Yeremiya 43:1-13

  • Anthu sanamvere ndipo anapita ku Iguputo (1-7)

  • Zimene Yehova anauza Yeremiya ku Iguputo (8-13)

43  Yeremiya atamaliza kuuza anthu onse mawu onsewa ochokera kwa Yehova Mulungu wawo, mawu onse amene Yehova Mulungu wawo anamutuma kuti akawauze, 2  Azariya mwana wa Hoshaya, Yohanani+ mwana wa Kareya ndi anthu onse odzikuza anauza Yeremiya kuti: “Zimene ukunenazo ndi zabodza! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti udzatiuze kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko.’ 3  Koma Baruki+ mwana wa Neriya ndi amene akukulimbikitsa kuti unene zinthu zofuna kutipweteketsa nʼcholinga choti mutipereke mʼmanja mwa Akasidi kuti atiphe kapena atitenge kupita ku ukapolo ku Babulo.”+ 4  Choncho Yohanani mwana wa Kareya, akuluakulu onse a asilikali ndi anthu onse sanamvere mawu a Yehova oti apitirize kukhala mʼdziko la Yuda. 5  Mʼmalomwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali anatenga anthu onse amene anatsala ku Yuda amene anabwerera kuchokera ku mitundu yonse ya anthu kumene anathawira kuti adzakhale mʼdziko la Yuda.+ 6  Anatenga amuna, akazi, ana, ana aakazi a mfumu ndiponso aliyense amene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anawasiya mʼmanja mwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani.+ Anatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya. 7  Iwo anapita mʼdziko la Iguputo chifukwa sanamvere mawu a Yehova ndipo anakafika ku Tahapanesi.+ 8  Ndiyeno pamene Yeremiya anali ku Tahapanesi, Yehova anamuuza kuti: 9  “Tenga miyala ikuluikulu ndipo ukaibise mʼdothi limene anamangira masitepe a njerwa amene ali pakhomo la nyumba ya Farao ku Tahapanesi. Ukachite zimenezi amuna onse a Chiyuda akuona. 10  Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndikuitana Nebukadinezara* mfumu ya Babulo mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala imene ndaibisayi. Iye adzamanga tenti yake yachifumu pamwamba pa miyala imeneyi.+ 11  Nebukadinezara adzabwera nʼkuukira dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo ndipo woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+ 12  Nyumba za milungu* ya ku Iguputo ndidzaziwotcha ndi moto.+ Nebukadinezara adzawotcha nyumbazo nʼkutenga milunguyo kupita nayo kudziko lina. Mʼbusa savutika kuvala chovala chake. Mofanana ndi zimenezi, Nebukadinezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo nʼkuchokako mwamtendere.* 13  Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu* ya ku Iguputo adzaziwotcha ndi moto.”’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “Akachisi a milungu.”
Kapena kuti, “osavulazidwa.”
Kapena kuti, “Nyumba ya (Kachisi wa) Dzuwa,” kutanthauza Heliyopolisi.
Kapena kuti, “akachisi a milungu.”