Yesaya 51:1-23
51 “Ndimvereni, inu anthu amene mukufunafuna chilungamo,Inu amene mukufunafuna Yehova.
Yangʼanani kuthanthwe limene munasemedwako,Ndi pamalo okumbapo miyala pamene munakumbidwa.
2 Yangʼanani kwa atate anu Abulahamu,Ndi kwa Sara+ amene anakuberekani.*
Chifukwa Abulahamu anali munthu mmodzi pamene ndinamuitana,+Koma ndinamudalitsa ndi kuchulukitsa mbadwa zake.+
3 Chifukwa Yehova adzatonthoza Ziyoni.+
Iye adzatonthoza malo ake onse amene anawonongedwa.+Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+Ndipo dera lake lachipululu lidzakhala ngati munda wa Yehova.+
Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera,Kuyamikira ndi kuimba nyimbo zosangalatsa.+
4 Inu anthu anga, ndimvereni.Iwe mtundu wanga,+ tchera khutu kwa ine.
Chifukwa kwa ine kudzachokera lamulo+Ndipo ndidzachititsa kuti chilungamo changa chikhazikike ngati kuwala ku mitundu ya anthu.+
5 Chilungamo changa chayandikira.+
Chipulumutso changa chikubwera kwa iwe+Ndipo manja anga adzaweruza mitundu ya anthu.+
Zilumba zidzayembekezera ine+Ndipo zidzadikira dzanja langa.*
6 Kwezani maso anu kumwamba,Ndipo yangʼanani padziko lapansi.
Kumwamba kudzabenthukabenthuka nʼkumwazika ngati utsi,Dziko lapansi lidzatha ngati chovala,Ndipo anthu amene akukhala mmenemo adzafa ngati ntchentche.
Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka kalekale+Ndipo chilungamo changa sichidzatha.*+
7 Ndimvereni, inu anthu amene mumadziwa chilungamo,Inu anthu amene chilamulo changa chili* mumtima mwanu.+
Musachite mantha ndi mawu otonza amene anthu akunenaNdipo musaope chifukwa cha mawu awo onyoza.
8 Chifukwa njenjete* idzawadya ngati chovalaNdipo kachilombo kodya zovala kadzawadya* ngati thonje.+
Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka kalekaleNdipo chipulumutso changa chidzafikira mibadwo yonse.”+
9 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu,Iwe dzanja la Yehova!+
Dzuka ngati masiku akale, ngati mʼmibadwo yakale.
Kodi si iwe amene unaphwanyaphwanya Rahabi,*+Amene unabaya chilombo chamʼnyanja?+
10 Kodi si iwe amene unaumitsa nyanja, amene unaumitsa madzi akuya kwambiri?+
Si iwe kodi amene unapangitsa kuti pansi pa nyanja pakhale njira yoti anthu owomboledwa awolokerepo?+
11 Anthu owomboledwa a Yehova adzabwerera.+
Adzabwera ku Ziyoni akufuula mosangalala,+Ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+
Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe,Ndipo chisoni komanso kulira zidzachoka.+
12 “Ineyo ndi amene ndikukutonthoza.+
Ndiye nʼchifukwa chiyani ukuopa munthu woti adzafa+Ndiponso mwana wa munthu amene adzanyale ngati udzu wobiriwira?
13 Nʼchifukwa chiyani ukuiwala Yehova amene anakupanga,+Amene anatambasula kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi?
Ndipo tsiku lonse unkangokhalira kuopa mkwiyo wa amene amakupondereza,Ngati kuti ali ndi mphamvu zoti akanatha kukuwononga.
Kodi tsopano mkwiyo wa amene ankakupondereza uja uli kuti?
14 Yemwe wawerama atamangidwa maunyolo amasulidwa posachedwapa.+Iye sadzafa nʼkutsikira kudzenje,Komanso sadzasowa chakudya.
15 Koma ine ndine Yehova Mulungu wako,Amene ndimavundula nyanja nʼkupangitsa kuti mafunde ake achite phokoso+Dzina langa ndine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
16 Ndidzaika mawu anga mʼkamwa mwako,Ndipo ndidzakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa,+Kuti ndikhazikitse kumwamba komanso kuyala maziko a dziko lapansi+Ndiponso kuti ndiuze Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’+
17 Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+Iwe amene wamwa zinthu zamʼkapu ya mkwiyo wa Yehova kuchokera mʼdzanja lake.
Iweyo wamwa zimene zili mʼchipanda,Wagugudiza kapu yochititsa kuti munthu aziyenda dzandidzandi.+
18 Pa ana onse amene iye anabereka, palibe ndi mmodzi yemwe woti amutsogolere,Ndipo pa ana onse amene iye analera, palibe ndi mmodzi yemwe amene wagwira dzanja lake.
19 Zinthu ziwiri izi zakugwera.
Ndi ndani amene akumvere chisoni?
Kuwonongedwa ndi kusakazidwa, njala ndi lupanga!+
Kodi ndi ndani amene akutonthoze?+
20 Ana ako akomoka.+
Agona pamphambano za misewu yonseNgati nkhosa zamʼtchire zimene zakodwa mu ukonde.
Iwo akhuta mkwiyo wa Yehova, akhuta kudzudzula kwa Mulungu wako.”
21 Choncho mvetsera izi,Iwe mkazi wovutika ndiponso woledzera, koma osati ndi vinyo.
22 Ambuye wako Yehova, Mulungu wako, amene amateteza anthu ake, wanena kuti:
“Taona! Ine ndidzachotsa mʼmanja mwako kapu yochititsa munthu kudzandira,+Chipanda kapena kuti kapu ya mkwiyo wanga.Sudzamwanso zinthu zamʼkapu imeneyi.+
23 Ndidzaika kapu imeneyi mʼmanja mwa amene akukuvutitsa,+Amene amakuuza kuti, ‘Werama kuti tiyende pamsana pako.’
Choncho unachititsa kuti msana wako ukhale ngati malo oti azipondapo,Ngati msewu woti azidutsamo.”
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amene anakuberekani ndi zowawa zapobereka.”
^ Kapena kuti, “mphamvu zanga.”
^ Kapena kuti, “sichidzaphwanyika.”
^ Kapena kuti, “malangizo anga ali.”
^ Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
^ Mabaibulo ena amati, “mbozi zodya zovala zidzawadya.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.