Yesaya 9:1-21

  • Anthu a ku Galileya anaona kuwala kwakukulu (1-7)

    • Kubadwa kwa “Kalonga Wamtendere” (6, 7)

  • Dzanja la Mulungu lidzaukira Isiraeli (8-21)

9  Komabe mdima wake sudzakhala ngati wa pa nthawi imene dzikolo linali mʼmavuto, ngati kale pamene anthu ankanyoza dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali.+ Koma pakadzapita nthawi, Mulungu adzachititsa kuti anthu alemekeze dzikolo, dera limene kuli njira yamʼmphepete mwa nyanja, mʼchigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina.  2  Anthu amene ankayenda mumdimaAona kuwala kwakukulu. Anthu amene ankakhala mʼdziko lamdima wandiweyani,Kuwala kwawawalira.+  3  Mwapangitsa kuti mtundu ukhale waukulu.Mwaupangitsa kuti usangalale kwambiri. Iwo akusangalala pamaso panuNgati mmene anthu amasangalalira pa nthawi yokolola,Ngati anthu amene amasangalala akamagawana katundu amene alanda.  4  Chifukwa mwathyolathyola goli la katundu wawo,Ndodo yomwe inali pamapewa awo, ndodo ya amene ankawagwiritsa ntchito,Ngati pa tsiku limene Amidiyani anagonjetsedwa.+  5  Nsapato iliyonse imene imagwedeza dziko lapansi munthu akamayendaNdi chovala chilichonse choviikidwa mʼmagaziZidzakhala zokolezera moto.  6  Chifukwa kwa ife kwabadwa mwana,+Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,Ndipo ulamuliro* udzakhala paphewa pake.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wamuyaya, Kalonga Wamtendere.  7  Ulamuliro* wake udzafika kutaliNdipo mtendere sudzatha,+Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wakeKuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimbaPogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+Kuyambira panopa mpaka kalekale. Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.  8  Yehova anatumiza mawu ochenjeza Yakobo,Ndipo mawuwo anafikira Isiraeli.+  9  Anthu onse adzawadziwa,Efuraimu ndi anthu okhala ku Samariya,Amene chifukwa cha kudzikweza kwawo ndiponso mwano wamumtima mwawo amanena kuti: 10  “Nyumba zanjerwa zagwa,Koma ife timanga zina zamiyala yosema.+ Mitengo ya mkuyu yadulidwa,Koma mʼmalo mwake ife tipezerapo mitengo ya mkungudza.” 11  Yehova adzakweza adani a Rezini kuti alimbane nayeNdipo adzachititsa adani a Isiraeli kuti amuukire, 12  Siriya adzachokera kumʼmawa ndipo Afilisiti adzachokera kumadzulo,*+Iwo adzadya Isiraeli ndi pakamwa potsegula.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+ 13  Chifukwa anthuwo sanabwerere kwa Mulungu amene akuwamenya,Ndipo sanafunefune Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+ 14  Choncho pa tsiku limodzi, Yehova adzadula IsiraeliMutu ndi mchira komanso mphukira ndi udzu wautali.*+ 15  Munthu wachikulire komanso wolemekezeka kwambiri ndi amene ali mutu,Ndipo mneneri wopereka malangizo abodza ndi amene ali mchira.+ 16  Amene akutsogolera anthuwa ndi amene akuwasocheretsa,Ndipo amene akutsogoleredwawo asokonezeka. 17  Nʼchifukwa chake Yehova sadzasangalala ndi anyamata awo,Ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye ndi akazi awo amasiye,Chifukwa onsewo ndi ampatuko komanso ochita zoipa+Ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru. Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+ 18  Chifukwa kuipa kwayaka ngati moto,Ndipo kukupsereza zitsamba zaminga ndi udzu. Kuipako kudzayatsa zitsamba zowirira zamʼnkhalango,Ndipo utsi wa mitengoyo udzakwera mʼmwamba kuti tolo! 19  Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova wa magulu ankhondo akumwambaDzikolo lawotchedwa ndi moto,Ndipo anthuwo adzakhala ngati nkhuni zokolezera motowo. Palibe amene adzapulumutse ngakhale mʼbale wake. 20  Munthu adzacheka zimene zili kumbali yakumanjaKoma adzakhalabe ndi njala.Ndipo munthu adzadya zimene zili kumanzere kwakeKoma sadzakhuta. Aliyense adzadya mnofu wa dzanja lake, 21  Manase adzadya Efuraimu,Ndipo Efuraimu adzadya Manase. Awiriwa adzaukira Yuda limodzi.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “boma; ulamuliro wa kalonga.”
Kapena kuti, “Boma; Ulamuliro wa kalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzachokera kumbuyo.”
Mabaibulo ena amati, “nthambi ya kanjedza ndi bango.”