Yesaya 18:1-7

  • Uthenga wokhudza Itiyopiya (1-7)

18  Tsoka kwa dziko lamkokomo wa tizilombo tamapiko,Limene lili mʼchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya.+  2  Dzikolo limatumiza nthumwi zake kudzera panyanja,Zimadutsa pamadzi mʼngalawa zopangidwa ndi gumbwa.* Dzikolo limanena kuti: “Pitani, inu amithenga achangu,Ku mtundu wa anthu ataliatali komanso akhungu losalala,Kwa anthu amene kulikonse amaopedwa,+Kwa mtundu wa anthu amphamvu, amene akugonjetsa mitundu ina,Umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.”  3  Inu nonse okhala padziko lapansi,Zimene mukuona zidzakhala ngati chizindikiro chimene chaikidwa pamapiri,Ndipo mudzamva phokoso lofanana ndi kulira kwa lipenga.  4  Chifukwa Yehova wandiuza kuti: “Ndidzakhala mosatekeseka nʼkumayangʼana pamalo anga okhala,*Ndidzachita zimenezi ngati kutentha komanso kuwala kwa dzuwa,Ngati mame amene amagwa pa nthawi yokolola, kukamatentha.  5  Chifukwa nthawi yokolola isanafike,Mitengo ikamaliza kuchita maluwa ndipo mphesa zikamapsa,Mphukira zidzadulidwa ndi chida chosadzira mitengoNdipo tiziyangoyango take tidzadulidwa nʼkuchotsedwa.  6  Onsewo adzasiyidwa kuti adyedwe ndi mbalame zamʼmapiri zodya nyamaKomanso nyama zakutchire zapadziko lapansi. Mbalame zodya nyamazo zidzakhala zikuwadya nyengo yonse yachilimwe,Ndipo nyama zonse zakutchire za padziko lapansi zidzakhala zikuwadya nthawi yonse yokolola.  7  Pa nthawi imeneyo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzapatsidwa mphatso,Kuchokera ku mtundu wa anthu ataliatali komanso akhungu losalala,Kuchokera kwa anthu amene kulikonse amaopedwa,Kuchokera kwa mtundu wa anthu amphamvu, amene akugonjetsa mitundu ina,Umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.Mphatsoyo adzaibweretsa kuphiri la Ziyoni, kumene kuli dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “nʼkumayangʼana ndili pamalo anga okhala.”