Yeremiya 12:1-17

  • Kudandaula kwa Yeremiya (1-4)

  • Zimene Yehova anayankha (5-17)

12  Inu Yehova, ndikabweretsa dandaulo langa kwa inu,Komanso ndikamalankhula ndi inu nkhani zokhudza chilungamo, mumasonyeza kuti ndinu wolungama.+ Koma nʼchifukwa chiyani anthu oipa, zinthu zikuwayendera bwino,+Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu amene amachita zachinyengo amakhala opanda nkhawa?  2  Munawadzala ndipo iwo anazika mizu. Akula ndipo abala zipatso. Amakutchulani pafupipafupi, koma mtima wawo uli kutali* kwambiri ndi inu.+  3  Koma inu Yehova, mukundidziwa bwino+ ndipo mumandiona.Mwafufuza mtima wanga ndipo mwapeza kuti ndine wokhulupirika kwa inu.+ Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,Ndipo muwaike padera poyembekezera tsiku limene adzaphedwe.  4  Kodi dzikoli likhalabe lofota mpaka liti?Kodi zomera zamʼmunda uliwonse zikhalabe zouma mpaka liti?+ Chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu amʼdzikoli akuchita,Zilombo zakutchire ndi mbalame zawonongedwa. Chifukwa anthuwo akuti: “Iye sakuona zimene zidzatichitikire.”  5  Ngati ukutopa pothamanga ndi anthu oyenda pansi,Ndiye ungapikisane bwanji ndi mahatchi?+ Ukhoza kuona kuti ndiwe wotetezeka mʼdziko lamtendere,Koma kodi udzatani ukadzakhala mʼnkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano?  6  Chifukwa ngakhale abale ako enieni, anthu a mʼnyumba ya bambo ako,Akuchitira zinthu zachinyengo.+ Iwo akunenera zinthu zoipa mofuula. Usawakhulupirire,Ngakhale atamalankhula zinthu zabwino kwa iwe.  7  “Nyumba yanga ndaisiya.+ Ndasiya cholowa changa.+ Wokondedwa wanga ndamupereka mʼmanja mwa adani ake.+  8  Cholowa changa chakhala ngati mkango kwa ine munkhalango. Wokondedwa wanga wandibangulira. Nʼchifukwa chake ndadana naye.  9  Cholowa changa chili ngati mbalame yanthenga zamitundu yosiyanasiyana imene imadya nyama.Mbalame zina zodya nyama zaizungulira nʼkuiukira.+ Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zamʼtchire,Bwerani kuti mudzadye.+ 10  Abusa ambiri awononga munda wanga wa mpesa.+Apondaponda malo omwe ndi cholowa changa.+ Malo omwe ndi cholowa changa chosiririka awasandutsa bwinja moti palibe aliyense amene akukhalamo. 11  Cholowa changacho chasanduka chipululu, Ndipo chafota.*Chawonongeka pamaso panga,+ Dziko lonse lakhala bwinja,Koma palibe aliyense amene zikumukhudza.+ 12  Anthu owononga adutsa mʼnjira zonse zodutsidwadutsidwa zamʼchipululu,Chifukwa lupanga la Yehova likuwononga anthu kuchokera kumalekezero a dziko kukafika kumalekezero ena a dziko.+ Ndipo palibe munthu aliyense amene ali pamtendere. 13  Afesa tirigu koma akolola minga.+ Agwira ntchito yotopetsa koma osapeza phindu lililonse. Iwo adzachita manyazi ndi zokolola zawoChifukwa mkwiyo waukulu wa Yehova udzawayakira.” 14  Yehova wanena kuti: “Anthu onse oipa amene ndinayandikana nawo amene akukhudza cholowa chimene ndinapatsa anthu anga Aisiraeli kuti chikhale chawo,+ ndikuwazula mʼdziko lawo+ ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pawo. 15  Koma ndikadzawazula, ndidzawachitiranso chifundo moti ndidzabwezeretsa aliyense wa iwo pacholowa chake ndi pamalo ake. 16  Ndiyeno anthu a mitundu ina akadzayesetsa kuphunzira njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’ ngati mmene iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, anthu a mitundu inawo adzakhazikika pakati pa anthu anga. 17  Koma akadzakana kumvera, ine ndidzazulanso anthu a mtundu umenewo. Ndidzawazula nʼkuwawononga,” akutero Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mmene akumvera mumtima mwawo.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zawo zili kutali.”
Mabaibulo ena amati, “chikundilirira.”