Yesaya 28:1-29
28 Tsoka kwa chisoti* chokongola* cha zidakwa za ku Efuraimu+Komanso maluwa ake okongola amene akufota!Maluwawo avalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde, kumene zidakwa zoledzera ndi vinyozo zimakhala.
2 Taonani! Yehova ali ndi winawake wamphamvu komanso wanyonga.
Mofanana ndi mvula yamabingu komanso yamatalala, mvula yamphepo yowononga,Mofanana ndi mvula yamabingu ya madzi amphamvu osefukira,Iye adzagwetsera pansi chisoti chaulemererocho mwamphamvu.
3 Zisoti zokongola* za zidakwa za ku Efuraimu,Zidzapondedwapondedwa ndi mapazi.+
4 Komanso maluwa ake okongola amene akufota,Amene avalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde,Adzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kucha chilimwe chisanafike.
Munthu akaiona, amaithyola nʼkuimeza mwamsanga.
5 Pa tsiku limenelo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakhala ngati chisoti chaulemerero ndiponso ngati nkhata yamaluwa yokongola kwa anthu ake otsala.+
6 Adzakhalanso ngati mzimu wa chilungamo kwa munthu wopereka chiweruzo, ndiponso adzapereka mphamvu kwa anthu othamangitsa adani amene afika pageti kuti adzawaukire.+
7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo.Akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.
Wansembe ndi mneneri asochera chifukwa cha mowa.Vinyo wawasokoneza,Ndipo akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.Sakuona bwinobwino ndipo akusochera,Komanso akulephera kusankha zinthu mwanzeru.+
8 Pamatebulo awo padzaza masanzi.Paliponse pali masanzi okhaokha.
9 Kodi iyeyo akufuna kuti aphunzitse ndani,Ndipo akufuna kuti afotokozere ndani uthengawo kuti aumvetsetse?
Kodi akufuna kufotokozera ana amene asiyitsidwa kumene kuyamwa,Amene angochotsedwa kumene kubere?
10 Chifukwa ndi “lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo,Mzera ndi mzera, mzera ndi mzera,*+Apa pangʼono, apo pangʼono.”
11 Choncho iye adzalankhula kwa anthu awa kudzera mwa anthu achibwibwi* ndiponso olankhula chilankhulo chachilendo.+
12 Iye anauzapo anthuwo kuti: “Awa ndi malo opumira. Munthu amene watopa musiyeni apume. Awa ndi malo ampumulo,” koma iwo sanafune kumvetsera.+
13 Choncho kwa iwowo mawu a Yehova adzakhala:
“Lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo,Mzera ndi mzera, mzera ndi mzera,*+Apa pangʼono, apo pangʼono,”
Kuti pamene akuyenda,Apunthwe nʼkugwa chagadaNʼkuthyoka, kukodwa ndi kugwidwa.+
14 Choncho imvani mawu a Yehova, inu anthu odzitama,Inu atsogoleri a anthu awa mu Yerusalemu,
15 Chifukwa anthu inu mwanena kuti:
“Ife tachita pangano ndi Imfa,+Ndipo tachita mgwirizano* ndi Manda.*
Madzi osefukira akamadutsa,Safika kuli ife kuno,Chifukwa bodza talisandutsa malo athu othawirakoNdipo tabisala mʼchinyengo.”+
16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Ndikuika mwala woyesedwa mu Ziyoni kuti ukhale maziko,+Umenewu ndi mwala wapakona wamtengo wapatali+ wa maziko olimba.+
Palibe munthu woukhulupirira amene adzade nkhawa.+
17 Chilungamo ndidzachisandutsa chingwe choyezera+Komanso ndidzachisandutsa chipangizo chosalazira.*+
Mvula yamatalala idzakokolola malo othawirapo abodza,Ndipo madzi adzasefukira pamalo obisalako.
18 Pangano lanu limene mwachita ndi Imfa lidzatha,Ndipo mgwirizano umene mwachita ndi Manda* sudzagwira ntchito.+
Madzi amphamvu osefukira akamadzadutsa,Adzakukokololani.
19 Nthawi iliyonse imene akudutsa,Azidzakukokololani.+Chifukwa azidzadutsa mʼmawa uliwonse,Azidzadutsanso masana komanso usiku.
Zinthu zochititsa mantha ndi zimene zidzawathandize kumvetsa zimene anamva.”*
20 Chifukwa bedi lafupika kwambiri moti munthu sangathe kugonapo mowongoka bwinobwino,Ndipo chofunda chachepa kwambiri moti sichikukwanira bwinobwino kuti munthu afunde.
21 Yehova adzaimirira ngati mmene anachitira paphiri la Perazimu.Adzaimirira ngati mmene anachitira mʼchigwa, pafupi ndi Gibiyoni,+Kuti achite zochita zake, zochita zake zodabwitsa,Komanso kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo.+
22 Tsopano pewani kunyoza+Kuti zingwe zanu asapitirize kuzimanga kwambiri,Chifukwa ndamva kuchokera kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa,Kuti waganiza zoti awononge dziko lonseli.*+
23 Tcherani khutu ndipo mvetserani mawu anga.Khalani tcheru ndi kumvetsera zimene ndikunena.
24 Kodi wolima munda ndi pulawo amangokhalira kulima tsiku lonse osadzala mbewu?
Kodi amangokhalira kuphwanya zibuma ndi kusalaza dothi?+
25 Iye akamaliza kusalaza dothiloKodi sawazapo chitowe chakuda ndiponso kufesa chitowe chamtundu wina?Ndipo kodi sadzala tirigu, mapira ndi balere mʼmalo ake,Komanso mbewu zina*+ mʼmphepete mwa mundawo?
26 Mulungu amaphunzitsa* munthu mʼnjira yoyenereraMulungu wake amamulangiza.+
27 Chifukwa chitowe chakuda sachipuntha ndi chida chopunthira,+Ndipo pachitowe chamtundu wina sayendetsapo mawilo a ngolo yopunthira mbewu.
Mʼmalomwake, chitowe chakuda amachipuntha ndi ndodo,Ndipo chitowe chamtundu wina amachipuntha ndi kamtengo.
28 Kodi munthu akamapuntha tirigu, amamuphwanya mpaka kukhala ufa?
Ayi, samangokhalira kupuntha tiriguyo mosalekeza.+Ndipo akamayendetsa mawilo a ngolo yake pa tirigu ndi mahatchi ake,Saphwanya tiriguyo.+
29 Izinso zachokera kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,Amene zolinga zake ndi zabwino kwambiri,Ndipo zonse zimene amachita zimayenda bwino kwambiri.*+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “chodzikuza; chonyada.”
^ Zikuoneka kuti akunena mzinda wa Samariya, womwe ndi likulu la dzikoli.
^ Kapena kuti, “zodzikuza; zonyada.”
^ Kapena kuti, “Chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mulomo wachibwibwi.”
^ Kapena kuti, “Chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera.”
^ Mabaibulo ena amati, “taona masomphenya limodzi.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Chimenechi ndi chipangizo chimene amachigwiritsa ntchito pofuna kuonetsetsa kuti pamalo pakhale pa fulati.
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu adzachita mantha kwambiri.”
^ Kapena kuti, “dziko lonse lapansi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “komanso sipeloti.” Sipeloti ndi mtundu wa tirigu koma wosakoma ngati tirigu weniweni.
^ Kapena kuti, “amalanga; amakwapula.”
^ Kapena kuti, “Amene nzeru zake nʼzazikulu.”