Yesaya 33:1-24

  • Chiweruzo komanso chiyembekezo kwa anthu olungama (1-24)

    • Yehova ndi Woweruza, Wotipatsa Malamulo komanso Mfumu (22)

    • Palibe amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala” (24)

33  Tsoka kwa iwe amene umawononga ena koma iwe sunawonongedwe,+Iwe amene umachitira ena zachinyengo pamene iwe sunachitiridwe zachinyengo. Ukadzangomaliza kuwononga ena, iwenso udzawonongedwa.+ Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwenso udzachitiridwa zachinyengo.  2  Inu Yehova, tikomereni mtima.+ Chiyembekezo chathu chili pa inu. Tilimbitseni ndi dzanja lanu+ mʼmawa uliwonse.Mukhale chipulumutso chathu pa nthawi yamavuto.+  3  Mitundu ya anthu yathawa itamva phokoso lalikulu. Inu mukanyamuka, mitundu ya anthu imamwazikana.+  4  Mofanana ndi dzombe lanjala limene limawononga chilichonse, zinthu zimene inu munalanda anthu ena zidzalandidwaAnthu adzathamanga ngati chigulu cha dzombe kudzazitenga.  5  Yehova adzakwezedwa,Chifukwa amakhala pamalo apamwamba. Iye adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo.  6  Mʼmasiku anu, iye adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.Chimene amaona kuti ndi chamtengo wapataliNdi chipulumutso chake chachikulu,+ nzeru, kudziwa zinthu komanso kuopa Yehova.+  7  Taonani! Anthu awo otchuka akulira mofuula mʼmisewu.Amithenga amtendere akulira mopwetekedwa mtima.  8  Mʼmisewu ikuluikulu mulibe aliyense.Palibe munthu aliyense amene akuyenda mʼnjira. Iye* waphwanya pangano,Wakana mizindaNdipo sakusamala za munthu aliyense.+  9  Dzikolo likulira* ndipo lafota. Lebanoni wachita manyazi+ ndipo wawola. Sharoni wakhala ngati chipululuNdipo Basana ndi Karimeli akuyoyola masamba awo.+ 10  Yehova wanena kuti: “Tsopano ndinyamuka,Tsopano ndidzikweza.+Tsopano ndidziika pamwamba. 11  Munali ndi pakati pa udzu wouma ndipo mwabereka mapesi. Mzimu wanu udzakupserezani ngati moto.+ 12  Mitundu ya anthu idzakhala ngati zinthu zimene zimatsalira laimu akawotchedwa. Iwo adzayaka ndi moto ngati minga zimene zasadzidwa.+ 13  Inu amene muli kutali, imvani zimene ndikufuna kuchita. Ndipo inu amene muli pafupi, vomerezani kuti ndine wamphamvu. 14  Anthu ochimwa mu Ziyoni akuchita mantha.+Anthu ampatuko akunjenjemera kwambiri. Akufunsa kuti: ‘Ndi ndani wa ife amene angakhale pamene pali moto wowononga?+ Ndi ndani wa ife amene angakhale pafupi ndi moto umene sungazimitsike?’ 15  Ndi amene amayenda mʼchilungamo nthawi zonse,+Amene amalankhula zoona,+Amene amakana kupeza phindu pochita zinthu mosaona mtima komanso mwachinyengo,Amene manja ake amakana chiphuphu, mʼmalo mochilandira,+Amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi,Ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zinthu zoipa. 16  Iye adzakhala pamalo okwera.Malo ake othawirako otetezeka* adzakhala mʼmatanthwe movuta kufikamo.Iye adzapatsidwa chakudyaNdipo madzi ake sadzatha.”+ 17  Maso ako adzaona ulemerero wa mfumu.Adzaona dziko lakutali. 18  Mumtima mwako udzaganizira mozama za chinthu choopsa kuti: “Kodi mlembi ali kuti? Kodi ali kuti amene ankapereka msonkho uja?+ Kodi amene ankawerenga nsanja uja ali kuti?” 19  Anthu achipongwe simudzawaonanso,Anthu amene chilankhulo chawo nʼchovuta kumva,*Anthu achibwibwi amene simungamvetse zimene akulankhula.+ 20  Taonani Ziyoni, mzinda umene timachitiramo zikondwerero zathu.+ Maso anu adzaona kuti Yerusalemu ndi malo okhalamo abata,Tenti imene sidzachotsedwa.+ Zikhomo zake sizidzazulidwaNdipo zingwe zake sizidzadulidwa. 21  Koma kumeneko, Yehova WolemekezekaAdzakhala malo a mitsinje ndi a ngalande zikuluzikulu kwa ife.Malo amene sitima zankhondo sizidzapitakoKomanso amene sitima zikuluzikulu sizidzadutsako. 22  Chifukwa Yehova ndi Woweruza wathu,+Yehova ndi Wotipatsa Malamulo,+Yehova ndi Mfumu yathu.+Iye ndi amene adzatipulumutse.+ 23  Zingwe zanu zidzakhala zosamanga.Sizidzalimbitsa mtengo wautali wapasitima kapena kutambasula chinsalu chake. Pa nthawi imeneyo adzagawana zinthu zambirimbiri zimene analanda adani awo.Ngakhale anthu olumala adzatenga katundu wambiri amene alanda adani awo.+ 24  Ndipo palibe munthu wokhala mʼdzikolo amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala.”+ Anthu okhala mʼdzikolo adzakhululukidwa machimo awo.+

Mawu a M'munsi

Apa akunena mdani.
Mabaibulo ena amati, “lauma.”
Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼchozama.”