Yesaya 48:1-22
48 Imvani izi, inu a mʼnyumba ya Yakobo,Inu amene mumadzitchula dzina la Isiraeli+Ndiponso amene munatuluka kuchokera mʼmadzi a Yuda,*Inu amene mumalumbira pa dzina la Yehova+Ndiponso amene mumapemphera kwa Mulungu wa Isiraeli,Ngakhale kuti simuchita zimenezi kuchokera pansi pa mtima ndipo simuchita zoyenera.+
2 Chifukwa mumanena kuti ndinu anthu amumzinda woyera+Ndipo mumadalira Mulungu wa Isiraeli+Amene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
3 “Ndinakuuziranitu kalekale zinthu zimene zidzachitike.
Zinatuluka pakamwa panga,Ndipo ndinazichititsa kuti zidziwike.+
Mwadzidzidzi, ndinachita zimene ndinanena ndipo zinachitikadi.+
4 Chifukwa ndinadziwa kuti ndinu anthu ouma khosi,Kuti khosi lanu lili ngati mtsempha wachitsulo ndiponso kuti chipumi chanu chili ngati kopa,*+
5 Ine ndinakuuzani kalekale.
Zisanachitike nʼkomwe, ine ndinachititsa kuti muzimve,Kuti musanene kuti, ‘Fano langa ndi limene linachita zimenezi.Chifaniziro changa chosema komanso chifaniziro chachitsulo* nʼzimene zinalamula zimenezi.’
6 Inuyo mwamva komanso kuona zonsezo.
Kodi simudzauza ena zimenezi?+
Kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, ndikulengeza zinthu zatsopano kwa inu,+Zinsinsi zobisika zimene simunkazidziwa.
7 Zinthu zimenezi zikulengedwa panopa osati kalekale,Zinthu zimene simunazimvepo mʼmbuyomu.Choncho simunganene kuti, ‘Ifetu tinkazidziwa kale zimenezi.’
8 Ayi, inu simunamve+ kapena kudziwa zimenezi,Ndipo mʼmbuyomu makutu anu anali osatseguka,
Chifukwa ndikudziwa kuti inu ndi achinyengo,+Ndipo kuyambira pamene munabadwa mumatchedwa wochimwa.+
9 Koma ndidzabweza mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.+Chifukwa cha ulemerero wanga, ine ndidzadziletsaNdipo sindidzakuwonongani.+
10 Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+
Ndinakuyesani* mʼngʼanjo ya mavuto.+
11 Ndithu, ndidzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa,+Chifukwa sindingalole kuti dzina langa liipitsidwe.+
Sindipereka ulemerero wanga kwa wina aliyense.*
12 Ndimvere iwe Yakobo, iwe Isiraeli amene ndinakuitana.
Ine sindinasinthe.+ Ine ndine woyamba. Ndinenso womaliza.+
13 Dzanja langa linayala maziko a dziko lapansi,+Ndipo dzanja langa lamanja linatambasula kumwamba.+
Ndikaitana zinthu zimenezi, zimaimirira limodzi.
14 Sonkhanani pamodzi nonsenu ndipo mumvetsere.
Ndi ndani pakati pawo amene walengeza zinthu zimenezi?
Yehova wamukonda.+
Adzachitira Babulo zimene akufuna,+Ndipo dzanja lake lidzaukira Akasidi.+
15 Ineyo ndalankhula, komanso ndamuitana.+
Ndamubweretsa, ndipo zochita zake zidzamuyendera bwino.+
16 Bwerani pafupi ndi ine ndipo mumve izi.
Kuyambira pachiyambi, ine sindinalankhulirepo mʼmalo obisika.+
Kuyambira pamene zinachitika ine ndinalipo.”
Ndipo panopa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine komanso* mzimu wake.
17 Yehova, Wokuwombolani, Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti:
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu,Amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,*+Amene ndimakutsogolerani mʼnjira imene mukuyenera kuyenda.+
18 Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga!+
Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje+Ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a mʼnyanja.+
19 Ana anu adzachuluka* ngati mchengaNdipo mbadwa zanu zidzachulukanso ngati mchenga.+
Dzina lawo silidzachotsedwa kapena kuwonongedwa pamaso panga.”
20 Tulukani mʼBabulo!+
Thawani mʼmanja mwa Akasidi.
Lengezani zimenezi mofuula komanso mosangalala. Uzani anthu zimenezi.+
Zineneni kuti anthu azidziwe mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+
21 Iwo sanamve ludzu pamene iye ankawatsogolera kudutsa mʼchipululu.+
Iye anachititsa kuti madzi atuluke pathanthwe kuti iwo amwe.Anangʼamba thanthwe nʼkupangitsa kuti madzi atuluke.”+
22 Yehova wanena kuti, “Oipa alibe mtendere.”+
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “amene ndinu a fuko la Yuda.”
^ Kapena kuti, “mkuwa.”
^ Kapena kuti, “chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.”
^ Mabaibulo ena amati, “ndinakusankhani.”
^ Kapena kuti, “Sindigawana ulemerero wanga ndi wina aliyense.”
^ Kapena kuti, “limodzi ndi.”
^ Kapena kuti, “ndimakuphunzitsani chifukwa cha ubwino wanu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu zanu zidzachuluka.”