Yesaya 45:1-25
45 Izi ndi zimene Yehova akunena kwa wodzozedwa wake, kwa Koresi,+Amene wamugwira dzanja lake lamanja+Kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+Kuti alande zida zankhondo za mafumu,*Kuti amutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri,Kuti mageti adzakhale osatseka. Iye wamuuza kuti:
2 “Ine ndidzakhala patsogolo pako+Ndipo ndidzasalaza zitunda.
Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zakopa,*Ndipo ndidzadula zitsulo zotsekera zitseko.+
3 Ndidzakupatsa chuma chimene chili mumdimaNdiponso chuma chimene chabisidwa mʼmalo achinsinsi,+Kuti udziwe kuti ine ndine Yehova,Mulungu wa Isiraeli, amene ndikukuitana pokutchula dzina lako.+
4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo ndi Isiraeli wosankhidwa wanga,Ine ndikukuitana pokutchula dzina lako.
Ndikukupatsa dzina laulemu, ngakhale kuti sukundidziwa.
5 Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.
Palibenso Mulungu wina kupatulapo ine.+
Ndidzakupatsa mphamvu* ngakhale kuti sukundidziwa,
6 Kuti anthu adziweKuyambira kumene kumatulukira dzuwa mpaka kumene limalowera*Kuti palibenso wina kupatulapo ine.+
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+
7 Ndimapanga kuwala+ ndiponso ndimabweretsa mdima.+Ndimabweretsa mtendere+ komanso tsoka.+Ine Yehova ndimapanga zonsezi.
8 Inu kumwamba, chititsani kuti mvula igwe.+Chititsani kuti mitambo igwetse chilungamo ngati mvula.
Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso,Pa nthawi imodzimodziyo lichititse kuti chilungamo chiphuke.+
Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”
9 Tsoka kwa amene akulimbana* ndi amene anamupanga,Chifukwa iye ali ngati phaleLimene lili pakati pa mapale ena amene ali pansi.
Kodi dongo lingafunse woumba mbiya* kuti: “Kodi ukupanga chiyani?”+
Kapena kodi chinthu chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?*
10 Tsoka kwa amene akufunsa bambo kuti: “Kodi nʼchiyani mwaberekachi?”
Ndiponso wofunsa mkazi kuti: “Kodi nʼchiyani mukuberekachi?”*
11 Yehova, Woyera wa Isiraeli+ ndiponso amene anamuumba, wanena kuti:
“Kodi ukukaikira mawu anga okhudza zinthu zimene zikubweraNdipo ukundilamula zinthu zokhudza ana anga+ komanso ntchito ya manja anga?
12 Ineyo ndinapanga dziko lapansi+ ndipo ndinalenga munthu nʼkumuika padzikolo.+
Ndinatambasula kumwamba ndi manja angawa,+Ndipo zinthu zonse zimene zili kumwambako* ndimazipatsa malamulo.+
13 Ine ndapatsa munthu mphamvu kuti achitepo kanthu mwachilungamo,+Ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola.
Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+Komanso kumasula anthu anga amene ali ku ukapolo,+ popanda malipiro kapena chiphuphu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
14 Yehova wanena kuti:
“Phindu la ku Iguputo,* malonda* a ku Itiyopiya ndi Asabeya, anthu ataliatali,Adzabwera kwa iwe ndipo adzakhala ako.
Iwo adzayenda pambuyo pako atamangidwa mʼmaunyolo
Adzabwera nʼkudzakugwadira.+
Adzapemphera kwa iwe kuti, ‘Zoonadi Mulungu ali ndi iwe,+Ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina.’”
15 Ndithu, inu ndinu Mulungu amene amadzibisa,Inu Mulungu wa Isiraeli, Mpulumutsi.+
16 Anthu onse adzachititsidwa manyazi ndipo adzanyozeka.Anthu onse amene amapanga mafano adzachoka mwamanyazi.+
17 Koma Isiraeli adzapulumutsidwa ndi Yehova ndipo chipulumutso chake chidzakhala chosatha.+
Inu simudzachititsidwa manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.+
18 Chifukwa Yehova,Mlengi wakumwamba,+ Mulungu woona,Amene anaumba dziko lapansi, amene analipanga ndi kulikhazikitsa mwamphamvu,+Amene sanalilenge popanda cholinga,* koma analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti:
“Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.
19 Ine sindinalankhule mʼmalo obisika,+ mʼdziko lamdima.Sindinauze mbadwa* za Yakobo kuti,‘Muzindifunafuna pachabe.’
Ine ndine Yehova, amene ndimalankhula zolungama komanso kulengeza zinthu zimene ndi zolondola.+
20 Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere.
Mubwere pamodzi, inu anthu amene mwapulumuka ku mitundu ya anthu.+
Amene amanyamula zifaniziro zawo zogoba sadziwa chilichonseNdipo amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+
21 Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu.
Mukambirane mogwirizana.
Kodi ndi ndani ananeneratu zimenezi kalekaleNʼkuzilengeza kuyambira kalekale?
Kodi si ine, Yehova?
Palibenso Mulungu wina koma ine ndekha.Ine ndi Mulungu wolungama komanso Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+
22 Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumalekezero a dziko lapansi,Chifukwa ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+
23 Ndalumbira pa dzina langa.Mawu amene atuluka pakamwa panga ndi olondola,Ndipo adzakwaniritsidwa ndithu:+
Bondo lililonse lidzandigwadira,Ndipo lilime lililonse lidzalumbira kuti lidzakhala lokhulupirika kwa ine,+
24 Nʼkunena kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chechicheni komanso mphamvu.
Onse omukwiyira adzabwera kwa iye mwamanyazi.
25 Mbadwa* zonse za Isiraeli zidzaona kuti zinachita bwino kutumikira Yehova,+Ndipo zidzadzitama chifukwa cha zinthu zimene iye anazichitira.’”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimasule mʼchiuno mwa mafumu.”
^ Kapena kuti, “zamkuwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzakumanga mwamphamvu mʼchiuno mwako.”
^ Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa kukafika kumadzulo.”
^ Kapena kuti, “akutsutsana.”
^ Kapena kuti, “amene akuliumba.”
^ Mabaibulo ena amati, “Kapena kodi dongo linganene kuti: ‘Chimene waumbacho chilibe zogwiriraʼ?”
^ Kapena kuti, “Mukuvutikiranji ndi ululu wa pobereka.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “magulu awo onse ankhondo.”
^ Mabaibulo ena amati, “Antchito a ku Iguputo.”
^ Mabaibulo ena amati, “amalonda.”
^ Mabaibulo ena amati, “sanalipange kuti likhale lopanda kanthu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”