimene mʼmadera ena amanena kuti kasemasema.
^ Vesi 11 poyamba linalembedwa mʼChiaramu.
^ Kapena kuti, “nthunzi.”
^ Kapena kuti, “mpweya.”
^ Kapena kuti, “Pa nthawi ino ndikutayira kutali.”
^ Kapena kuti, “chifukwa fupa langa lathyoka.”