Yesaya 27:1-13

  • Leviyatani adzaphedwa ndi Yehova (1)

  • Nyimbo yosonyeza kuti Isiraeli ndi munda wa mpesa (2-13)

27  Pa tsiku limenelo, Yehova adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lolimba,+Kulanga Leviyatani,* njoka yokwawa mothamanga!Adzalanga Leviyatani, njoka yoyenda mokhotakhota,Ndipo adzapha chinjoka chachikulu chokhala mʼnyanja.  2  Pa tsiku limenelo mudzaimbire mkaziyo* nyimbo yakuti: “Iwe ndiwe munda wa mpesa wotulutsa vinyo wathovu.+  3  Ine Yehova ndikulondera mkaziyo.+ Ndimamuthirira nthawi zonse.+ Ndimamulondera masana ndi usiku,Kuti wina aliyense asamuvulaze.+  4  Ndaleka kumukwiyira.+ Ngati munthu wina ataika zitsamba zaminga ndi udzu pamaso panga, Ndidzazipondaponda nʼkuziwotcha nthawi imodzi ndipo ndidzamenyana naye.  5  Apo ayi, iye athawire kumalo anga otetezeka. Akhazikitse mtendere ndi ine.Iye akhazikitse mtendere ndi ine.”  6  Mʼmasiku amene akubwerawo, Yakobo adzamera mizu,Isiraeli adzaphuka nʼkuchita maluwa,+Ndipo iwo adzadzaza dzikolo ndi zipatso.+  7  Kodi iye akufunikira kumenyedwa ngati mmene akumenyedweramu? Kapena kodi iye akufunikira kuphedwa ngati mmene anthu ake akuphedweramu?  8  Mudzalimbana naye ndi mfuu yoopseza pomuthamangitsa. Iye adzamuthamangitsa ndi mphepo yake yamphamvu pa tsiku lamphepo yakumʼmawa.+  9  Choncho mwa njira imeneyi zolakwa za Yakobo zidzaphimbidwa,+Ndipo tchimo lake likadzachotsedwa zotsatira zake zidzakhala izi: Adzasandutsa miyala yonse yapaguwa lansembeKukhala ngati miyala yofewa kwambiri imene yanyenyekanyenyeka,Ndipo sipadzatsala mizati yopatulika* kapena maguwa ofukizirapo zonunkhira.+ 10  Chifukwa mumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mudzakhala mopanda anthu.Malo odyetserako ziweto adzasiyidwa ndipo adzakhala opanda kanthu ngati chipululu.+ Kumeneko mwana wa ngʼombe azidzadya msipu ndiponso kugona pansiNdipo iye adzadya nthambi zake.+ 11  Tinthambi take tikadzauma,Akazi adzabwera kudzatithyolaNʼkukakolezera moto. Anthu awa samvetsa zinthu,+ Nʼchifukwa chake amene anawapanga sadzawachitira chifundo,Ndipo amene anawaumba sadzawakomera mtima.+ 12  Pa tsiku limenelo Yehova adzathyola zipatso kuchokera ku Mtsinje* mpaka kukafika kukhwawa la Iguputo+ ndipo mudzasonkhanitsidwa mmodzimmodzi, inu Aisiraeli.+ 13  Pa tsiku limenelo nyanga yaikulu ya nkhosa idzalizidwa,+ ndipo anthu amene anali atatsala pangʼono kufa mʼdziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana mʼdziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira Yehova mʼphiri loyera ku Yerusalemu.+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti mkazi ameneyu akunena Isiraeli ndipo akumuyerekezera ndi munda wampesa.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.