Yesaya 55:1-13

  • Kuitanidwa kuti adzadye ndi kumwa kwaulere (1-5)

  • Funafunani Yehova komanso mawu ake omwe ndi odalirika (6-13)

    • Njira za Mulungu nʼzapamwamba kuposa za anthu (8, 9)

    • Mawu a Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake (10, 11)

55  Inu nonse amene mukumva ludzu,+ bwerani mudzamwe madzi.+ Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye. Inde bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka+ popanda ndalama ndiponso popanda mtengo.+  2  Nʼchifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya,Ndipo nʼchifukwa chiyani mukuwononga ndalama* zimene mwapeza polipirira zinthu zimene nʼzosakhutitsa? Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino,+Ndipo mudzasangalala kwambiri ndi zakudya zabwino.*+  3  Tcherani khutu lanu ndipo mubwere kwa ine.+ Mverani ndipo mudzapitiriza kukhala ndi moyo,Ndithu ine ndidzachita nanu pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale+Lokhudza chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.+  4  Taonani! Ine ndinamuchititsa kuti akhale mboni+ ku mitundu ya anthu,Ndiponso kuti akhale mtsogoleri+ ndi wolamulira+ wa mitundu ya anthu.  5  Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,Ndipo anthu a mtundu umene sukukudziwa adzathamangira kwa iweChifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ Woyera wa Isiraeli,Komanso chifukwa chakuti adzakupatsa ulemerero.+  6  Funafunani Yehova pa nthawi imene akupezeka.+ Muitaneni adakali pafupi.+  7  Munthu woipa asiye njira yake+Ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.+  8  “Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu,+Ndipo njira zanu ndi zosiyana ndi njira zanga,” akutero Yehova.  9  “Chifukwa mofanana ndi kumwamba kumene kuli pamwamba kuposa dziko lapansi,Njira zanganso nʼzapamwamba kuposa njira zanuNdipo maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.+ 10  Mofanana ndi mvula komanso sinowo* zimene zimagwa kuchokera kumwambaNdipo sizibwerera kumeneko mpaka zitanyowetsa kwambiri nthaka nʼkuchititsa kuti mbewu zimere ndi kubereka zipatso,Nʼkupereka mbewu kuti anthu adzale komanso chakudya kuti adye, 11  Ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+Koma adzachitadi chilichonse chimene ine ndikufuna,+Ndipo zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi. 12  Chifukwa mudzapita mukusangalala,+Ndipo adzakubweretsani kwanu mwamtendere.+ Mukadzafika, mapiri ndi zitunda zidzafuula mosangalala,+Ndipo mitengo yonse yakutchire idzawomba mʼmanja.+ 13  Mʼmalo mwa chitsamba chaminga padzamera mtengo wa junipa.*+Mʼmalo mwa chomera choyabwa padzamera mtengo wa mchisu. Zinthu zimenezi zidzachititsa kuti Yehova atchuke,*+Ndipo zidzakhala chizindikiro chamuyaya chimene sichidzawonongeka.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndalama zimene mumazipeza movutikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zamafuta.”
Kapena kuti, “chipale chofewa.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Kapena kuti, “zidzamupangira dzina.”