Yesaya 38:1-22
38 Mʼmasiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pangʼono kufa.+ Ndiyeno mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anapita kukamuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita, chifukwa iweyo ufa ndithu, suchira.’”+
2 Hezekiya atamva zimenezi, anatembenukira kukhoma nʼkuyamba kupemphera kwa Yehova kuti:
3 “Yehova ndikukupemphani kuti chonde, mukumbukire+ kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse+ komanso ndachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.
4 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yesaya kuti:
5 “Bwerera kwa Hezekiya+ ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndipo ndaona misozi yako.+ Tsopano ndiwonjezera zaka 15 pa moyo wako,*+
6 ndipo ndidzapulumutsa iweyo ndi mzindawu mʼmanja mwa mfumu ya Asuri komanso ndidzateteza mzinda uno.+
7 Chizindikiro chochokera kwa Yehova chosonyeza kuti Yehova adzakwaniritsadi mawu ake,+ ndi ichi:
8 Ndichititsa kuti mthunzi wa dzuwa umene wadutsa kale pamasitepe* a Ahazi, ubwerere mʼmbuyo masitepe 10.”’”+ Choncho dzuwa linabwerera mʼmbuyo masitepe 10 pamasitepe amene linali litadutsa kale.
9 Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala nʼkuchira, analemba zotsatirazi.
10 Ine ndinati: “Pakatikati pa moyo wangaNdidzalowa pamageti a Manda.*
Zaka zotsala za moyo wanga zidzachotsedwa.”
11 Ndinanena kuti: “Sindidzamuona Ya,* Ya sindidzamuonanso mʼdziko la amoyo.+
Anthu sindidzawaonansoNdikadzakhala ndi anthu okhala kudziko limene kulibe moyo.
12 Malo anga okhala azulidwa ndi kuchotsedwa kwa ine+Ngati tenti ya abusa.
Ndakulunga moyo wanga ngati munthu wowomba nsalu.Mwadula moyo wanga ngati ulusi wa nsalu.
Kuyambira mʼmawa mpaka usiku mukuchititsa kuti ndithe pangʼonopangʼono.+
13 Ndadzitonthoza mpaka mʼmawa.
Mofanana ndi mkango, iye akungokhalira kuphwanya mafupa anga onse.Kuyambira mʼmawa mpaka usiku mukuchititsa kuti ndithe pangʼonopangʼono.+
14 Ndikungokhalira kulira ngati namzeze kapena kamwana ka mbalame.+Ndikungokhalira kubuula ngati njiwa.+
Ndatopa ndi kudikirira thandizo kuchokera kumwamba.+ Choncho ndinati:
‘Inu Yehova ine ndapanikizika kwambiri.Chonde ndithandizeni.’+
15 Kodi ndinene kuti chiyani?
Iye walankhula ndi ine ndipo wachitapo kanthu.
Ndidzayenda modzichepetsa zaka zonse za moyo wangaChifukwa cha kupweteka kwa mtima wanga.*
16 ‘Inu Yehova, munthu aliyense amakhala ndi moyo chifukwa cha zinthu zimenezi,*Ndipo mʼzinthu zimenezi, mzimu wanga umapezamo moyo.
Inu mudzabwezeretsa thanzi langa nʼkundithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.+
17 Mʼmalo mopeza mtendere ndinali ndi chisoni chachikulu.Koma chifukwa chakuti mumandikonda kwambiri,Munanditeteza kuti ndisapite kudzenje lachiwonongeko.+
Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.*+
18 Chifukwa Manda* sangakupatseni ulemerero,+Imfa singakutamandeni.+
Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kuti muwasonyeze kukhulupirika kwanu.+
19 Munthu wamoyo, amene akupuma, ndi amene angakutamandeni,Ngati mmene ineyo ndikuchitira lero.
Bambo akhoza kuphunzitsa ana ake za kukhulupirika kwanu.+
20 Inu Yehova, ndipulumutseni,Ndipo ine ndi anthu ena tidzaimba nyimbo zanga ndi zoimbira za zingwe+Kunyumba ya Yehova masiku onse a moyo wathu.’”+
21 Kenako Yesaya anati: “Bweretsani keke ya nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndipo muziike pachotupa chimene ali nacho kuti achire.”+
22 Hezekiya anali atafunsa kuti: “Kodi chizindikiro chakuti ndidzapitadi kunyumba ya Yehova nʼchiyani?”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ako.”
^ Nʼkutheka kuti masitepe amenewa ankawagwiritsa ntchito ngati chipangizo chodziwira nthawi.
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
^ Kapena kuti, “kupwetekedwa moyo.”
^ Kutanthauza mawu a Mulungu ndi zochita zake.
^ Kapena kuti, “Mwachotsa machimo anga onse kuti musawaonenso.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.