Yeremiya 20:1-18

  • Pasuri anamenya Yeremiya (1-6)

  • Yeremiya sangasiye kulalikira (7-13)

    • Uthenga wa Mulungu unali ngati moto woyaka (9)

    • Yehova ali ngati msilikali woopsa (11)

  • Kudandaula kwa Yeremiya (14-18)

20  Tsopano Pasuri, mwana wa Imeri, wansembe, amenenso anali mtumiki wamkulu mʼnyumba ya Yehova, ankamvetsera pamene Yeremiya ankalosera zinthu zimenezi. 2  Kenako Pasuri anamenya mneneri Yeremiya n‘kumuika mʼmatangadza+ amene anali pa Geti Lakumtunda la Benjamini, limene linali mʼnyumba ya Yehova. 3  Ndiyeno pa tsiku lotsatira, Pasuri atamasula Yeremiya mʼmatangadzawo, Yeremiya anamuuza kuti: “Yehova wanena kuti dzina lako silikhalanso Pasuri koma Chochititsa Mantha Paliponse.+ 4  Chifukwa Yehova wanena kuti, ‘Ine ndikukuchititsa kuti ukhale chinthu chochititsa mantha kwa iwe ndi kwa anzako onse, ndipo adzaphedwa ndi lupanga la adani awo iweyo ukuona.+ Anthu onse a mu Yuda ndidzawapereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babulo. Ena adzapita nawo ku Babulo ndipo ena adzawapha ndi lupanga.+ 5  Ndipo chuma chonse chamumzindawu, katundu wawo yense, zinthu zawo zonse zamtengo wapatali ndi chuma chonse cha mafumu a Yuda ndidzazipereka mʼmanja mwa adani awo.+ Adaniwo adzatenga zinthu zimenezi nʼkupita nazo ku Babulo.+ 6  Koma iwe Pasuri ndi anthu onse amene amakhala mʼnyumba yako, mudzapita ku ukapolo. Iweyo udzapita ku Babulo ndipo udzafera kumeneko nʼkuikidwa mʼmanda komweko limodzi ndi anzako onse, chifukwa walosera zabodza kwa iwo.’”+  7  Mwandipusitsa* inu Yehova, ndithu mwandipusitsa. Mwagwiritsa ntchito mphamvu zanu pa ine ndipo mwapambana.+ Ndakhala chinthu choseketsa tsiku lonse.Aliyense akungondinyoza.+  8  Nthawi zonse ndikafuna kulankhula, ndimafuula kuti,“Chiwawa ndi chiwonongeko!” Kwa ine mawu a Yehova achititsa kuti ndizinyozedwa ndi kusekedwa tsiku lonse.+  9  Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye,Ndipo sindidzalankhulanso mʼdzina lake.”+ Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka umene watsekeredwa mʼmafupa anga,Ndipo ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhuleMoti sindikanathanso kupirira.+ 10  Chifukwa ndinamva mphekesera zambiri zoipa.Zinthu zochititsa mantha zinali paliponse.+ Iwo ankanena kuti, “Muimbeni mlandu, tiyeni timuimbe mlandu!” Munthu aliyense amene ankandifunira zabwino ankayembekezera kuti ndichite chinachake cholakwika.+ Ankanena kuti: “Mwina alakwitsa chinachake ameneyu,Ndipo timugonjetsa nʼkumubwezera.” 11  Koma Yehova anali nane ngati msilikali woopsa.+ Nʼchifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana.+ Adzachita manyazi kwambiri chifukwa zinthu sizidzawayendera bwino. Manyazi awo adzakhala nawo mpaka kalekale ndipo sadzaiwalika.+ 12  Koma inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mumafufuza munthu wolungama.Mumaona maganizo a munthu* komanso mtima wake.+ Ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,+Chifukwa mlandu wanga ndausiya mʼmanja mwanu.+ 13  Imbirani Yehova! Tamandani Yehova! Chifukwa wapulumutsa munthu wosauka mʼmanja mwa anthu ochita zoipa. 14  Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! Tsiku limene mayi anga anandibereka lisadalitsike!+ 15  Atembereredwe munthu amene anabweretsa uthenga wabwino kwa bambo anga powauza kuti: “Mkazi wako wakuberekera mwana wamwamuna, kamnyamata!” Nʼkuchititsa kuti bambo anga asangalale kwambiri. 16  Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova anaigonjetsa popanda kuimvera chisoni. Mʼmawa kwambiri azimva kulira kofuula ndipo masana azimva phokoso lochenjeza. 17  Nʼchifukwa chiyani sanandiphe ndili mʼmimba,Kuti mayi anga akhale manda anga,Ndiponso kuti apitirize kukhala oyembekezera?+ 18  Nʼchifukwa chiyani ndinabadwa?Kodi ndinabadwa kuti ndidzaone mavuto komanso kukhala wachisoni,Kuti moyo wanga uthe mochititsa manyazi?+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mwandidabwitsa.”
Kapena kuti, “Mumaona mmene munthu akumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumaona impso za munthu.”