Yesaya 26:1-21
26 Pa tsiku limenelo, mʼdziko la Yuda+ mudzaimbidwa nyimbo+ yakuti:
“Ife tili ndi mzinda wolimba.+
Chipulumutso chake chili ngati mipanda yake ndiponso ngati malo ake okwera omenyerapo nkhondo.+
2 Tsegulani mageti+ kuti mtundu wolungama ulowe,Mtundu umene ukuchita zinthu mokhulupirika.
3 Anthu amene amakudalirani ndi mtima wonse* mudzawateteza.Mudzawapatsa mtendere wosatha,+Chifukwa amadalira inu.+
4 Muzidalira Yehova mpaka kalekale,+Chifukwa Ya,* Yehova ndi Thanthwe lamuyaya.+
5 Chifukwa iye watsitsa anthu okhala pamalo okwezeka, mzinda wokwezeka.
Mzindawo wautsitsa,Wautsitsira pansi,Waugwetsera pafumbi.
6 Phazi lidzaupondaponda,Mapazi a anthu osautsika, mapazi a anthu onyozeka adzaupondaponda.”
7 Njira ya munthu wolungama ndi yowongoka.*
Chifukwa choti ndinu wowongoka mtima,Mudzasalaza njira ya anthu olungama.
8 Inu Yehova, pamene tikutsatira njira ya ziweruzo zanu,Chiyembekezo chathu chili pa inu.
Tikulakalaka dzina lanu komanso zimene dzinalo limaimira.*
9 Usiku ndimakulakalakani ndi mtima wanga wonse,Inde, ndimakufunafunani ndi mtima wonse.+Chifukwa mukaweruza dziko lapansi,Anthu okhala mʼdzikoli amaphunzira zokhudza chilungamo.+
10 Ngakhale munthu woipa atachitiridwa zabwino,Sadzaphunzira kuchita zinthu zolungama.+
Ngakhale mʼdziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zoipa,+Ndipo sadzaona ulemerero wa Yehova.+
11 Inu Yehova, dzanja lanu lakwezedwa, koma iwo sakuliona.+
Iwo adzaona kuti mumakonda kwambiri anthu anu* ndipo adzachita manyazi.
Inde, moto wanu udzapsereza adani anu.
12 Inu Yehova, mudzatipatsa mtendere,+Chifukwa zonse zimene tachitaTazikwanitsa chifukwa cha inu.
13 Inu Yehova Mulungu wathu, ife takhala tikulamuliridwa ndi ambuye ena osati inu,+Koma timatchula dzina lanu lokha.+
14 Iwo afa. Sadzakhalanso ndi moyo.
Iwo ndi akufa ndipo sadzaukanso.+
Chifukwa inu mwawapatsa chilangoKuti muwawononge nʼcholinga choti asadzatchulidwenso.
15 Mwakulitsa mtundu wa anthu, inu Yehova,Mwakulitsa mtundu wa anthu.Mwadzilemekeza.+
Mwafutukula kwambiri malire onse a dzikolo.+
16 Inu Yehova, pa nthawi ya mavuto iwo anatembenukira kwa inu kuti muwathandize.Mutawalanga, anakhuthulira mitima yawo kwa inu mʼpemphero lonongʼona.+
17 Mofanana ndi mkazi woyembekezera amene watsala pangʼono kubereka,Amene akulira chifukwa cha ululu wa pobereka,Ndi mmenenso tikumvera chifukwa cha inu Yehova.
18 Ife tinali oyembekezera ndipo tinamva zowawa za pobereka,Koma zili ngati tinabereka mphepo.
Sitinabweretse chipulumutso mʼdzikoli,Ndipo palibe aliyense amene wabadwa kuti akhale mʼdzikoli.
19 “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo.
Anthu anga amene anafa adzadzuka* nʼkuimirira.+
Dzukani ndipo mufuule mosangalala,Inu anthu okhala mʼfumbi!+
Chifukwa mame anu ali ngati mame amʼmawa,*Ndipo dziko lapansi lidzatulutsa anthu amene anafa kuti akhalenso ndi moyo.*
20 Inu anthu anga, pitani mukalowe mʼzipinda zanu zamkati,Ndipo mukatseke zitseko.+
Mukabisale kwa kanthawiMpaka mkwiyo utadutsa.*+
21 Chifukwa taonani! Yehova akubwera kuchokera kumene amakhalaKuti adzaimbe mlandu anthu okhala mʼdzikoli chifukwa cha zolakwa zawo,Ndipo dzikoli lidzaonetsa poyera magazi amene linakhetsaNdipo silidzabisanso anthu ake amene anaphedwa.”
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “Anthu a mtima wokhazikika.”
^ “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “ndi yosalazika.”
^ Kutanthauza, Mulungu ndi dzina lake akumbukiridwe, anthu amudziwe.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaona mmene mukudziperekera chifukwa cha anthu anu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mtembo wanga udzadzuka.”
^ Mabaibulo ena amati, “ali ngati mame a maluwa.”
^ Kapena kuti, “lidzabereka anthu amene anafa.”
^ Kapena kuti, “chilango chitadutsa.”