Yesaya 61:1-11
61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+Chifukwa Yehova anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+
Anandituma kuti ndikamange mabala a anthu osweka mtima,Kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,Komanso kuti maso a akaidi adzatsegulidwa.+
2 Wandituma kuti ndilengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,*Ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu,+Komanso kuti nditonthoze anthu onse amene akulira,+
3 Kuti ndisamalire anthu onse amene akulirira Ziyoni,Kuti ndiwapatse nsalu yovala kumutu mʼmalo mwa phulusa,Kuti ndiwapatse mafuta kuti azisangalala mʼmalo molira,Kuti ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda mʼmalo mokhala otaya mtima.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ikuluikulu ya chilungamo,Yodzalidwa ndi Yehova kuti iyeyo alemekezedwe.*+
4 Iwo adzamanganso malo amene akhala bwinja kwa nthawi yaitali.Adzamanga malo amene anasakazidwa kalekale,+Adzakonzanso mizinda imene inawonongedwa,+Malo amene akhala ali osakazidwa kumibadwomibadwo.+
5 “Alendo adzabwera nʼkumaweta ziweto zanu,Ndipo anthu ochokera kwina+ adzakhala olima minda yanu ndi osamalira minda yanu ya mpesa.+
6 Inuyo mudzatchedwa ansembe a Yehova.+Anthu adzakutchulani kuti atumiki a Mulungu wathu.
Mudzadya zinthu zochokera kumitundu ya anthu+Ndiponso mudzadzitamandira chifukwa cha ulemerero umene* mudzapeze kuchokera kwa iwo.
7 Mʼmalo mwa manyazi, mudzalandira madalitso ochuluka kuwirikiza kawiri,Ndipo mʼmalo mochita manyazi, mudzafuula mosangalala chifukwa cha gawo lanu.
Inde, mudzalandira madalitso owirikiza kawiri mʼdziko lanu,+
Ndipo mudzasangalala mpaka kalekale.+
8 Chifukwa ine Yehova ndimakonda chilungamo.+Ndimadana ndi zauchifwamba komanso zinthu zopanda chilungamo.+
Anthu anga ndidzawapatsa malipiro awo mokhulupirika,Ndipo ndidzachita nawo pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale.+
9 Ana awo* adzadziwika pakati pa mitundu ya anthu,+Ndipo mbadwa zawo zidzadziwika pakati pa anthu osiyanasiyana.
Anthu onse owaona adzawazindikira,Kuti ndi ana amene* Yehova anawadalitsa.”+
10 Ndidzasangalala kwambiri mwa Yehova.
Ndidzasangalala mwa Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.+
Chifukwa iye wandiveka zovala zachipulumutso.+Wandiveka mkanjo wa chilungamo,*Ngati mkwati amene wavala nduwira yofanana ndi ya wansembe,+Ndiponso ngati mkwatibwi amene wavala zinthu zake zodzikongoletsera.
11 Chifukwa mofanana ndi dziko lapansi limene limatulutsa zomera zake,Ndiponso mofanana ndi munda umene umameretsa zinthu zimene zadzalidwa mmenemo,Nayenso Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,Adzachititsa kuti chilungamo+ komanso mawu otamanda zimere+ pamaso pa mitundu yonse.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “chofunira anthu zabwino.”
^ Kapena kuti, “aoneke kukongola.”
^ Kapena kuti, “cha chuma chimene.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zimene.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu zawo.”
^ Kapena kuti, “malaya odula manja a chilungamo.”