Yesaya 43:1-28
43 Tsopano izi ndi zimene Yehova wanena,Mlengi wako iwe Yakobo, amene anakupanga iwe Isiraeli.+ Iye wanena kuti:
“Usachite mantha, chifukwa ine ndakuwombola.+
Ndakuitana pokutchula dzina lako.
Iwe ndiwe wanga.
2 Ukamadzadutsa pamadzi, ine ndidzakhala nawe.+Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakukokolola.+
Ukamadzayenda pamoto sudzapsaNdipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.
3 Chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wako,Woyera wa Isiraeli, Mpulumutsi wako.
Ndapereka Iguputo kuti akhale dipo* lako.Ndaperekanso Itiyopiya ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
4 Chifukwa ndinayamba kukuona kuti ndiwe wamtengo wapatali,+Unalemekezedwa ndipo ndimakukonda.+
Choncho ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iweKomanso mitundu ya anthu posinthanitsa ndi moyo wako.
5 Usachite mantha chifukwa ine ndili ndi iwe.+
Ndidzabweretsa mbadwa* zako kuchokera kumʼmawa,Ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumadzulo.+
6 Ndidzauza kumpoto kuti, ‘Abwezere kwawo!’+
Ndipo ndidzauza kumʼmwera kuti, ‘Usawakanize.
Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali komanso ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
7 Bweretsa aliyense amene amatchedwa ndi dzina langa,+Ndiponso amene ndinamulenga kuti ndipatsidwe ulemerero,Amene ndinamuumba komanso kumupanga.’+
8 Bweretsa anthu amene saona ngakhale kuti ali ndi maso,Ndiponso anthu osamva ngakhale kuti ali ndi makutu.+
9 Mitundu yonse isonkhane pamalo amodzi,Ndipo mitundu ya anthu isonkhanitsidwe pamodzi.+
Ndi ndani pakati pa milungu yawo amene ananena kuti zinthu zimenezi zidzachitika?
Kapena kodi angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+
Abweretse mboni zawo kuti tidziwe ngati akunena zoona,Kapena mbonizo zimvetsere nʼkunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+
10 “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova,“Inde, mtumiki wanga amene ndamusankha,+Kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira,*Komanso kuti mumvetse kuti ine sindimasintha.+
Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,Ndipo pambuyo panga palibenso wina.+
11 Ine ndine Yehova.+ Palibenso mpulumutsi wina kupatulapo ine.”+
12 “Ine ndi amene ndinanena zimene zidzachitike, amene ndinakupulumutsani komanso amene ndinachititsa kuti zimenezi zidziwike,Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo.+
Choncho inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+
13 “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+Ndipo palibe amene angathe kulanda chinthu chilichonse mʼdzanja langa.+
Ndikachita chinthu, ndi ndani amene angaletse?”+
14 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti:
“Chifukwa cha inu, ndidzatumiza asilikali ku Babulo ndipo adzagwetsa zotsekera mʼmageti,+Komanso Akasidi adzalira chifukwa chopanikizika, ali mʼsitima zawo zapamadzi.+
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu,+ Mlengi wa Isiraeli+ ndiponso Mfumu yanu.”+
16 Izi nʼzimene Yehova wanena,Yemwe amapanga msewu panyanjaKomanso njira ngakhale pamadzi osefukira,+
17 Amene amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi,+Gulu lankhondo pamodzi ndi asilikali amphamvu, wanena kuti:
“Iwo adzagona pansi ndipo sadzadzukanso.+
Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.”
18 “Musakumbukire zinthu zakale,Ndipo musamangoganizira zinthu zakumbuyo.
19 Taonani! Ndikupanga chinthu chatsopano.+Ngakhale panopa chikuonekera.
Kodi simukuchizindikira?
Ndidzapanga njira mʼchipululu,+Ndipo mitsinje idzadutsa mʼchipululumo.+
20 Zilombo zakutchire zidzandilemekeza,Komanso mimbulu ndi nthiwatiwa,Chifukwa ndimapereka madzi,Ndiponso mitsinje mʼchipululu,+Kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe,
21 Ndiponso kuti anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga,Alengeze za ulemerero wanga.+
22 Koma iwe Yakobo sunapemphe thandizo kwa ine+Chifukwa chakuti watopa nane, iwe Isiraeli.+
23 Iwe sunandibweretsere nkhosa kuti zikhale nsembe zako zopsereza zathunthuKapena kundilemekeza ndi nsembe zako.
Ine sindinakukakamize kuti undibweretsere mphatso,Ndipo sindinakutopetse pokulamula kuti undipatse lubani.*+
24 Iwe sunandigulire bango lonunkhira* ndi ndalama zako,Ndipo sunandikhutitse ndi mafuta a nsembe zako.+
Mʼmalomwake, wanditopetsa ndi machimo akoNdipo wandilemetsa ndi zolakwa zako.+
25 Ineyo ndi amene ndikufafaniza zolakwa zako*+ chifukwa cha dzina langa,+Ndipo machimo ako sindidzawakumbukira.+
26 Ndikumbutse, tiye tiimbane mlandu.Fotokoza mbali yako kuti usonyeze kuti ndiwe wosalakwa.
27 Kholo lanu loyambirira linachimwa,Ndipo anthu okulankhulirani* andipandukira.+
28 Choncho ndidzadetsa akalonga apamalo oyera,Ndidzachititsa kuti Yakobo awonongedweNdipo ndidzachititsa kuti Isiraeli amunenere mawu onyoza.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Kapena kuti, “kundidalira.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Chimenechi ndi chomera chonunkhira. Mtundu weniweni wa chomerachi sukudziwika.
^ Kapena kuti, “zochita zako zondipandukira.”
^ Nʼkutheka kuti akunena aphunzitsi a Chilamulo.