Yesaya 35:1-10

  • Paradaiso adzabwezeretsedwa (1-7)

    • Amene ali ndi vuto losaona adzaona, amene ali ndi vuto losamva adzamva (5)

  • Msewu Wopatulika wa anthu owomboledwa (8-10)

35  Chipululu ndi dziko louma zidzasangalala,+Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa ambiri.*+  2  Deralo lidzachitadi maluwa.+Lidzasangalala ndipo lidzafuula chifukwa cha chisangalalo. Lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni,+Kukongola kwa Karimeli+ ndiponso kwa Sharoni.+ Anthu adzaona ulemerero wa Yehova ndi kukongola kwa Mulungu wathu.  3  Limbitsani manja ofookaKomanso mawondo amene akugwedera.+  4  Amene ali ndi nkhawa mumtima mwawo muwauze kuti: “Limbani mtima. Musachite mantha. Chifukwa Mulungu wanu adzabwera nʼkudzabwezera adani anu.Mulungu adzabwera kudzapereka chilango.+ Iye adzabwera ndipo adzakupulumutsani.”+  5  Pa nthawi imeneyo, maso a anthu amene ali ndi vuto losaona adzatsegulidwa,+Ndipo makutu a anthu amene ali ndi vuto losamva adzayamba kumva.+  6  Pa nthawi imeneyo, munthu wolumala adzadumpha ngati mmene imachitira mbawala,+Ndipo lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mosangalala.+ Mʼchipululu mudzatumphuka madzi,Ndipo mʼdera lachipululu mudzayenda mitsinje.  7  Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi,Ndipo malo aludzu adzakhala ndi akasupe amadzi.+ Mʼmalo amene mimbulu inkakhala,+Mudzakhala udzu wobiriwira, bango ndi gumbwa.*  8  Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+Inde msewu umene udzatchedwe Msewu Wopatulika. Munthu wodetsedwa sadzayenda mumsewu umenewo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera.Palibe munthu wopusa amene adzayende mumsewu umenewo.  9  Mmenemo simudzakhala mkangoNdipo nyama zolusa zakutchire sizidzafikamo. Nyama zotere sizidzapezekamo.+Anthu okhawo amene anagulidwanso ndi amene adzayende mumsewuwo.+ 10  Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera+ ndipo adzafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Chisangalalo chosatha chidzakhala ngati chisoti chachifumu kumutu kwawo.+ Adzakhala okondwa ndi osangalalaNdipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “lidzachita maluwa ngati safironi.”